M’Baibulo muli masomphenya ambiri ochititsa chidwi omwe amatithandiza kudziwa za amene ali kumwamba. Tikukulimbikitsani kuti muwerenge ndiponso kuganizira mofatsa nkhaniyi. Zinthu zambiri za m’masomphenyawa ndi zongoyerekezera, komabe zingakuthandizeni kudziwa amene amakhala kumwamba komanso mmene angakuthandizireni.

YEHOVA NDIYE WAMKULU

“Mpando wachifumu unaoneka uli pamalo ake kumwamba, wina atakhalapo. Wokhala pampandoyo, anali wooneka ngati mwala wa yasipi, ndi mwala wofiira wamtengo wapatali. Utawaleza wooneka ngati mwala wa emarodi unazungulira mpando wachifumuwo.”—Chivumbulutso 4:2, 3.

“Pamalo onse omuzungulira panali powala. Panali chinachake chooneka ngati utawaleza umene umaoneka mumtambo pa tsiku la mvula yamphamvu. Umu ndi mmene kuwala kozungulira pamalopo kunali kuonekera. Zinali kuoneka ngati ulemerero wa Yehova.”—Ezekieli 1:27, 28.

Mulungu anaonetsa masomphenyawa kwa mtumwi Yohane ndi mneneri Ezekieli ndipo anagwiritsa ntchito zinthu zodziwika bwino monga miyala yamtengo wapatali, utawaleza komanso mpando wachifumu pofuna kusonyeza ulemerero wa Yehova Mulungu. Izi zimatithandiza kudziwa kuti malo amene Yehova amakhala ndi okongola kwambiri, ochititsa kaso komanso amtendere.

Zimenezi zikugwirizana ndi mawu a wolemba masalimo akuti: “Yehova ndi wamkulu ndi woyenera kutamandidwa kwambiri. Iye ndi wochititsa mantha kuposa milungu ina yonse. Chifukwa milungu yonse ya anthu a mitundu ina ndi milungu yopanda pake, koma Yehova ndiye anapanga kumwamba. Ulemu ndi ulemerero zili pamaso pake. Mphamvu ndi kukongola zili m’nyumba yake yopatulika.”—Salimo 96:4-6.

Ngakhale kuti Yehova ndi wapamwamba kwambiri, amatilimbikitsa kuti tizipemphera kwa iye ndipo amatitsimikizira kuti amamvetsera mapemphero athu. (Salimo 65:2) Mulungu amatikonda kwambiri ndiponso amatisamalira moti mtumwi Yohane analemba kuti: “Mulungu ndiye chikondi.”—1 Yohane 4:8.

YESU ALI NDI MULUNGU

“[Sitefano], pokhala wodzazidwa ndi mzimu woyera, anayang’anitsitsa kumwamba ndi kuona ulemelero wa Mulungu ndi wa Yesu ataimirira kudzanja lamanja la Mulungu. Ndipo ananena kuti: ‘Taonani! Ndikuona kumwamba kotseguka, ndipo Mwana wa munthu waimirira kudzanja lamanja la Mulungu.’”—Machitidwe 7:55, 56.

Sitefano anaona masomphenyawa Yesu atangophedwa kumene ndi atsogoleri achiyuda omwewo amene Sitefano ankawauza zinthuzi. Masomphenyawa anasonyeza kuti Yesu anali moyo ndiponso kuti anali ataukitsidwa n’kupita kumwamba. Mtumwi Paulo analemba zokhudza nkhaniyi kuti: “[Yehova] anamuukitsa  [Yesu] kwa akufa ndi kumukhazika kudzanja lake lamanja m’malo akumwamba. Anamuika pamwambamwamba kuposa boma lililonse, ulamuliro uliwonse, amphamvu onse, ambuye onse, ndi dzina lililonse loperekedwa kwa wina aliyense, osati mu nthawi ino yokha, komanso imene ikubwerayo.”—Aefeso 1:20, 21.

