Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Nsanja ya Olonda (Yophunzira)  |  April 2017

“Uzikwaniritsa Zinthu Zimene Walonjeza”

“Uzikwaniritsa Zinthu Zimene Walonjeza”

“Uzikwaniritsa malonjezo ako kwa Yehova.”​—MAT. 5:33.

NYIMBO: 63, 59

1. (a) Kodi Yefita ndi Hana anachita chiyani? (Onani zithunzi zoyambirira.) (b) Kodi tikambirana mafunso ati munkhaniyi?

YEFITA anali mtsogoleri wamphamvu komanso msilikali wolimba mtima. Hana ankagonjera mwamuna wake ndiponso ankasamalira bwino banja lake. Anthu awiri onsewa ankalambira Yehova ndipo anachita zinthu zina zofanana. Onse analonjeza Yehova zinazake ndipo anazikwaniritsa. Masiku ano, anthu amene amalonjeza zinazake kwa Yehova akhoza kuphunzira zambiri kwa anthu awiriwa. Komano tingafunse kuti: N’chifukwa chiyani tinganene kuti kulonjeza zinthu kwa Mulungu ndi nkhani yaikulu? Nanga tingaphunzire chiyani kwa Yefita ndi Hana?

2, 3. (a) Kodi munthu angalonjeze kwa Mulungu zinthu ziti? (b) Kodi Malemba amati chiyani pa nkhani ya zinthu zimene talonjeza kwa Mulungu?

2 Baibulo limasonyeza kuti pali zinthu zosiyanasiyana zimene munthu angalonjeze kwa Mulungu. Angalonjeze kuti achita zinazake, apereka mphatso inayake, achita utumiki winawake kapena azipewa zinthu zinazake. Munthu amalonjeza zinthu ngati zimenezi mwa kufuna kwake osati mokakamizidwa. Koma malonjezo oterewa amakhala opatulika chifukwa chakuti munthuyo amakhala kuti walumbira pamaso pa Mulungu kuti azichita kapena sazichita zinazake. (Gen. 14:22, 23; Aheb. 6:16, 17) Kodi Malemba amasonyeza bwanji kuti kulonjeza zinthu kwa Mulungu ndi nkhani yaikulu?

3 Mu Chilamulo cha Mose munali lamulo lakuti: “Munthu  akalonjeza kwa Yehova, kapena akachita lumbiro lodzimana asalephere kukwaniritsa mawu ake. Achite malinga ndi mawu onse otuluka pakamwa pake.” (Num. 30:2) Patapita nthawi, Solomo analemba kuti: “Ukalonjeza kwa Mulungu usamachedwe kukwaniritsa lonjezo lako, chifukwa palibe amene amasangalala ndi anthu opusa. Uzikwaniritsa zinthu zimene walonjeza.” (Mlal. 5:4) Nayenso Yesu anasonyeza kuti kulonjeza zinthu kwa Mulungu ndi nkhani yaikulu. Anati: “Munamva kuti anthu akale anauzidwa kuti, ‘Usamalumbire koma osachita, m’malomwake uzikwaniritsa malonjezo ako kwa Yehova.’”​—Mat. 5:33.

4. (a) N’chifukwa chiyani tinganene kuti kulonjeza zinthu kwa Mulungu ndi nkhani yaikulu? (b) Kodi tiphunzira chiyani pa zimene Yefita komanso Hana anachita?

4 Taona kuti kulonjeza zinthu kwa Mulungu ndi nkhani yaikulu. Tikutero chifukwa chakuti zimene tingachite pa nkhaniyi, zimakhudza ubwenzi wathu ndi Yehova. Davide analemba kuti: “Ndani angakwere m’phiri la Yehova? Ndipo ndani anganyamuke kukalowa m’malo ake opatulika? Aliyense . . . amene sanaone Moyo wanga [wa Yehova] ngati wopanda pake, kapena kulumbira mwachinyengo.” (Sal. 24:3, 4) Kodi Yefita komanso Hana analonjeza Yehova zinthu ziti? Nanga n’chifukwa chiyani tingati kukwaniritsa lonjezo lawo sikunali kophweka?

