Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

NSANJA YA OLONDA Na. 4 2017 | Kodi Baibulo Limanena Zotani pa Nkhani ya Imfa?

KODI INUYO MUKUGANIZA BWANJI?

Kodi chinali cholinga cha Mulungu kuti anthufe tizifa? Baibulo limati: “[Mulungu] adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso.”​Chivumbulutso 21:4.

Magaziniyi ikufotokoza zimene Baibulo limanena pa nkhani ya imfa.

 

NKHANI YAPACHIKUTO

Kodi Munthu Akamwalira Amakakhalanso Ndi Moyo Kwinakwake?

Popeza anthu amasiyana maganizo pa nkhani ya zimene zimachitika munthu akamwalira, kodi n’chiyani chimene chingatithandize kudziwa zolondola pa nkhaniyi?

NKHANI YAPACHIKUTO

Kodi Baibulo Limanena Zotani pa Nkhani ya Imfa?

Kodi pali chinachake chimene chimapitirizabe kukhala ndi moyo munthu akamwalira? Kodi munthu ali ndi mzimu umene suufa? Kodi munthu akamwalira amapita kuti?

Mungatani Ngati Munthu Amene Mumamukonda Akudwala Matenda Oti Sachira?

Kodi achibale angalimbikitse komanso kusamalira bwanji munthu amene akudwala matenda oti sachira? Kodi achibale angatani kuti asavutike kwambiri pa nthawi imene m’bale wawoyo akudwala?

Elias Hutter Anamasulira Mabaibulo Othandiza Kwambiri

Elias Hutter, yemwe anakhalako m’zaka za m’ma 1500 anamasulira Mabaibulo omwe anali othandiza kwambiri

Zomwe Yesu Ananena Zokhudza Kachilembo Kachiheberi Zimalimbitsa Chikhulupiriro Chathu

Kodi mfundo ya Yesu inali yotani pamene ananena za kachilembo kakang’ono ka afabeti?

Kodi Dzikoli Lidzakhaladi Paradaiso Kapena ndi Maloto Chabe?

Kuyambira kale, anthu akhala akudziwa za Paradaiso amene anatayika. Kodi zidzatheka kuti Paradaiso ameneyu akhalekonso?

Kodi Baibulo Limanena Zotani?

Nkhawa ndi mbali imodzi ya moyo wa munthu. Kodi n’zotheka kukhala opanda nkhawa?

Zina zimene zili pawebusaiti

N’chifukwa Chiyani Anthu Amafa?

Yankho limene Baibulo limapereka pa nkhaniyi ndi lolimbikitsa komanso lopatsa chiyembekezo