KODI INUYO MUKUGANIZA BWANJI?

Kodi mphatso yaikulu kwambiri imene Mulungu anatipatsa ndi iti?

Baibulo limati: “Mulungu anakonda kwambiri dziko mwakuti anapereka Mwana wake wobadwa yekha.”Yohane 3:16.

Nsanja ya Olonda iyi ikufotokoza chifukwa chimene Mulungu anatumizira Yesu padziko lapansi kuti adzatifere komanso zimene tingachite posonyeza kuti timayamikira mphatsoyi.