ANAKWANIRITSA ZIMENE ANALONJEZA KWA MULUNGU

5. Kodi Yefita analonjeza Yehova chiyani, nanga ndani anabwera kudzamuchingamira?

5 Yefita anakwaniritsa zimene analonjeza Yehova. Iye ankafunitsitsa kuti akapambane pa nkhondo yomenyana ndi ana a Amoni, omwe ankazunza anthu a Mulungu. (Ower. 10:7-9) Choncho analonjeza kuti: “Ngati mudzaperekadi ana a Amoni m’manja mwanga, ine ndidzapereka kwa Yehova aliyense amene adzatuluka m’nyumba yanga kudzandichingamira pamene ndikubwera mwamtendere kuchokera kwa ana a Amoni.” Yefita anapambanadi pa nkhondoyi ndipo mwana wake wamkazi ndi amene anapita kukamuchingamira. Mogwirizana ndi lonjezo lake, Yefita anayenera kupereka mwana wakeyu “kwa Yehova.” (Ower. 11:30-34) Koma kodi zimenezi zinakhudza bwanji mwanayo?

6. (a) N’chiyani chikusonyeza kuti sizinali zophweka kuti Yefita komanso mwana wake akwaniritse zimene Yefitayo analonjeza? (b) Kodi lemba la Deuteronomo 23:21, 23 ndi la Salimo 15:4 likutiphunzitsa chiyani pa nkhani ya zimene timalonjeza Mulungu?

6 Kuti akwaniritse lonjezo la bambo ake, mwana wa Yefita ankafunika kukatumikira panyumba ya Yehova moyo wake wonse. Kodi bambo ake sanaganize bwino polonjeza Yehova kuti aliyense wobwera kudzawachingamira adzamupereka? Ayi, n’kutheka kuti Yefita ankadziwa kuti mwina wobwera kudzamuchingamirayo akhoza kukhala mwana wake. Komabe sizinali zophweka kuti Yefita ndi mwana wake akwaniritse lonjezoli chifukwa onsewa anafunika kudzimana zinthu zina. N’chifukwa chake Yefita atangoona mwana wakeyo, “anayamba kung’amba zovala zake” ndipo anamva chisoni. Nayenso mwanayo anapita ‘kukalirira unamwali wake.’ N’chifukwa chiyani awiriwa anachita zimenezi? N’chifukwa choti Yefita anali ndi mwana mmodzi yekhayu. Ndipo izi zinasonyeza kuti tsopano mwanayu sadzakwatiwa n’kukhala ndi ana. Choncho panalibe wodzatenga dzina komanso cholowa cha banja la Yefita. Komabe Yefita sanalole kuti izi zimulepheretse kukwaniritsa lonjezo lake. Iye anati: “Ndatsegula pakamwa panga pamaso pa Yehova, ndipo sindingathe kubweza mawu anga.” Nayenso mwanayo anayankha kuti: “Ndichitireni mogwirizana ndi zimene zatuluka pakamwa panu.” (Ower. 11:35-39) Yefita ndi mwana wake anali anthu okhulupirika ndipo anakwaniritsa lonjezoli kwa Yehova ngakhale kuti sizinali zophweka.​—Werengani Deuteronomo 23:21, 23; Salimo 15:4.

7. (a) Kodi Hana analonjeza Yehova chiyani, nanga zotsatira zake zinali zotani? (b) Kodi Samueli ankayenera kudzakhala wotani mogwirizana ndi lonjezo la Hana? (Onani mawu a m’munsi.)

