NSANJA YA OLONDA Na. 3 2019 | Kodi Mulungu Ankafuna Kuti Tizikhala Ndi Moyo Waufupi Chonchi?

Anthu ambiri amakhala ndi funso limeneli ndipo yankho limene munthu angalione kuti ndi lolondola lingakhudze kwambiri zimene amachita pa moyo wake.

Palibe Angathawe Imfa

Ngakhale titayesetsa bwanji sitingathawe zotsatira zaukalamba ndi imfa. Kodi Mulungu ankafuna kuti tizikhala ndi moyo waufupi chonchi?

Kufufuza Moyo Wautali

Asayansi ena akuyesetsa kuti apeze chimene chimachititsa kuti tizikalamba. Kodi zotsatira za kafukufuku wawoyu ndi zotani?

Tinalengedwa Kuti Tizikhala Kwamuyaya

Ndani amene safuna kukhala ndi moyo wautali komanso wosangalala?

Kodi N’chifukwa Chiyani Timakalamba Komanso Kufa?

Sichinali cholinga cha Mulungu kuti anthu azifa. Makolo athu oyamba analengedwa ndi thupi komanso maganizo angwiro moti bwenzi alipobe mpaka pano.

Kodi Imfa Idzagonjetsedwa Bwanji?

Mwachikondi Mulungu anakonza zowombola anthu ku imfa popereka dipo.

Kodi Mungatani Kuti Mudzakhale Ndi Moyo Wabwino Kuposa Umene Tili Nawo Panopa?

Pali “msewu” umene muyenera kuyendamo kuti mudzapeze moyo umene Mulungu wakonzera anthu amene amamukonda.

Zimene Mungachite Kuti Muzisangalala

Kodi malangizo a m’Baibulo angakuthandizeni bwanji kukhala wokhutira, kulimbitsa banja lanu komanso kupirira matenda?