Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Galamukani!  |  Na. 4 2016

 NKHANI YA PACHIKUTO | KODI N’ZOTHEKA KUSINTHA ZOMWE MUNAZOLOWERA?

2 Muzichita Zinthu Zomwe Zingakuthandizeni Kukwaniritsa Zolinga Zanu

2 Muzichita Zinthu Zomwe Zingakuthandizeni Kukwaniritsa Zolinga Zanu
  • Munanenetsa kuti simudzadyanso zakudya zonenepetsa koma chifukwa choti mwaona kanyenya, kamtima kali dyokodyoko moti mwalephera kuugwira mtima.

  • Munasankha kuti musiye kusuta fodya koma mnzanu wina akukupatsani ndudu ngakhale kuti akudziwa zoti mukufuna kusiya.

  • Munakonza zoti lero muchite masewera olimbitsa thupi koma mukugwa ulesi kuti muyang’ane nsapato zothamangira.

Zochitika zonsezi zikusonyeza kuti anthufe nthawi zina tingalephere kukwaniritsa zolinga zathu zofuna kuchita zinthu zabwino. Zimenezi zingachitike chifukwa malo komanso anthu amene timacheza nawo.

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Wochenjera ndi amene amati akaona tsoka amabisala, koma anthu osadziwa zinthu amangopitabe ndipo amalangidwa.”Miyambo 22:3.

Kutsatira mfundo ya m’Baibuloyi kungatithandize kupewa zinthu zomwe zingatilepheretse kukwaniritsa zolinga zathu zabwino. (2 Timoteyo 2:22) Choncho tingachite bwino kumayesetsa kuchita zinthu zomwe zingatithandize kukwaniritsa zolinga zathu.

Muzidziikira mfundo zokhwima pa zinthu zomwe mukufuna kusiya ndiponso muzidziikira mfundo zosavuta kutsatira pa zinthu zabwino zomwe mukufuna kumachita.

ZIMENE MUNGACHITE

  • Muzidziikira mfundo zokhwima pa zinthu zomwe mukufuna kusiya. Mwachitsanzo, ngati mukufuna kusiya kudya zakudya zonenepetsa, musamazigule n’komwe. Mukatero, sizingakuvuteni kuzipewa.

  • Muzidziikira mfundo zosavuta kutsatira pa zinthu zabwino zomwe mukufuna kumachita. Mwachitsanzo, ngati mukufuna kumachita masewera olimbitsa thupi m’mawa uliwonse mukangodzuka, muzikonzeratu zovala zochitira masewerawo madzulo musanagone. Zimenezi zingakuthandizeni kuti musavutike kuzolowera.

  • Muzisankha mwanzeru anthu ocheza nawo. Anthufe timakonda kutengera zochita za anzathu. (1 Akorinto 15:33) Ndiyetu ndi nzeru kusiya kucheza ndi anthu omwe angatilimbikitse kuchita zinthu zoipa, n’kuyamba kucheza ndi anthu omwe angatithandize kukhala ndi makhalidwe bwino.