KODI BAIBULO NDI LOTHANDIZABE MASIKU ANO?

Popeza masiku ano anthu amagwiritsa ntchito kwambiri intaneti kapena njira zina zamakono pofufuza zimene akufuna, kodi Baibulo ndi lothandizabe kapena mfundo zake n’zachikale? Baibulo limanena kuti:

“Malemba onse anauziridwa ndi Mulungu, ndipo ndi opindulitsa.”​—2 Timoteyo 3:16.

Nsanja ya Olonda iyi ikufotokoza umboni wosonyeza kuti zimene Baibulo limanena kuti lingatithandize pa mbali iliyonse ya moyo wathu ndi zoona.