 7 Nayenso Hana anakwaniritsa zimene analonjeza kwa Yehova. Iye ananena lonjezo lake pamene anali wokhumudwa kwambiri chifukwa cha vuto lake la kusabereka komanso chipongwe chimene mkazi mnzake ankamuchitira. (1 Sam. 1:4-7, 10, 16) Iye anauza Yehova zakukhosi kwake komanso anamulonjeza kuti: “Inu Yehova wa makamu, mukaona nsautso yanga, ine kapolo wanu wamkazi, ndi kundikumbukira, ndiponso ngati simudzaiwala kapolo wanu wamkazi ndi kum’patsa mwana wamwamuna, ndidzam’pereka kwa Yehova masiku onse a moyo wake, ndipo lezala silidzadutsa m’mutu mwake.” * (1 Sam. 1:11) Yehova anayankha pemphero la Hanali ndipo anamupatsadi​ mwana wamwamuna. Hana ayenera kuti anasangalala kwambiri. Komabe iye sanaiwale lonjezo lake komanso sanaiwale kuti Yehova ndi amene anamuthandiza kuti abereke mwanayu. Moti mwanayu atangobadwa iye anati: “Ndinam’pempha kwa Yehova.”​—1 Sam. 1:20.

8. (a) N’chifukwa chiyani tingati sizinali zophweka kuti Hana akwaniritse lonjezo lake? (b) Kodi mawu a Davide a mu Salimo 61 akutikumbutsa chiyani za Hana?

8 N’kutheka kuti Samueli ali ndi zaka zitatu, ndipo atangosiya kuyamwa, Hana anakwaniritsa lonjezo lake kwa Mulungu. Iye sanayambe kupeza zifukwa zoti alephere kuchita zomwe analonjeza. Anatenga Samueli n’kupita naye ku Silo n’kukamupereka kwa Mkulu wa Ansembe dzina lake Eli. Iye anauza Eli kuti: ‘Ndinali kupemphera kuti Yehova andipatse mwana uyu. Ndipo ine ndikum’pereka kwa Yehova. Ndam’pereka kwa Yehova masiku onse a moyo wake.’ (1 Sam. 1:24-28) Kumeneko, “Samueli anapitiriza kukula, akukondedwa ndi Yehova.” (1 Sam. 2:21) Koma kodi zinali zophweka kuti Hana apereke mwana wake? Ayi. Iye ankam’konda kwambiri mwanayu. Koma tsopano sakanathanso kumacheza naye tsiku ndi tsiku. Analibenso mwayi woti azimunyamula, kusewera naye, kumusamalira komanso kuona zinthu zosangalatsa zimene mwana amachita akamakula. Komabe Hana sanayambe kuganiza kuti mwina analakwitsa pa zomwe analonjeza. Mtima wake unkakondwera mwa Yehova podziwa kuti wakwaniritsa lonjezo lake​.—1 Sam. 2:1, 2; werengani Salimo 61:1, 5, 8.

Kodi mukuyesetsa kukwaniritsa malonjezo anu kwa Yehova?

9. Kodi tsopano tikambirana mafunso ati?

9 Popeza tadziwa kuti kulonjeza zinthu kwa Mulungu ndi nkhani yaikulu, tsopano tiyeni tikambirane mafunso awa: Kodi Akhristufe timapanga malonjezo ati? Nanga n’chifukwa chiyani tiyenera kuyesetsa kuti tiwakwaniritse?

ZIMENE MUNALONJEZA PODZIPEREKA KWA MULUNGU

Zimene munalonjeza podzipereka kwa Mulungu (Onani ndime 10)

10. (a) Kodi lonjezo lofunika kwambiri kwa Mkhristu ndi liti? (b) Kodi munthu akapanga lonjezoli amayenera kuchita chiyani?

10 Lonjezo lofunika kwambiri kwa Mkhristu ndi lokhudza kudzipereka kwa Yehova. Tikutero chifukwa chakuti munthuyo amalonjeza Yehova m’pemphero kuti adzamutumikira kwa moyo wake wonse, zivute zitani. Malinga ndi zimene Yesu ananena, munthu amakhala kuti ‘wadzikana yekha’ ndipo walolera kuti akhala kapolo wa Mulungu n’kumaika zofuna za Mulunguyo patsogolo. (Mat. 16:24) Kungoyambira nthawi imeneyo amakhala kuti ndi ‘wa Yehova.’ (Aroma 14:8) Munthu aliyense akadzipereka kwa Yehova ayenera kudziwa kuti imeneyi ndi nkhani yaikulu. Ayenera kukhala ndi maganizo ofanana ndi amene wamasalimo ananena akuti: “Yehova ndidzamubwezera chiyani pa zabwino zonse zimene wandichitira? Ndidzakwaniritsa  malonjezo anga kwa Yehova, pamaso pa anthu ake onse.”​—Sal. 116:12, 14.

