Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Nsanja ya Olonda  |  Na. 2 2017

Anthu amene adzapulumuke adzakhala m’dziko lokongola kwambiri

Kodi Baibulo Limanena Zotani?

Kodi Baibulo Limanena Zotani?

Kodi tili ‘m’masiku otsiriza’?

Kodi mungayankhe bwanji?

  • Inde

  • Ayi

  • Mwina

Zimene Baibulo limanena

“Masiku otsiriza adzakhala nthawi yapadera komanso yovuta.” (2 Timoteyo 3:1) Ulosi wa m’Baibulo komanso zimene zikuchitika masiku ano zikusonyeza kuti tikukhala ‘m’masiku otsiriza.’

Mfundo zinanso zomwe tikuphunzira m’Baibulo

  • Linaneneratu kuti m’masiku otsiriza padzakhala nkhondo, njala, zivomerezi ndiponso matenda oopsa.—Mateyu 24:3, 7; Luka 21:11.

  • Linaneneratunso kuti m’masiku otsiriza anthu ambiri adzakhala ndi makhalidwe oipa komanso sadzakonda Mulungu.—2 Timoteyo 3:2-5.

Kodi zinthu zidzakhala bwanji m’tsogolo?

Anthu ena amakhulupirira kuti . . . pa mapeto pa masiku otsiriza, dziko ndiponso anthu onse adzawonongedwa, pomwe ena amakhulupirira kuti zinthu zidzayamba kuyenda bwino. Kodi inuyo mukuganiza bwanji?

Zimene Baibulo limanena

“Olungama adzalandira dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.”Salimo 37:29.

Mfundo zinanso zomwe tikuphunzira m’Baibulo

  • Pa mapeto pa masiku otsiriza anthu onse oipa adzawonongedwa.—1 Yohane 2:17.

  • Dziko lidzasinthidwa kuti likhale lokongola kwambiri.—Yesaya 35:1, 6.