Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

Kodi mipukutu inkapangidwa bwanji, nanga ankaigwiritsa ntchito bwanji?

Mipukutu ya buku la Esitere yopangidwa ndi chikopa komanso pepala ya m’ma 1700

Buku la Uthenga Wabwino wa Luka limanena kuti Yesu anapatsidwa mpukutu wa Yesaya kuti awerenge. Atapatsidwa mpukutuwo anaufutukula ndipo atamaliza kuwerenga anaupinda. Nayenso Yohane ananena kuti sanakwanitse kulemba mumpukutu wake zozizwitsa zonse zimene Yesu anachita.—Luka 4:16-20; Yohane 20:30; 21:25.

Koma kodi mipukutu inkapangidwa bwanji? Anthu ankagwiritsa ntchito zikopa, mapepala opangidwa ndi gumbwa komanso opangidwa ndi zinthu zina. Ndiyeno kuti apange mpukutu, ankalumikiza zikopa kapena mapepalawa n’kupanga chinthu chachitali. Kenako ankalembapo zimene akufuna, n’kukulunga mpukutuwo kumtengo. Mbali imene alembayo inkakhala mkati ndipo ankalembamo ngati mmene timachitira tikamalemba m’kope. Mpukutuwo ukakhala wautali kwambiri, unkakhala ndi timitengo tiwiri, kena kumayambiriro, kena kumapeto. Ndiye munthu akamawerenga, ankagwira timitengoto n’kumafutukula ndi dzanja limodzi, kwinaku akupinda ndi dzanja linali mpaka atafika pamene akufuna kuwerengapo.

Buku lina linati: “Nthawi zambiri mpukutu unkakhala wautali mamita 10 ndipo anthu ankatha kulembapo zinthu zambiri. Koma ukapindidwa sunkavuta kunyamula.” (The Anchor Bible Dictionary) Mwachitsanzo, buku la Uthenga Wabwino wa Luka linali lalitali mamita 9.5. Ndiye pofuna kuti mipukutuyi ikhale yolimba komanso yokongola, nthawi zina ankaidula, kuipenta komanso kuikhula ndi mwala m’mbali mwake kuti mukhale mosalala.

Kodi “ansembe aakulu” omwe amatchulidwa m’Malemba Achigiriki Achikhristu anali ndani?

Kungoyambira pamene Mulungu anasankha ansembe ku Isiraeli, munthu mmodzi yekha ndi amene ankakhala mkulu wa ansembe. (Numeri 35:25) Aroni ndi amene anali woyamba kupatsidwa udindowu. Kungochokera nthawi imeneyo, mkulu wa ansembe akamwalira, udindowu unkaperekedwa kwa mwana wamwamuna yemwe anali wamkulu m’banja la Aroni. (Ekisodo 29:9) Ana ambiri a Aroni anali ansembe, koma ndi ochepa amene anadzakhala akulu ansembe.

Ndiyeno mafumu a mitundu ina atayamba kulamulira Aisiraeli, ankachotsa komanso kuika pampando akulu a ansembe achiyuda nthawi iliyonse imene afuna. Komabe anthu omwe ankasankhidwawo ankakhala ochokera m’mabanja ena olemekezeka ndipo nthawi zambiri ankachokera m’banja la Aroni. Mkulu wa ansembe ankakhala m’modzi ndipo ankayang’anira ansembe onse. Koma panalinso “ansembe aakulu” omwe ankayang’anira magulu a ansembe ena. N’kutheka kuti m’gulu la ansembe aakuluwa, munali anthu ena amene anali atsogoleri a magulu 24 a ansembe a pakachisi. Munalinso anthu otchuka ochokera m’banja la mkulu wa ansembe komanso anthu ena omwe anachotsedwa pa udindo wawo ngati mkulu wa ansembe monga Anasi.—1 Mbiri 24:1-19; Mateyu 2:4; Maliko 8:31; Machitidwe 4:6.