Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Nsanja ya Olonda  |  Na. 1 2016

Kodi Baibulo Limanena Zotani?

Kodi Baibulo Limanena Zotani?

Kodi chimachitika n’chiyani munthu akamwalira?

ANTHU ENA AMAKHULUPIRIRA kuti munthu akamwalira amakabadwanso kwinakwake ngati nyama kapena chinthu chinachake. Pamene ena amakhulupirira kuti munthu akafa, ndiye kuti zake zathera pomwepo. Nanga inuyo mumakhulupirira zotani?

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

“Akufa sadziwa chilichonse.” (Mlaliki 9:5) Choncho munthu akamwalira, ndiye kuti kulibenso.

MFUNDO ZINANSO ZOMWE TIKUPHUNZIRA M’BAIBULO

  • Adamu atamwalira anabwereranso kufumbi. (Genesis 2:7; 3:19) Masiku anonso anthu onse amene amamwalira, amabwerera kufumbi.—Mlaliki 3:19, 20.

  • Anthu amene amwalira amakhala kuti amasuka ku machimo awo. (Aroma 6:7) Umenewu ndi umboni wakuti munthu akamwalira, sapita kwinakwake kukalangidwa chifukwa cha machimo amene anachita.

Kodi anthu amene anamwalira adzakhalanso ndi moyo?

KODI MUNGAYANKHE KUTI . . .

  • Inde

  • Ayi

  • Mwina

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

“Kudzakhala kuuka.”—Machitidwe 24:15.

MFUNDO ZINANSO ZOMWE TIKUPHUNZIRA M’BAIBULO

 

Onaninso

Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?

Kodi Munthu Akafa Amapita Kuti?

Werengani nkhaniyi kuti mumve zimene Baibulo limanena zokhudza kumene kuli akufa komanso chifukwa chake timafa.

GALAMUKANI!

Kodi Munthu Akamwalira Amapita Kuti?

Kodi n’chiyani chimachitika munthu akamwalira? Kodi pali chiyembekezo choti tingadzaonanenso ndi okondedwa anthu amene anamwalira? Werengani nkhaniyi kuti mudziwe zimene Baibulo limanena.