11. Fotokozani zimene zinachitika pa tsiku limene munabatizidwa.

11 Kodi inuyo munadzipereka kwa Yehova n’kubatizidwa? Ngati ndi choncho munachita bwino kwambiri. Kumbukirani kuti pa tsiku la ubatizo wanu anakufunsani pagulu ngati munadzipereka kwa Yehova. Kenako anakufunsani kuti: “Kodi mukuzindikira kuti kudzipereka kumene munachita, ndi kubatizidwa kwanu lero, zikupangitsani kukhala wa Mboni za Yehova, wogwirizana ndi gulu la Mulungu limene amalitsogolera ndi mzimu wake?” Kuyankha kwanu momveka bwino kuti inde kunasonyeza kuti munadziperekadi ndi mtima wonse ndipo munkayenera kubatizidwa n’kukhala mtumiki woikidwa ndi Yehova.

12. (a) Kodi tiyenera kudzifunsa mafunso ati? (b) Kodi Petulo anati tiyenera kukhala ndi makhalidwe ati?

12 Koma kubatizidwa ndi chiyambi chabe. Munthu akabatizidwa ayenera kuchita zinthu mogwirizana ndi zimene analonjeza kwa Mulungu. Choncho ndi bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi zinthu zakhala zikuyenda bwanji kuyambira pamene ndinabatizidwa? Kodi ndikutumikirabe  Yehova ndi mtima wonse? (Akol. 3:23) Kodi ndimapemphera, kuwerenga Mawu a Mulungu, kusonkhana komanso kulalikira nthawi zonse? Kapena kodi ndafooka pang’ono pa zinthu zimenezi? Paja mtumwi Petulo anati tiyenera “kuwonjezera pa chikhulupiriro chathu kudziwa zinthu, kudziletsa, kupirira ndiponso kudzipereka kwa Mulungu.”​(Werengani 2 Petulo 1:5-8.) Makhalidwe amenewa angatithandize kuti tizitumikirabe Mulungu mwakhama.

13. Kodi Mkhristu amene anadzipereka n’kubatizidwa ayenera kuzindikira mfundo iti?

13 Munthu akadzipereka kwa Mulungu, ndiye kuti wadzipereka basi ndipo n’zosatheka kusintha. Munthu sanganene kuti watopa ndi kutumikira Yehova kapena kuchita zimene Mkhristu amayenera kuchita ndipo akufuna kusintha kuti asamaonedwenso ngati Mkhristu wodzipereka ndiponso wobatizidwa. * Izi n’zosatheka chifukwa munthuyo anadzipereka kale kwa Yehova ndi mtima wonse. Ndipo akachita machimo aakulu, amayenera kuyankha kwa Yehova komanso kumpingo. (Aroma 14:12) Choncho ndi bwino kuti tiziyesetsa kuti ‘tisasiye chikondi chimene tinali nacho poyamba.’ Koma tizichita zinthu zimene zingapangitse Yesu kutiuza kuti: “Ndikudziwa ntchito zako, chikondi chako, chikhulupiriro chako, utumiki wako, ndi kupirira kwako. Ndikudziwanso kuti ntchito zako zapanopa n’zambiri kuposa zoyamba zija.” (Chiv. 2:4, 19) Tiyeni tiziyesetsa kukwaniritsa lonjezo lathu kuti tizisangalatsa Yehova.

