ZIPEMBEDZO padziko lonse lapansi monga Katolika, Orthodox komanso Chibuda zimaona kuti si bwino kuti atsogoleri awo akwatire. Koma anthu ambiri amaona kuti zimenezi n’zimene zachititsa kuti atsogoleri azipembedzo zosiyanasiyana azipezeka ndi milandu yokhudza chiwerewere.

Choncho tingadzifunse kuti, Kodi Baibulo limanena kuti atumiki achikhristu asamakwatire? Kuti tiyankhe funsoli tiyeni tione mmene nkhaniyi inayambira komanso mmene Mulungu amaionera.

KODI NKHANI YOLETSA KUKWATIRA INAYAMBA BWANJI?

Mu 2006, Benedict 16, yemwe anali papa pa nthawiyo, anakamba nkhani kwa akuluakulu a tchalitchi cha Katolika. M’nkhaniyo ananena kuti “mwambo woletsa kukwatira unayamba cham’nthawi ya Atumwi.”

Komabe Akhristu a m’nthawi ya atumwi sankaletsa anthu kukwatira. Mwachitsanzo mtumwi Paulo anachenjeza Akhristu zokhudza anthu amene amalankhula “mawu ouziridwa omwe ndi osocheretsa” ndipo ‘amaletsa anthu kukwatira.’—1 Timoteyo 4:1-3.

M’zaka za m’ma 100, matchalitchi ena anayamba kutsatira mwambo woletsa atsogoleri awo kuti akwatire. Buku lina limanena kuti zimenezi zinali “zogwirizana ndi maganizo odziletsa pa nkhani ya kugonana amene anthu ambiri anayamba kukhala nawo mu ulamuliro wa Aroma.”—Celibacy and Religious Traditions.

M’zaka zotsatira, akuluakulu a matchalitchi ankalimbikitsa mwambo woletsa kukwatira. Ankaona kuti kugonana kumaipitsa munthu ndipo sizingakhale bwino kuti anthu oipitsidwa azitumikira mumpingo. Ngakhale zili choncho, buku  lina limanena kuti “m’zaka za m’ma 900 ansembe ndiponso mabishopu ambiri anali okwatira.”—Encyclopædia Britannica.

Pamisonkhano ya akuluakulu a tchalitchi cha Katolika imene inachitika ku Rome m’chaka cha 1123 ndi 1139, anasankha kuti azitsatira lamulo loti atsogoleri awo asamakwatire. Mpaka pano tchalitchi cha Katolika chimatsatirabe lamuloli. Izi zinathandiza kuti tchalitchi chisathe mphamvu kapena kuluza chuma ansembe okwatira akamwalira n’kusiyira akazi ndiponso ana awo chuma cha tchalitchi.

KODI MULUNGU AMAONA BWANJI NKHANIYI?

Maganizo a Mulungu pa nkhaniyi tingawapeze m’Baibulo. Mwachitsanzo, tingapezemo mawu a Yesu okhudza anthu amene amakhala osakwatira ngati iyeyo, “chifukwa cha ufumu wakumwamba.” (Mateyu 19:12) Nayenso mtumwi Paulo ananena kuti panali Akhristu amene anatsatira chitsanzo chake n’kukhala osakwatira “chifukwa cha uthenga wabwino.”—1 Akorinto 7:37, 38; 9:23.

Koma sikuti Yesu kapena Paulo ankalamula kuti atumiki achikhristu azikhala osakwatira. Yesu ananena kuti si anthu onse amene angakhale ndi “mphatso” yokhala osakwatira. Pamenenso Paulo ankanena za anthu “amene sali pabanja,” anafotokoza momveka bwino kuti: “Ndilibe lamulo lililonse la Ambuye, koma ndikupereka maganizo anga.”—Mateyu 19:11; 1 Akorinto 7:25.

Baibulo limasonyezanso kuti atumiki ena a m’nthawi ya atumwi, kuphatikizapo mtumwi Petulo, anali okwatira. (Mateyu 8:14; Maliko 1:29-31; 1 Akorinto 9:5) Podziwa kuti chiwerewere chinali chofala mu ulamuliro wa Aroma, Paulo analemba kuti woyang’anira wachikhristu amene ali pa banja ayenera kukhala “mwamuna wa mkazi mmodzi” komanso “woti ana ake amamumvera ndi mtima wonse.”—1 Timoteyo 3:2, 4.

Koma sikuti ankangokhala m’banja popanda kugonana chifukwa Baibulo limanena momveka bwino kuti mwamuna “azipereka kwa mkazi wake mangawa ake” komanso kuti anthu okwatirana ‘asamanane’ mangawa. (1 Akorinto 7:3-5) Choncho zikuonekeratu kuti Mulungu sanapereke lamulo loletsa kukwatira ndipo atumiki achikhristu sayenera kukakamizidwa kuti akhale osakwatira.

KUSAKWATIRA CHIFUKWA CHA UTHENGA WABWINO

Ngati si zoona kuti Mulungu amaletsa kukwatira, n’chifukwa chiyani Yesu ndi Paulo ananena kuti kusakwatira n’kothandiza? Ananena zimenezi chifukwa choti munthu amene sali pa banja amakhala ndi mipata yambiri yoti alalikire uthenga wabwino. Sakhalanso ndi nkhawa zimene anthu a pa banja amakhala nazo, choncho akhoza kuchita zambiri potumikira Mulungu.—1 Akorinto 7:32-35.

Chitsanzo pa nkhaniyi ndi David. Iye anasiya ntchito yake yabwino ku Mexico City n’kupita kudera lakumidzi ku Costa Rica kuti azikaphunzitsa anthu Baibulo. Iye ananena kuti kukhala wosakwatira kwamuthandiza kwambiri kuti izi zitheke. Iye anati: “Zinali zovuta kuti ndizolowere chikhalidwe komanso moyo watsopano. Koma poti ndili ndekha sizinandivute kwenikweni.”

Claudia nayenso sali pa banja ndipo wasamukira kumadera angapo kumene kukufunika olalikira ambiri. Iye anati: “Ndimatumikira Mulungu mosangalala kwambiri. Panopa chikhulupiriro changa ndi champhamvu komanso ubwenzi wanga ndi Mulungu walimba kwambiri chifukwa choti ndaona akundisamalira.”

“Kaya tili pa banja kapena ayi, tikhoza kukhala osangalala ngati timachita zonse zimene tingathe potumikira Yehova Mulungu.”—Claudia

Munthu akhoza kukhala wosangalala ngakhale kuti sali pa banja. Claudia ananenanso kuti: “Kaya tili pa banja kapena ayi, tikhoza kukhala osangalala ngati timachita zonse zimene tingathe potumikira Yehova Mulungu.”—Salimo 119:1, 2.