Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Anthu Amene Anamwalira Adzakhalanso Ndi Moyo?

Kodi Anthu Amene Anamwalira Adzakhalanso Ndi Moyo?

Imfa imakhudza aliyense. Koma kodi imfa ndi mathero a zonse? Kodi anthu amene anamwalira ndiye kuti basi anaiwalidwa? Kodi pali chiyembekezo chilichonse chokhudza anthu amene anamwalira?

TAONANI ZIMENE BAIBULO LIMANENA:

ANTHU AMENE ANAMWALIRA SANAIWALIDWE

“Onse ali m’manda achikumbutso . . . adzatuluka.”—Yohane 5:28, 29.

Mulungu sanaiwale anthu amene anamwalira ndipo adzaukitsa onse amene ali m’manda achikumbutso.

AKUFA ADZAUKITSIDWA PADZIKOLI

“Kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama omwe.”​—Machitidwe 24:15.

Anthu mamiliyoni ambirimbiri adzaukitsidwa n’kupatsidwa mwayi wokhala ndi moyo kwamuyaya m’dziko la mtendere.

CHIYEMBEKEZO CHOTI AKUFA ADZAUKITSIDWA N’CHODALIRIKA

“[Mulungu] amawerenga nyenyezi zonse, ndipo zonsezo amazitchula mayina ake.”​—Salimo 147:4.

Ngati Mulungu amakwanitsa kutchula nyenyezi iliyonse dzina, ndiye kuti akukumbukira anthu amene akufuna kudzawaukitsa.