Palibe munthu amene ali ndi chithunzi cha Yesu. Komanso pamene Yesu anali padzikoli, palibe aliyense amene anagoba kapena kujambula chithunzi chosonyeza mmene ankaonekera. Komabe, kwa zaka zambiri anthu aluso akhala akujambula zithunzi zosiyanasiyana zoyerekezera mmene Yesu ankaonekera.

Komatu palibe aliyense wa anthuwa yemwe amadziwa mmene Yesu ankaonekera. Anthuwa akhala akujambula Yesu potengera chikhalidwe chawo, zimene amakhulupirira, komanso zimene anthu ofuna kugula zithunzizo akufuna. Koma zithunzi zimene amajambulazi zikhoza kuchititsa anthu kuti azikhala ndi maganizo olakwika okhudza Yesu komanso kuwalepheretsa kumvetsa zimene ankaphunzitsa.

Anthu ena amajambula Yesu akuoneka wofooka, wa tsitsi lalitali, ali ndi ndevu zochepa komanso akuoneka wodandaula. Zithunzi zina zimasonyeza Yesu akuoneka ngati mngelo, atazunguliridwa ndi kuwala kwaulemerero ndiponso akuoneka wapamwamba kwambiri kuposa anthu ena. Kodi zithunzi zoterezi zimasonyezadi mmene Yesu analili? Nanga tingadziwe bwanji mmene ankaonekera? Njira imodzi ndi kuona mavesi a m’Baibulo amene amafotokoza zina ndi zina zokhudza Yesu. Mavesi amenewa angatithandizenso kuti tikhale ndi maganizo oyenera okhudza mmene Yesu alili panopa.

“MUNANDIKONZERA THUPI”

Zikuoneka kuti Yesu ananena mawu amenewa m’pemphero pa nthawi imene ankabatizidwa. (Aheberi 10:5; Mateyu 3:13-17) Kodi thupi limene Yehova anamukonzeralo linkaoneka bwanji? Zaka pafupifupi 30 m’mbuyomo, mngelo Gabirieli anauza Mariya kuti: “Udzakhala ndi pakati ndipo udzabereka mwana wamwamuna, . . . Mwana wa Mulungu.” (Luka 1:31, 35) Izi zikusonyeza kuti Yesu anali munthu wangwiro, mofanana ndi mmene Adamu analili atangolengedwa kumene. (Luka 3:38; 1 Akorinto 15:45) Choncho Yesu ayenera kuti anali wooneka bwino ndipo n’kuthekanso kuti ankafananako ndi Mariya, yemwe anali mayi ake.

Mosiyana ndi Aroma, Yesu ankasunga ndevu monga mmene Ayuda ambiri ankachitira. Ayuda ankaona kuti kukhala ndi ndevu ndi chizindikiro choti munthuyo ndi wolemekezeka. Komabe ndevuzo zinkakhala zosamaliridwa bwino ndipo sizinkakhala zazitali kwambiri. Ndipo n’zosakayikitsa kuti Yesu anali ndi tsitsi lometedwa bwino komanso ndevu zoduliridwa bwino. Anthu okhawo omwe anali Anaziri, ngati Samisoni, ndi omwe sankameta ndevu komanso tsitsi lawo.​—Numeri 6:5; Oweruza 13:5.

Yesu anagwira ntchito ya ukalipentala kwa zaka pafupifupi 30 ndipo pa nthawiyo kunalibe zipangizo zangati zimene anthu amagwiritsa ntchito masiku ano. (Maliko 6:3) Choncho n’zosakayikitsa kuti ankaoneka wamphamvu. Ndipotu atangoyamba kumene utumiki wake, anapita kukachisi ‘n’kuthamangitsa onse amene anali ndi nkhosa ndi ng’ombe ndipo anawatulutsa m’kachisimo. Anakhuthula makobidi a osintha ndalama ndi kugubuduza matebulo awo.’ (Yohane 2:14-17) Yesu anachita zimenezi yekha popanda womuthandiza, choncho ayeneradi kuti anali munthu wamphamvu. Yesu ankagwiritsa ntchito thupi limene Mulungu anamukonzera pogwira ntchito imene anapatsidwa ndi Mulunguyo. Pa nthawi ina iye ananena kuti: “Ndiyenera kukalengeza uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu kumizinda inanso, chifukwa ndi zimene anandituma kudzachita.” (Luka 4:43) Yesu akanakhala wopanda mphamvu sakanakwanitsa kumayenda maulendo ataliatali wapansi ku Palesitina konse, n’kumalalikira uthenga umenewu.

“BWERANI KWA INE . . . NDIPO NDIDZAKUTSITSIMUTSANI”

Yesu anali wochezeka komanso wansangala. Choncho n’zosakayikitsa kuti anthu amene ‘ankagwira ntchito zolemetsa komanso omwe anali olemedwa,’ ankakopeka  naye ndipo ankapitadi kwa iye. (Mateyu 11:28-30) Komanso popeza Yesu anali wachikondi ndiponso wokoma mtima, anthu omwe anali ndi chidwi chofuna kuphunzira kwa iye, sankakayikira zoti atsitsimulidwadi. Ngakhalenso ana ankamukonda kwambiri Yesu. Tikutero chifukwa Baibulo limanena kuti nthawi ina iye “anatenga anawo m’manja mwake.”​—Maliko 10:13-16.