Kuwonjezera pa kufotokoza udindo wa Yesu, Malemba amasonyezanso kuti Yesu amakonda kwambiri anthu ngati mmene Yehova amachitira. Yesu ali padzikoli, anachiritsa odwala komanso kuukitsa akufa. Iye anasonyeza kuti amakonda kwambiri Mulungu ndiponso anthu pamene anapereka moyo wake nsembe. (Aefeso 2:4, 5) Posachedwapa, Yesu adzagwiritsa ntchito udindo wake kuti adalitse anthu omvera padziko lonse lapansi.

ANGELO AMATUMIKIRA MULUNGU

Mneneri Danieli anati: “Ndinapitiriza kuyang’ana kufikira pamene mipando yachifumu inaikidwa ndipo Wamasiku Ambiri [Yehova] anakhala pa mpando wake wachifumu. . . . Panali atumiki okwana miliyoni imodzi amene anali kumutumikira nthawi zonse, ndi atumiki enanso mamiliyoni 100 amene anali kuimirira pamaso pake nthawi zonse.”—Danieli 7:9, 10.

M’masomphenya okhudza kumwambawa, Danieli sanaone mngelo mmodzi yekha koma ambirimbiri. Zimenezi ziyenera kuti zinali zochititsa mantha. Angelo ndi mizimu yamphamvu komanso yanzeru. Pali maudindo osiyanasiyana a angelo, ena ndi aserafi ndipo ena ndi akerubi. Baibulo limatchula za angelo maulendo oposa 250.

Sikuti angelo ndi anthu amene anakhalapo padziko lapansili kenako n’kupita kumwamba. Mulungu analenga angelo kalekale asanalenge anthu. Pamene Mulungu ankalenga dzikoli n’kuti angelo alipo kale moti ankaona zimenezi ndipo pamapeto pake anafuula ndi chisangalalo.—Yobu 38:4-7.

Njira imodzi imene angelo okhulupirika amatumikirira Mulungu ndi kuthandiza pa ntchito yofunika kwambiri yomwe ndi kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu padziko lonse. (Mateyu 24:14) Masomphenya amene mtumwi Yohane anaona amatsimikizira zimenezi. Iye analemba kuti: “Ndinaona mngelo winanso akuuluka chapafupi m’mlengalenga. Iye anali ndi uthenga wabwino wosatha woti aulengeze monga nkhani yosangalatsa kwa anthu okhala padziko lapansi, ndi kudziko lililonse, fuko lililonse, chinenero chilichonse, ndi mtundu uliwonse.” (Chivumbulutso 14:6) Masiku ano, angelo salankhula ndi  anthu ngati mmene ankachitira kale komabe amatsogolera anthu amene akulalikira uthenga wabwino kuti apeze anthu ofuna kumvetsera.

SATANA AMASOCHERETSA ANTHU AMBIRI

“Kumwamba kunabuka nkhondo: Mikayeli [Yesu Khristu] ndi angelo ake anamenyana ndi chinjoka. Chinjokacho ndi angelo ake chinamenya nkhondo, koma sichinapambane, ndipo malo awo sanapezekenso kumwamba. Choncho chinjokacho chinaponyedwa pansi, njoka yakale ija, iye wotchedwa Mdyerekezi ndi Satana, amene akusocheretsa dziko lonse lapansi kumene kuli anthu. Iye anaponyedwa kudziko lapansi, ndipo angelo akenso anaponyedwa naye limodzi.”—Chivumbulutso 12:7-9.

Sikuti kumwamba kwakhala kuli mtendere nthawi zonse. Anthu atangolengedwa kumene, mngelo mmodzi anagalukira Yehova chifukwa chakuti ankafunitsitsa kuti anthu azilambira iyeyo. Mngeloyo anapatsidwa dzina lakuti Satana limene limatanthauza kuti “Wotsutsa.” Kenako angelo ena anagwirizana naye ndipo anayamba kudziwika kuti ziwanda. Iwo ndi oipa kwambiri chifukwa amatsutsa Yehova ndipo achititsa kuti anthu ambiri ayambe kuchita zinthu zosemphana ndi malangizo abwino a Yehova.