ZIMENE MUNALONJEZA PA TSIKU LA UKWATI WANU

Zimene munalonjeza pa tsiku la ukwati wanu (Onani ndime 14)

14. Kodi lonjezo lina lofunika kwambiri ndi liti, ndipo n’chifukwa chiyani?

14 Lonjezo lina lofunika kwambiri ndi limene munthu amachita pa tsiku la ukwati wake. Tikutero chifukwa chakuti ukwati ndi wopatulika. Mwamuna ndi mkazi amalonjeza pamaso pa Mulungu komanso anthu. Mwachitsanzo, akhoza kulonjeza kuti adzakondana, kusamalirana komanso kulemekezana ‘pa nthawi yonse imene adzakhale ndi moyo padzikoli, mogwirizana ndi zimene Mulungu anakonza pa nkhani ya ukwati.’ Ena sananene mawuwa ndendende koma analonjezabe pamaso pa Mulungu kuti adzakhala limodzi mpaka kalekale. Zikatero amakhala mwamuna ndi mkazi wake ndipo ukwati wawo suyenera kutha. (Gen. 2:24; 1 Akor. 7:39) Malinga ndi mawu a Yesu, “chimene Mulungu wachimanga pamodzi, munthu asachilekanitse.” (Maliko 10:9) Choncho mwamuna, mkazi kapena munthu aliyense sayenera kuthetsa banja. Aliyense akamalowa m’banja ayenera kudziwa kuti kuthetsa banja si njira yothetsera mavuto.

15. N’chifukwa chiyani Akhristu ayenera kupewa maganizo a anthu a m’dzikoli pa nkhani ya banja?

15 N’zoona kuti banja lililonse limakumana ndi mavuto chifukwa choti okwatiranawo sakhala anthu angwiro. N’chifukwa chake Baibulo limanena kuti anthu amene amalowa m’banja “adzakhala ndi nsautso m’thupi mwawo.” (1 Akor. 7:28) N’zomvetsa chisoni kuti anthu ambiri m’dzikoli ali ndi maganizo olakwika pa nkhani ya banja. Amaona kuti ngati pali vuto linalake ndi bwino kungomusiya mnzawoyo. Koma Akhristu amapewa maganizo amenewa. Munthu amene amaphwanya lonjezo lake pa nkhani ya ukwati amakhala kuti wanamiza Mulungu ndipo Mulungu amadana ndi anthu abodza. (Lev. 19:12; Miy. 6:16-19) Mtumwi Paulo analemba kuti: “Kodi ndiwe womangika kwa mkazi? Leka kufunafuna njira yomasukira.” (1 Akor. 7:27) Iye ananena zimenezi chifukwa ankadziwa kuti Yehova amadana ndi anthu amene amathetsa banja popanda zifukwa za m’Malemba.​—Mal. 2:13-16.

16. Kodi Baibulo limati chiyani pa nkhani ya kuthetsa banja komanso kupatukana?

 16 Yesu ananena kuti banja likhoza kutha ngati wina wachita chigololo ndipo mnzakeyo wasankha kuti banjalo lithe. (Mat. 19:9; Aheb. 13:4) Nanga bwanji za kupatukana? M’Baibulo mulinso malangizo omveka bwino okhudza nkhani imeneyi. (Werengani 1 Akorinto 7:10, 11.) Baibulo silitchula chifukwa chimene chingapangitse kuti anthu apatukane. Komabe Akhristu ena amaona kuti akhoza kupatukana ngati akukumana ndi mavuto aakulu omwe akuika moyo wawo pa ngozi kapena akuwalepheretsa kulambira Mulungu. Izi zingachitike ngati mnzawoyo amawachitira nkhanza kwambiri kapena ngati ndi wampatuko. *

