Anthu ambiri akaona malo okongola m’mabuku okopa alendo, amatengeka. Akatero amapita kumalowo n’cholinga choti akapume komanso akaiwaleko mavuto. Koma akabwerako, mavuto onse amene anawasiya aja amapeza akuwadikirira.

Kunena zoona munthu aliyense amalakalaka atamakhala pamalo okongola. Zimenezi zikubweretsa funso lakuti, ‘Kodi n’zothekadi kukhala m’Paradaiso kapena ndi maloto chabe? Ngati ali maloto chabe n’chifukwa chiyani anthufe timalakalaka titakhala m’Paradaiso? Nanga kodi n’zotheka kudzakhaladi m’Paradaiso?’

ANTHU AMBIRI AMADZIWA ZA PARADAISO

Kwa zaka zambiri, anthu akhala akuchita chidwi ndi nkhani ya Paradaiso. Ambiri amayamba kuganizira za nkhaniyi akadziwa kuti Baibulo limanena za munda wa ‘Edeni womwe unali chakum’mawa.’ Kodi n’chiyani chinapangitsa kuti mundawu ukhale wochititsa chidwi? Baibulo limati: “Yehova Mulungu anameretsa m’nthaka mtengo wamtundu uliwonse wooneka bwino ndi wa zipatso zabwino kudya.” M’mundamu munali malo abwino komanso okongola kwambiri. Chinanso chochititsa chidwi chinali ‘mtengo wa moyo womwe unali pakati pa mundawo.’​—Genesis 2:8, 9.

Komanso Baibulo limanena kuti m’mundawo munali mitsinje 4. Iwiri ya mitsinje imeneyi idakalipo mpaka pano. Mitsinje yake ndi Hidekeli (Tigris) komanso Firate (Euphrates). (Genesis 2:10-14) Mitsinje imeneyi imapita ku Persian Gulf kudzera ku Iraq, dera limene poyamba linali mbali ya Perisiya.

N’chifukwa chake anthu ambiri a ku Persia amakhulupirira za dziko lapansi la Paradaiso. Mwachitsanzo, kumalo ena osungirako zinthu zochititsa chidwi (Philadelphia Museum of Art), mumzinda wa Pennsylvania ku U.S.A. kuli kalapeti ina ya m’zaka za m’ma 1500. Pakalapetiyi anajambulapo munda wokongola wokhala ndi mitengo komanso maluwa ndipo uli kumpanda. Mawu achiperisiya akuti “munda wamaluwa womwe uli kumpanda” angatanthauzenso “Paradaiso.” Ndipo zimene anajambula pakalapetizi, zikufananako ndi zimene Baibulo limafotokoza zokhudza munda wa Edeni.

Nkhani yonena za Paradaiso imakambidwa ndi anthu azilankhulo komanso zikhalidwe zosiyanasiyana padziko lonse. Zili choncho chifukwa choti pamene anthu anayamba kusamukira kumadera ena a dziko lapansi, ankadziwa nkhani yokhudza Paradaiso woyambirira. Ndiyeno pang’ono ndi pang’ono anayamba kusakaniza zimene ankadziwazo ndi nthano komanso zinthu zina zimene anayamba kuzikhulupirira kumeneko. Ngakhale masiku ano, anthu ambiri amagwiritsa ntchito mawu akuti Paradaiso akamanena za malo okongola.

ANTHU AKHALA AKUFUFUZA MALO AMENE PANALI PARADAISO

Anthu ena ofufuza malo amati anapeza pamene panali Paradaiso woyambirira. Mwachitsanzo, munthu wina yemwe anali mkulu wa asilikali ku Britain, dzina lake Charles Gordon, atafika ku Seychelles mu 1881, anachita chidwi kwambiri ndi kukongola kwa malo ena otchedwa Vallée de Mai. Iye anati malo amenewa ndi munda wa Edeni. Panopa bungwe la UNESCO linaika malowa m’gulu la zinthu zochititsa chidwi. M’zaka za m’ma 1400 munthu wina wofufuza malo wa ku Italy, dzina lake Christopher Columbus, anafika pachilumba cha Hispaniola, chomwe panopa ndi Dominican Republic komanso Haiti. Ataona kukongola kwa malowo, anaganiza kuti mwina watsala pang’ono kupeza malo amene panali munda wa Edeni.

Buku lina la mbiri yakale lili ndi zinthu zokhudza mapu a malo akale oposa 190. (Mapping Paradise) Ambiri mwa mapuwa amasonyeza Adamu ndi Hava ali m’munda wa Edeni. Amodzi mwa mapu amenewa ndi ochititsa chidwi ndipo anawatenga mumpukutu wina wa zaka za m’ma 1200 wa Beatus wa ku Liébana. Pamwamba pa mapuwa pali bokosi la makona 4 ndipo pakati pa bokosilo pali chithunzi cha Paradaiso. Ndiyeno pali mitsinje 4 yomwe ikuchokera pachithunzi cha Paradaisocho kupita kumakona 4 a bokosilo. Mitsinje yake ndi Tigirisi, Firate, Pisoni ndi Gihoni. Izi ziyenera kuti zikuimira kufalikira kwa Chikhristu kumbali zonse za padziko lapansi. Zinthu ngati zimenezi zikusonyeza kuti ngakhale kuti anthu sadziwa pomwe panali Paradaiso woyambirira,  ambiri amamukumbukirabe ndipo amaona kuti anali malo okongola kwambiri.

