Pali mavuto ena amene sitingawapewe kapena kuwathetsa. Mwachitsanzo, ngati mwaferedwa kapena ngati mukudwala matenda okhalitsa palibe chimene mungachite, mungangofunika kupirira. Kodi Baibulo lingatithandize bwanji pa mavuto ngati amenewa?

MATENDA OKHALITSA

Mtsikana wina dzina lake Rose anati: “Ndinabadwa ndi vuto linalake limene limachititsa kuti ndizimva kupweteka kwambiri. Vutoli limachititsa kuti thanzi langa lizifooka.” Vuto lalikulu limene Rose ankakumana nalo linali lakuti nthawi zambiri akamawerenga Baibulo komanso mabuku othandiza kuphunzira Baibulo ankalephera kuika maganizo ake pa zimene akuwerengazo. Koma mawu a Yesu a palemba la Mateyu 19:26 ndi amene anamuthandiza. Lembali limati: “Zinthu zonse n’zotheka kwa Mulungu.” Rose anazindikira kuti pali njira zambiri zophunzirira. Popeza nthawi zambiri ankamva kupweteka akamawerenga, anaganiza zoti azingomvetsera Baibulo kapena mabuku othandiza kuphunzira Baibulo amene anajambulidwa. * Rose anati: “Njira imeneyi ndi imene inandithandiza kulimbitsa ubwenzi wanga ndi Mulungu.”

Nthawi zina Rose amakhumudwa chifukwa choona kuti sakutha kuchita zimene ankachita poyamba. Koma lemba limene limamulimbikitsa ndi la 2 Akorinto 8:12 lomwe limati: “Mphatso yochokera pansi pa mtima ndi imene Mulungu amakondwera nayo, chifukwa Mulungu amafuna kuti munthu apereke zimene angathe, osati zimene sangathe.” Mawu amenewa amamukumbutsa Rose mfundo yakuti Mulungu amasangalala ndi zimene iye amachita chifukwa ndi zimene angakwanitse.

 IMFA YA MNZATHU KAPENA WACHIBALE

Delphine amene tamutchula kale uja anati: “Mwana wanga wamkazi wazaka 18 atamwalira, ndinali ndi chisoni kwambiri moti ndinkangoona ngati nanenso ndifa. Ndinkaona kuti palibe chomwe chinkayenda.” Koma mawu a palemba la Salimo 94:19 ndi omwe anamuthandiza. Lembali limati: “Malingaliro osautsa atandichulukira mumtima mwanga, mawu anu otonthoza anayamba kusangalatsa moyo wanga.” Delphine anati: “Ndinapempha Yehova kuti andithandize kupeza zochita zimene zingandithandize kuti ndizisangalala.”

Delphine anayamba kumatanganidwa ndi ntchito yophunzitsa anthu Baibulo. Kenako zinthu zinayamba kusintha. Iye ankaona kuti ali ngati chekeni chomwe chathyoka koma munthu angathe kuchigwiritsabe ntchito. Ankaona kuti ngakhale kuti ali ndi mavuto ambiri, angathe kuthandiza ena. Delphine anati: “Ndikamagwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo pothandiza anthu amene ndinkaphunzira nawo Baibulo, inenso ndinkalimbikitsidwa. Ndinazindikira kuti imeneyi inali njira imene Mulungu ankandithandizira kuti ndizikhala wosangalala.” Delphine analemba mayina a anthu otchulidwa m’Baibulo amene anakhalapo ndi chisoni chifukwa choferedwa. Iye anati: “Anthu onsewa ankakonda kupemphera.” Iye anazindikiranso kuti “sungapeze mayankho amene ukufuna ngati sumawerenga Baibulo.”

Kuphunzira Baibulo kwamuthandiza Delphine kuti asamaganizire kwambiri za m’mbuyo koma zakutsogolo. Mfundo imene imamuthandiza kwambiri ndi ya pa Machitidwe 24:15 yakuti: “Kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama omwe.” Iye amakhulupirira kwambiri kuti Yehova adzaukitsa mwana wake. Delphine anati: “M’maganizo mwanga ndimamuona mwana wanga ataukitsidwa. Ndimakhulupirira kuti Yehova anakonza kale tsiku loti adzamuukitse. Ndimatha kumuona ndili naye limodzi m’munda wathu wamaluwa ndikusangalala kwambiri ngati mmene zinalili patsiku lomwe anabadwa.”

^ ndime 4 Zinthu zongomvetserazi zimapezeka pa webusaiti yathu ya jw.org.

Baibulo lingakuthandizeni kwambiri ngakhale pa nthawi ya mavuto