Satana ndi ziwanda zake ndi oopsa komanso ankhanza. Iwo ndi adani a anthu ndipo akhala akuchititsa mavuto ambiri padzikoli. Mwachitsanzo, Satana anapha ziweto ndiponso antchito a Yobu. Kenako anachititsa kuti kubwere “chimphepo” chomwe chinagwetsa nyumba imene munali ana 10 a Yobu ndipo onse anafera pomwepo. Pambuyo pake, Satana anachititsanso kuti Yobu atuluke “zilonda zopweteka, kuyambira kuphazi mpaka kumutu.”—Yobu 1:7-19; 2:7.

Komabe Satana awonongedwa posachedwapa. Kungochokera pamene anaponyedwa padziko lapansi, iye amadziwa kuti “wangotsala ndi kanthawi kochepa.” (Chivumbulutso 12:12) N’zosangalatsa kudziwa kuti Satana sadzakhalapo mpaka kalekale.

OCHOKERA PADZIKO LAPANSI

“[Inu Yesu] munagula anthu kuti atumikire Mulungu. Anthu ochokera mu fuko lililonse, chinenero chilichonse, mtundu uliwonse, ndi dziko lililonse. Ndipo munawasandutsa mafumu ndi ansembe a Mulungu wathu, moti adzakhala mafumu olamulira dziko lapansi.”—Chivumbulutso 5:9, 10.

Yesu anaukitsidwa padziko pano kenako n’kupita kumwamba. Mofanana ndi zimenezi, pali anthu enanso amene adzaukitsidwe n’kupita kumwamba. Yesu anauza atumwi ake okhulupirika kuti: “Ndikupita kukakukonzerani malo. . . . Ndidzabweranso kudzakutengerani kwathu, kuti kumene kuli ineko inunso mukakhale kumeneko.”—Yohane 14:2, 3.

 Pali chifukwa chimene anthuwa adzapitire kumwamba. Iwo adzalamulira limodzi ndi Yesu mu Ufumu umene udzalamulire ndiponso kudalitsa anthu onse amene adzakhale padziko lapansi. Ufumu umenewu ndi umene Yesu anauza otsatira ake kuti aziupempherera kuti: “Atate wathu wakumwamba, dzina lanu liyeretsedwe. Ufumu wanu ubwere. Chifuniro chanu chichitike, monga kumwamba, chimodzimodzinso pansi pano.”—Mateyu 6:9, 10.

ZIMENE OKHALA KUMWAMBA ADZACHITE

Mtumwi Yohane anati: “Ndinamva mawu ofuula kuchokera kumpando wachifumu, akuti: ‘Taonani! Chihema cha Mulungu chili pakati pa anthu. . . . Iye adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.’”—Chivumbulutso 21:3, 4.

Masomphenyawa akunena za nthawi imene Ufumu wa Mulungu, womwe olamulira ake ndi Yesu limodzi ndi anthu amene anaukitsidwa n’kupita kumwamba, udzathetse ulamuliro wa Satana ndiponso kukonza dzikoli kuti likhale paradaiso. Zinthu zonse zimene anthu akhala akuvutika nazo zidzatha. Ngakhale imfa sidzakhalaponso.

Koma nanga bwanji za anthu ambirimbiri omwe anamwalira koma sadzaukitsidwa n’kupita kumwamba? M’tsogolo, anthuwa adzaukitsidwa ndipo adzakhala ndi mwayi wokhala ndi moyo wosatha m’Paradaiso padziko lapansi.—Luka 23:43.

Masomphenya onsewa amatitsimikizira kuti Yehova Mulungu, Mwana wake Yesu Khristu, angelo okhulupirika ndiponso anthu amene anapita kumwamba, amatikonda kwambiri ndipo amatifunira zabwino. Kuti mudziwe zambiri pa nkhaniyi, mukhoza kulankhula ndi Mboni za Yehova kapena kupita pawebusaiti ya www.jw.org/ny n’kuchita dawunilodi buku lakuti Zimene Baibulo Limaphunzitsa.