Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Nsanja ya Olonda  |  Na. 6 2017

 NKHANI YA PACHIKUTO | KODI MPHATSO YAMTENGO WAPATALI KWAMBIRI NDI ITI?

“Ndinali Ndisanapatsidwepo Mphatso Yamtengo Wapatali Ngati Imeneyi”

“Ndinali Ndisanapatsidwepo Mphatso Yamtengo Wapatali Ngati Imeneyi”

Mawu amenewa ananena ndi mtsikana wina wazaka 13, atapatsidwa mphatso ya kagalu. Mayi wina wabizinezi ananena kuti ali kusekondale, bambo ake anamupatsa kompyuta. Mayiyu anati kompyutayo inali mphatso yamtengo wapatali kwambiri kwa iye chifukwa inamuthandiza kwabasi. Komanso bambo wina anati pa tsiku limene ankakumbukira kuti atha chaka ali m’banja, mkazi wake anamupatsa khadi limene anapanga pamanja. Bamboyu anaona kuti imeneyi inali mphatso yamtengo wapatali kwambiri.

Chaka chilichonse, anthu ambiri amayesetsa kuti apeze mphatso yabwino yoti adzapatse mnzawo kapena wachibale pa tsiku lapadera. Ndipo ambiri amalakalaka atapeza mphatso imene munthuyo adzasangalale nayo ngati mmene zinaliri ndi anthu omwe tawatchulawa. Kodi nanunso mumafuna mutalandira kapena kupereka mphatso yomwe ingakhale ya mtengo wapatali kwambiri?

Aliyense amafuna zimenezi chifukwa mphatso ya mtengo wapatali imachititsa kuti wolandirayo komanso woperekayo asangalale. Ndipotu Baibulo limati: “Kupatsa kumabweretsa chimwemwe chochuluka kuposa kulandira.” (Machitidwe 20:35) Koma munthu woperekayo amasangalala kwambiri zikakhala kuti amene wapatsidwa mphatsoyo waikonda ndipo akuiona kuti ndi yofunika kwambiri.

Ndiye kodi mungatani kuti inuyo komanso munthu amene mwamupatsa mphatso musangalale kwambiri? Nanga mungapeze bwanji mphatso yoti munthuyo akasangalale nayo komanso akaione kuti ndi yamtengo wapatali?