17. Kodi Akhristu angatani kuti banja lawo lisathe?

17 Ngati anthu ena apita kwa akulu kukafunsa malangizo pa nkhani ya mavuto a m’banja, akuluwo angachite bwino kuwafunsa ngati posachedwapa anaonera vidiyo yakuti, Chikondi Chenicheni kapena kuphunzira kabuku kakuti, Banja Lanu Likhoza Kukhala Losangalala. Tikutero chifukwa chakuti zinthu zimenezi zili ndi mfundo za m’Malemba zimene zingathandize kuti banja liziyenda bwino. Banja lina linanena kuti: “Kungoyambira nthawi imene tinaphunzira kabukuka, banja lathu ndi losangalala.” Mlongo wina amene wakhala m’banja zaka 22 ndipo banja lawo linangotsala pang’ono kutha anati: “Tonse ndife obatizidwa ndithu koma tinkasiyana maganizo pa zinthu zina. Vidiyoyi inatuluka pa nthawi yake. Panopa zinthu zikuyenda bwino.” Kodi inunso muli pa banja? Ngati ndi choncho muziyesetsa kutsatira mfundo za Yehova m’banja lanu. Mukamatero muzisangalala komanso mudzakwaniritsa zimene munalonjeza pa tsiku la ukwati wanu.

ZIMENE MUNALONJEZA POYAMBA UTUMIKI WA NTHAWI ZONSE WAPADERA

18, 19. (a) Kodi makolo ambiri amatani? (b) Kodi anthu amene akuchita utumiki wa nthawi zonse wapadera amakwaniritsa bwanji lonjezo loti azikhala moyo wosalira zambiri?

18 Zimene Yefita ndi Hana analonjeza zinachititsa kuti ana awo azikachita utumiki wa nthawi zonse panyumba ya Yehova. Izi zinathandiza kuti anawo akhale osangalala pa moyo wawo. Masiku anonso pali makolo amene amalimbikitsa ana awo kuti ayambe utumiki wa nthawi zonse wapadera. Ana oterewa ayenera kuyamikiridwa kwambiri.​—Ower. 11:40; Sal. 110:3.

Zimene munalonjeza poyamba utumiki wa nthawi zonse wapadera (Onani ndime 19)

19 Panopa pali abale ndi alongo okwana 67,000 amene akuchita utumiki wa nthawi zonse wapadera. Ena akutumikira pa Beteli, ena amagwira ntchito zomangamanga, ena ndi oyang’anira dera, ena ndi alangizi a Sukulu Zophunzitsa Baibulo, ena ndi apainiya apadera, ena ndi amishonale ndipo ena amatumikira m’Malo a Misonkhano kapena m’malo amene kumachitikira Masukulu Ophunzitsa Baibulo. Atumiki onsewa amalonjeza kuti azikhala moyo wosalira zambiri ndipo sangagwire ntchito yolembedwa pa nthawi imene akuchita utumikiwu. Anthuwa si apadera koma utumiki umene akuchita ndi womwe umakhala wapadera. Iwo amadziwa kuti pa nthawi yonse imene akuchita utumikiwu, ayenera kuchita zinthu mogwirizana ndi zimene analonjeza.

20. Kodi tiziona bwanji zinthu zimene tinalonjeza kwa Yehova, ndipo n’chifukwa chiyani?

20 Kodi ndi malonjezo ati amene takambirana m’nkhaniyi amene inuyo munapanga? Kodi ndi limodzi, awiri kapena onsewa? Nkhaniyi yatithandiza kudziwa kuti zimene munalonjezazo si nkhani yaing’ono. (Miy. 20:25) Pangakhale zotsatira zoipa ngati munthu walephera kukwaniritsa zimene analonjeza kwa Yehova. (Mlal. 5:6) Choncho tiyeni ‘tiziimba nyimbo zotamanda dzina la Yehova mpaka muyaya, uku tikukwaniritsa malonjezo athu tsiku ndi tsiku.’​—Sal. 61:8.

^ ndime 7 Zimene Hana analonjezazi zinkatanthauza kuti mwana wakeyo adzakhala Mnaziri kwa moyo wake wonse. Zinkatanthauzanso kuti mwanayo adzakhala wosiyana ndi ana ena, adzaperekedwa kwa Yehova ndipo azidzachita utumiki wopatulika.​—Num. 6:2, 5, 8.

^ ndime 13 Tikaganizira zimene akulu amachita potsimikizira kuti munthu akuyenerera kubatizidwa, tingati m’povuta kuti munthu abatizidwe ali wosayenera kubatizidwa.

^ ndime 16 Onani tsamba 219 mpaka 221 m’buku la ‘Mulungu Apitirize Kukukondani.’