Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Nsanja ya Olonda  |  Na. 4 2016

Kodi Baibulo Limanena Zotani?

Kodi Baibulo Limanena Zotani?

Kodi anthu ndi amene anayambitsa kupembedza?

ANTHU ENA AMAKHULUPIRIRA kuti anthu anayambitsa okha zoti azipembedza. Ena amakhulupirira kuti Mulungu amagwiritsa ntchito chipembedzo pofuna kuthandiza anthu kuti akhale naye pa ubwenzi. Kodi inuyo mukuganiza bwanji?

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Pali “kupembedza koyera ndi kosaipitsidwa kwa Mulungu ndi Atate wathu.” (Yakobo 1:27) Mfundoyi ikusonyeza kuti pali chipembedzo choona chimene Mulungu anayambitsa.

MFUNDO ZINANSO ZOMWE BAIBULO LIMANENA

  • Mulungu amasangalala ndi chipembedzo chimene chimaphunzitsa mfundo za m’Baibulo.Yohane 4:23, 24.

  • Zipembedzo zimene zimaphunzitsa mfundo za anthu n’zosathandiza.Maliko 7:7, 8.

Kodi munthu ayenera kukhala m’chipembedzo chinachake?

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

  • Inde

  • Ayi

  • Mwina

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

“Tiyeni tiganizirane kuti tilimbikitsane pa chikondi ndi ntchito zabwino. Tisaleke kusonkhana pamodzi.” (Aheberi 10:24, 25) Choncho Mulungu amafuna kuti anthu amene amamulambira azisonkhana pamodzi mogwirizana.

MFUNDO ZINANSO ZOMWE BAIBULO LIMANENA

  • Anthu omwe amalambira Mulungu mogwirizana amayenera kukhulupirira mfundo zofanana.1 Akorinto 1:10, 11.

  • Anthu a m’chipembedzo chimene Mulungu amavomereza ndi ogwirizana padziko lonse.1 Petulo 2:17.