Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Palibe Angathawe Imfa

Palibe Angathawe Imfa

TIYEREKEZE kuti mukuonera filimu ya munthu winawake wotchuka amene amakusangalatsani, yemwe mwina ndi woimba. Filimuyo ikuyamba ndi kuonetsa munthuyo ali mwana, kenako akuphunzira kuimba ndipo kenako akuyeserera kuimba pogwiritsa ntchito chida chinachake. Pambuyo poti wakula akumuonetsa akuimba m’madansi, atapita kumayiko osiyanasiyana komanso atakhala wotchuka padziko lonse. Koma pasanapite nthawi yaitali, mukuyamba kuona zithunzi zake zosonyeza kuti wakalamba ndipo pamene filimuyo ikufika kumapeto, mukuona kuti munthu uja wamwalira.

Ngakhale kuti imeneyi inali filimu chabe, zimenezi ndi zimene zimachitikadi pa moyo wa munthu. Kaya munthuyo anali woimba, wasayansi, katswiri wothamanga kapena munthu wina wotchuka, pamapeto pake amakalamba kenako n’kumwalira. Amakhala kuti anachita zambiri ndithu, koma kodi akanakhala kuti sanakalambe kenako n’kufa si zoona kuti akanachita zambiri kuposa zomwe anachitazo?

Zimenezi ndi zomvetsa chisoni, komabe ndi zimene tonsefe timayembekezera. (Mlaliki 9:5) Ngakhale munthu atayesetsa bwanji, palibe chimene angachite kuti asakalambe kapena asadzafe. Ndipotu anthu ena amamwalira asanakalambe n’komwe chifukwa cha ngozi kapena matenda. Mogwirizana ndi zimene Baibulo limanena, anthufe tili ngati nkhungu ya m’mawa “yongoonekera kanthawi kenako n’kuzimiririka.”​—Yakobo 4:14.

Anthu ena amaona kuti moyo ndi waufupi komanso wopanda phindu choncho amangoyendera mfundo yakuti, “tiyeni tidye ndi kumwa, pakuti mawa tifa.” (1 Akorinto 15:32) Komatu anthuwa akamachita zimenezi amakhala kuti akungovomereza mfundo yoti palibe amene angathawe imfa. Mwina inunso pa nthawi ina, makamaka pamene mukukumana ndi mavuto, mungafunse kuti, ‘Kodi Mulungu ankafuna kuti tizikhala ndi moyo waufupi chonchi?’ Ndiye kodi mungapeze kuti yankho la funso limeneli?

Masiku ano anthu ambiri amayembekezera kuti asayansi angatithandize kupeza yankho la funsoli. Chifukwa cha kupita patsogolo kwa sayansi komanso nkhani zachipatala, moyo wathu masiku ano ukumakhala wotalikirapo. Ndipo asayansi ena akuyesetsabe kuti apeze njira zotalikitsira moyo kuposa pamenepa. Kaya adzapezadi njira zimenezi kapena ayi, padzakhalabe mafunso akuti: N’chifukwa chiyani timakalamba komanso kufa? Kodi pali chiyembekezo chilichonse choti imfa idzatha? Nkhani zotsatira ziyankha mafunso amenewa komanso lakuti: Kodi Mulungu ankafuna kuti tizikhala ndi moyo waufupi chonchi?