N’zoona kuti Yesu atatsala pang’ono kufa anamva ululu kwambiri. Komabe sikuti pa moyo wake wonse ankangokhala wodandaula kapena wosasangalala. Mwachitsanzo, Yesu ndi anthu ena anasangalala paphwando la ukwati wina ku Kana pamene iyeyo anasandutsa madzi kukhala vinyo wabwino kwambiri. (Yohane 2:1-11) Komanso anapita maulendo angapo kunyumba za anthu kukacheza komanso kukadya nawo limodzi chakudya ndipo kumeneko anaphunzitsa zinthu zosaiwalika.​—Mateyu 9:9-13; Yohane 12:1-8.

Yesu ankalalikira uthenga wabwino m’njira yosangalatsa kwambiri moti anthu amene ankamumvetsera ankasangalala komanso ankakhala ndi chiyembekezo cha moyo wosatha. (Yohane 11:25, 26; 17:3) Komanso ophunzira ake okwana 70 atamufotokozera zinthu zabwino zimene zinawachitikira pamene ankagwira ntchito yolalikira, iye “anakondwera kwambiri” n’kuwauza kuti: “Kondwerani chifukwa mayina anu alembedwa kumwamba.”​—Luka 10:20, 21.

“INU MUSAKHALE OTERO”

Atsogoleri achipembedzo a m’nthawi ya Yesu ankakonda kulamulira ena komanso kuchita zinthu zoti ena aziwatama. (Numeri 15:38-40; Mateyu 23:5-7) Koma mosiyana ndi atsogoleriwa, Yesu analangiza atumwi ake kuti ‘asamachite ulamuliro’ pa ena. (Luka 22:25, 26) Ndipotu iye anawachenjeza kuti: “Chenjerani ndi alembi amene amakonda kuyendayenda atavala mikanjo ndi kupatsidwa moni m’misika.”​—Maliko 12:38.

Yesu anali wosiyana kwambiri ndi anthu amenewa chifukwa ankakhala ndi anthu wamba moti tsiku lina atapita ku chikondwerero, anthu analephera kumuzindikira. (Yohane 7:10, 11) Ndipo nthawi ina ali ndi atumwi ake 11, sankadziwika kuti Yesu ndi uti moti Yudasi anachita kumupsompsona n’cholinga choti anthu omwe anabwera kudzamugwira amuzindikire.​—Maliko 14:44, 45.

Choncho ngakhale kuti sitidziwa zambiri zokhudza mmene Yesu ankaonekera, n’zodziwikiratu kuti sankaoneka ngati mmene anthu ambiri amamujambulira. Komabe chofunika kwambiri si kudziwa mmene ankaonekera ali padzikoli, koma udindo womwe ali nawo panopa.

“KWATSALA KANTHAWI PANG’ONO NDIPO DZIKO SILIDZANDIONANSO”

Tsiku limene Yesu anayankhula mawuwa ndi lomwenso anaphedwa n’kuikidwa m’manda. (Yohane 14:19) Iye anapereka moyo wake monga “dipo kuwombola anthu ambiri.” (Mateyu 20:28) Pa tsiku lachitatu, Mulungu anamuukitsa “monga mzimu” ndipo ‘anamulola kuonekera’ kwa ophunzira ake ena. (1 Petulo 3:18; Machitidwe 10:40) Kodi Yesu ankaoneka bwanji ataukitsidwa? Zikuoneka kuti ankaoneka mosiyana ndi mmene ankaonekera poyamba moti ngakhale ophunzira ake ena sanathe kumuzindikira. Mwachitsanzo, Mariya Mmagadala atamuona, anaganiza kuti ndi wosamalira munda. Komanso ophunzira ake awiri atakumana naye mumsewu wopita ku Emau, ankamuyesa kuti ndi mlendo.​—Luka 24:13-18; Yohane 20:1, 14, 15.

Kodi panopa tizimuona bwanji Yesu? Patatha zaka 60 kuchokera pamene Yesu anaphedwa, Yohane, yemwe anali mtumwi wake wokondedwa, anamuona m’masomphenya. Komatu sikuti anamuona ali pamtanda atamwalira. Iye anaona Yesu ali “Mfumu ya mafumu ndi Mbuye wa ambuye.” Choncho Yohane anaona Yesu ali Mfumu ya Ufumu wa Mulungu yomwe posachedwapa igonjetse adani onse a Mulungu, omwe ndi ziwanda ndiponso anthu onse oipa, n’kubweretsa madalitso osatha kwa anthu.​—Chivumbulutso 19:16; 21:3, 4.