Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

GALAMUKANI! Na. 3 2017 | Kodi Baibulo Linachokeradi kwa Mulungu?

Kodi Baibulo linachokeradi kwa Mulungu kapena mumaona kuti ndi buku lomwe munangolembedwa maganizo a anthu?

Galamukani! iyi ikusonyeza maumboni atatu omwe amatitsimikizira kuti Baibulo linachokeradi kwa Mulungu.

 

NKHANI YAPACHIKUTO

Kodi Baibulo ‘Linauziridwadi Ndi Mulungu’?

Anthu ena amaona kuti mwina n’kutheka kuti Baibulo linachokeradi kwa Mulungu. Pomwe ena amaona kuti Baibulo ndi buku lanthano, longofotokoza mbiri ya anthu akale komanso lolembedwa ndi anthu.

NKHANI YAPACHIKUTO

Baibulo Limanena Zinthu Molondola

Baibulo linafotokoza kalekale zinthu zosiyanasiyana za m’chilengedwe asayansi asanazitulukire n’komwe. Linaneneratunso za kukhalapo ndi kugwa kwa maulamuliro akuluakulu padziko lonse ndiponso lili ndi mayankho ogwira mtima a mafunso ofunika kwambiri.

MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA

Kodi Kuphunzitsa Ana Ntchito Zapakhomo N’kothandiza Bwanji?

Kodi makolo zimakuvutani kuphunzitsa ana anu ntchito zapakhomo? Ngati ndi choncho, werengani nkhaniyi kuti mudziwe mmene kupatsa ana ntchitozi kumawathandizira kudziwa udindo wawo komanso kukhala osangalala.

Kodi Mumadziwa Kuti Tili ndi Mitsempha Ina Imene Imagwira Ntchito Ngati Ubongo?

Timitsempha totumiza mauthengati timapezeka m’mimba. Koma kodi timagwira ntchito yanji?

KUCHEZA NDI ANTHU

Katswiri Wopanga Mapulogalamu a Pakompyuta Akufotokoza za Chikhulupiriro Chake

Pamene a Fan Yu ankayamba kuphunzira za masamu n’kuti akukhulupirira kuti zamoyo zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina. Panopo a Fan Yu amakhulupirira kuti zamoyo zinachita kulengedwa ndi Mulungu. N’chifukwa chiyani amakhulupirira zimenezi?

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Angelo

Angelo amaonetsedwa m’mafilimu ndipo zithunzi zawo zimapezekanso m’mabuku ndi m’zinthu zina zopangidwa mwaluso. Kodi Malemba amanena zotani zokhudza angelowo?

KODI ZINANGOCHITIKA ZOKHA?

Ubweya wa Katumbu

Nyama zambiri zam’madzi zimakhala ndi mafuta ambiri pansi pa khungu lake, omwe amathandiza kuti zizimva kutentha. Koma katumbu ali ndi ubweya wambiri womwe umamuthandiza kuti azimva kutentha.

Zina zimene zili pawebusaiti

Kodi Analemba Baibulo Ndi Ndani?

Ngati Baibulo linalembedwa ndi anthu, kodi n’zomveka kunena kuti ndi Mawu a Mulungu? Kodi m’Baibulo muli mawu a ndani?