Wolemba ndakatulo wina wa ku England wa zaka za m’ma 1600, dzina lake John Milton, analemba ndakatulo yotchuka kwambiri yakuti, Paradaiso Wotayika. Ndakatuloyi inachokera pa nkhani ya m’Baibulo ya m’buku la Genesis yonena za kuchimwa kwa Adamu ndi Hava komanso kuthamangitsidwa kwawo mu Edeni. Mu ndakatulo imeneyi anatchula lonjezo loti anthu adzakhala ndi moyo kosatha. Iye anati: “Popeza dziko lonse lidzakhala Paradaiso.” Kenako Milton analembanso ndakatulo ina ya mutu wakuti, Paradaiso Wobwezeretsedwa.

ANTHU SAKUCHITANSO CHIDWI NDI NKHANI YA PARADAISO

Monga taonera, kuyambira kale anthu akhala akudziwa komanso kukamba nkhani yakuti kunali Paradaiso. Koma panopa zikuoneka kuti anthu sakuchitanso chidwi ndi nkhaniyi. Kodi n’chifukwa chiyani zili choncho? Mogwirizana ndi zimene buku tinalitchula lija linanena, chifukwa chachikulu n’chakuti, “akatswiri amaphunziro azachipembedzo anasiya kuchita chidwi ndi nkhani yokhudza malo amene panali Paradaiso. Izi zachititsa kuti anthu asamaganizirenso za Paradaiso.”​—Mapping Paradise.

Anthu ambiri amene amapita kutchalitchi amaphunzitsidwa kuti adzapita kumwamba osati adzakhala m’Paradaiso padzikoli. Koma palemba la Salimo 37:29 Baibulo limati: “Olungama adzalandira dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.” Popeza panopa dzikoli si Paradaiso, kodi tingakhulupirire bwanji kuti lonjezo limeneli lidzakwaniritsidwa? *

ZOTI DZIKO LONSE LIDZAKHALA PARADAISO NDI ZOONA

Yehova Mulungu ndi amene analenga Paradaiso woyamba uja ndipo akulonjeza kuti adzachititsa kuti dzikoli likhalenso Paradaiso. Kodi adzachita bwanji zimenezi? Paja Yesu anatiphunzitsa kuti tizipemphera kuti: “Ufumu wanu ubwere. Chifuniro chanu chichitike, monga kumwamba, chimodzimodzinso pansi pano.” (Mateyu 6:10) Ufumu umenewu udzalamulira dziko lonse lapansi ndipo Mfumu yake ndi Yesu Khristu. Ufumuwu udzalowa m’malo mwa maufumu onse apadziko lapansi. (Danieli 2:44) Ufumu umenewu ukamadzalamulira, chifuniro cha Mulungu chokhudza Paradaiso ‘chidzachitika.’

Mneneri Yesaya anauziridwa ndi Mulungu kuti afotokoze zoti m’Paradaiso, mavuto onse amene anthu amakumana nawo adzatha. (Yesaya 11:6-9; 35:5-7; 65:21-23) Tikukulimbikitsani kuti muwerenge mavesi amene ali pamwambawa m’Baibulo lanu. Mukatero mudziwa zimene Mulungu adzachitire anthu omvera. Izi zikuthandizaninso kuti muzikhulupirira malonjezo amenewa. Mofanana ndi mmene zinalili ndi Adamu asanachimwe, anthu amene adzakhalepo pa nthawiyo adzakhala m’Paradaiso ndipo Mulungu azidzasangalala nawo.​—Chivumbulutso 21:3.

Ndiye kodi tingatsimikize bwanji kuti dzikoli lidzakhaladi Paradaiso? Chifukwa Baibulo limati: “Kunena za kumwamba, kumwamba ndi kwa Yehova, koma dziko lapansi analipereka kwa ana a anthu.” “Mulungu amene sanganame” ndi amene “analonjeza kalekale” kuti dzikoli lidzakhala Paradaiso. (Salimo 115:16; Tito 1:2) M’nkhaniyi taona kuti m’Baibulo muli lonjezo losangalatsa kwambiri loti dzikoli lidzakhala Paradaiso.

^ ndime 15 N’zochititsanso chidwi kuti mu Korani, vesi 105 ya sura 21, Al-Anbiya’ [Aneneri], limati: “Atumiki anga olungama adzalandira dziko lapansi.”