Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi N’chifukwa Chiyani Timakalamba Komanso Kufa?

Kodi N’chifukwa Chiyani Timakalamba Komanso Kufa?

SICHINALI cholinga cha Mulungu kuti anthufe tizifa. Makolo athu oyambirira, Adamu ndi Hava analengedwa ndi matupi angwiro moti bwenzi pano alipobe. Umboni wa zimenezi ndi zimene Yehova anauza Adamu zokhudza zipatso za mtengo wina womwe unali m’munda wa Edeni.

Mulungu anamuuza kuti: “Tsiku limene udzadya [zipatso zake] udzafa ndithu.” (Genesis 2:17) Zikanakhala kuti Adamu analengedwa m’njira yoti adzakalambe kenako n’kufa, ndiye kuti lamuloli likanakhala lopanda ntchito. Ngakhalenso Adamuyo ankadziwa kuti sangafe ngati atapanda kudya zipatso za mtengowo.

MULUNGU SANALI NDI CHOLINGA CHOTI ANTHU AZIFA

Sikuti Adamu ndi Hava ankasowa chakudya chifukwa m’mundamo munali mitengo yambiri ya zipatso zomwe akanatha kudya. (Genesis 2:9) Ndipotu akanapanda kudya zipatso za mtengo umene anawaletsawo akanasonyeza kuti anali omvera. Akanasonyezanso kuti ankadziwa kuti Mulungu ali ndi ufulu wowauza zochita.

CHIFUKWA CHAKE ADAMU NDI HAVA ANAFA

Kuti timvetse chifukwa chake Adamu ndi Hava anafa, tiyeni tione zimene Satana anakambirana ndi Hava, zomwe zotsatira zake zimatikhudza. Satana anagwiritsa ntchito njoka kuti anene bodza. Baibulo limati: “Tsopano njoka inali yochenjera kwambiri kuposa nyama zonse zakutchire zimene Yehova Mulungu anapanga. Ndipo njokayo inafunsa mkaziyo kuti: ‘Eti n’zoona kuti Mulungu anati musadye zipatso za mtengo uliwonse wa m’mundamu?’”​—Genesis 3:1.

Hava anayankha njokayo kuti: “Zipatso za mitengo yonse ya m’mundamu anatiuza kuti tizidya. Koma zipatso za mtengo umene uli pakati pa munda, Mulungu anati, ‘Musadye zipatso zake ayi, musaukhudze kuti mungafe.’” Kenako njokayo inamuuza kuti: “Kufa simudzafa ayi. Mulungutu akudziwa kuti tsiku limene mudzadye chipatso cha mtengo umenewu, maso anu adzatseguka ndithu, ndipo mudzafanana ndi Mulungu. Mudzadziwa zabwino ndi zoipa.” Pamenepa Satana anatanthauza kuti Yehova ndi wabodza ndipo anabisira Adamu ndi Hava zinthu zabwino.​—Genesis 3:2-5.

Hava anakhulupirira bodzali ndipo anayamba kuyang’anitsitsa zipatso za mtengowo. Iye anaona kuti zinali zosiririka komanso zabwino kudya moti anathyola n’kudya. Baibulo limati: “Pambuyo pake, anapatsako mwamuna wake pamene anali limodzi, ndipo nayenso anadya.”​—Genesis 3:6.

Mulungu anauza Adamu kuti: ‘Tsiku limene udzadya zipatso zake, udzafa ndithu.’​—GENESIS 2:17

Mulungu ayenera kuti anakhumudwa kwambiri ataona kuti ana akewa asankha mwadala kuti asamumvere. Ndiye kodi iye anatani? Anauza Adamu kuti: ‘Udzabwerera kunthaka, pakuti n’kumene unatengedwa. Popeza ndiwe fumbi, kufumbiko udzabwerera.’ (Genesis 3:17-19) Chifukwa cha zimenezi, “masiku onse amene Adamu anakhala ndi moyo anakwana zaka 930, kenako anamwalira.” (Genesis 5:5) Adamu atafa sanapite kumwamba kapena kudziko lamizimu. Yehova asanamulenge kuchokera kufumbi, Adamu kunalibe. Choncho atafa anakhalanso dothi ngati mmene zinalili asanalengedwe ndipo kunalibenso. Izitu n’zomvetsa chisoni kwambiri.

 CHIFUKWA CHAKE SI IFE ANGWIRO

Chifukwa choti Adamu ndi Hava anasankha mwadala kusamvera, anataya mwayi wokhala angwiro komanso wokhala ndi moyo wosatha. Zinthu zinasintha kwambiri pa moyo wawo moti anakhala opanda ungwiro komanso ochimwa. Koma kusamvera kwawoku sikunakhudze iwo okha. Anapatsira ana awo uchimowo. Lemba la Aroma 5:12 limati: ‘Uchimo unalowa m’dziko kudzera mwa munthu mmodzi [Adamu], ndi imfa kudzera mwa uchimo, imfayo n’kufalikira kwa anthu onse chifukwa onse anachimwa.’

Baibulo limati uchimo ndi imfa zili ngati “chophimba chimene chikuphimba anthu onse, ndi nsalu imene yakuta mitundu yonse.” (Yesaya 25:7) Chophimba chimenechi chimakuta mtundu wa anthu ngati utsi wapoizoni moti anthu sapeza kothawira. N’zoonadi kuti kudzera ‘mwa Adamu onse amafa.’ (1 Akorinto 15:22) Tikaganizira zimenezi mwina tingafunse funso limenenso mtumwi Paulo anafunsa lakuti: “Ndani adzandipulumutse ku thupi limene likufa imfa imeneyi?” Kodi pali amene angatipulumutse?​—Aroma 7:24.