Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Nsanja ya Olonda  |  Na. 4 2016

Kodi Zimene Mumakhulupirira Zimagwirizana Ndi Zimene Baibulo Limaphunzitsa

Kodi Zimene Mumakhulupirira Zimagwirizana Ndi Zimene Baibulo Limaphunzitsa

KODI ndinu Mkhristu? Ngati ndi choncho, dziwani kuti simuli nokha. Padziko lonse pali anthu oposa 2 biliyoni omwe amati amatsatira Khristu, ndipo izi zikusonyeza kuti pafupifupi munthu mmodzi pa atatu alionse, ndi Mkhristu. Masiku ano pali zipembedzo zambiri zachikhristu, koma zimasiyana pa nkhani ya zikhulupiriro. Choncho zimene mumakhulupirira zingasiyane ndi zomwe anthu ena omwe amati ndi Akhristu amakhulupirira. Kodi kukhulupirira zilizonse kuli ndi vuto? Inde, chifukwa Akhristu amayenera kutsatira mfundo zopezeka m’Baibulo.

Anthu omwe ankatsatira Yesu Khristu anayamba kudziwika kuti “Akhristu.” (Machitidwe 11:26) Iwo sankadziwika ndi maina ena chifukwa panali chikhulupiriro chimodzi chokha chachikhristu. Popeza kuti Yesu Khristu ndi yemwe anayambitsa Chikhristu, Akhristu onse ankatsatira malangizo komanso zimene iye ankawaphunzitsa. Kodi zimene amaphunzitsa kutchalitchi kwanu zimagwirizana ndi zimene Khristu ankaphunzitsa, komanso zomwe otsatira ake oyambirira ankakhulupirira? Kodi mungadziwe bwanji ngati zimagwirizana? Njira yabwino kwambiri n’kudziwa zimene Baibulo limanena.

 Taganizirani izi: Yesu Khristu ankalemekeza kwambiri Malemba chifukwa ndi Mawu a Mulungu. Iye ankadana ndi anthu omwe ankalimbikitsa miyambo ya anthu m’malo mophunzitsa mfundo za m’Baibulo. (Maliko 7:9-13) Choncho tinganene kuti otsatira enieni a Yesu amayenera kutenga zikhulupiriro zawo m’Baibulo. Ndiyetu Mkhristu aliyense ayenera kudzifunsa kuti, ‘Kodi zimene amaphunzitsa kutchalitchi kwathu zimagwirizana ndi zimene Baibulo limanena?’ Kuti muyankhe funsoli, mungachite bwino kuyerekezera zimene mumaphunzira ku tchalitchi kwanuko ndi zimene Baibulo limanena.

Yesu ananena kuti tiyenera kulambira Mulungu m’choonadi ndipo choonadi chimenechi chimapezeka m’Baibulo. (Yohane 4:24; 17:17) Nayenso mtumwi Paulo ananena kuti tidzapulumuka ngati timadziwa “choonadi molondola.” (1 Timoteyo 2:4) Choncho zimene timakhulupirira ziyenera kugwirizana ndi mfundo zolondola za m’Baibulo. Zimenezitu n’zofunika kwambiri chifukwa kupanda kutero sitingadzapulumuke.

KODI ZIMENE TIMAKHULUPIRIRA TINGAZIYEREKEZERE BWANJI NDI BAIBULO?

Tikukupemphani kuti muwerenge mafunso 6 amene ali m’nkhaniyi komanso muone mmene Baibulo likuyankhira mafunsowo. Muwerenge mavesi amene aikidwawo ndipo muone ngati akugwirizana ndi mayankho amene ali pansi pa mafunsowo. Kenako mudzifunse kuti, ‘Kodi zimene ndimaphunzira kutchalitchi kwathu zikugwirizana ndi zimene Baibulo likunenazi?’

Mafunso komanso mayankho omwe ali m’nkhaniyi akuthandizani kwambiri. Kodi mukufuna kuyerekezera zinanso zimene mumaphunzira kutchalitchi kwanu ndi zomwe Baibulo limanena? A Mboni za Yehova akhoza kukuthandizani kuti mudziwe mfundo zolondola za m’Baibulo. Mungachite bwino kupempha wa Mboni za Yehova kuti aziphunzira nanu Baibulo kwaulere. Mukhozanso kupita pawebusaiti yathu ya jw.org/ny.