ZIMENE ZIMACHITIKA

Zolinga ndi zinthu zomwe mumafuna mudzazikwaniritse. Mumafunika kukonzekera bwino, kusintha zina ndi zina komanso kuchita khama kuti mudzakwaniritse zolingazo.

Zolinga zimakhala zosiyanasiyana. Zina zimatenga nthawi yochepa, mwina masiku kapena milungu yochepa kuti zitheke. Pamene zina zimatenga nthawi yaitali, mwina miyezi kapenanso zaka. Nthawi zambiri timafunika kukwaniritsa kaye zolinga zing’onozing’ono kuti tidzakwaniritse zolinga zikuluzikulu.

N’CHIFUKWA CHIYANI KUGANIZIRA NKHANIYI N’KOFUNIKA?

Mukakwaniritsa zolinga zanu, mumalimba mtima. Zimathandizanso kuti anzanu azikudalirani komanso mumakhala osangalala.

Kulimba mtima: Mukakwaniritsa zolinga zanu zing’onozing’ono mumalimba mtima kuti mukhozanso kukwaniritsa zolinga zanu zazikulu. Komanso simungagonje mukamakumana ndi mavuto. Mwachitsanzo, simungalole kuti anzanu akukakamizeni kuchita zinthu zolakwika.

Anzanu: Anthu ambiri amagwirizana ndi anthu amene amakhala ndi zolinga komanso amene amayesetsa kukwaniritsa zolingazo. Komanso mukamathandizana ndi munthu wina pokwaniritsa cholinga chanu, mumayamba kugwirizana naye kwambiri.

Kukhala osangalala: Zolinga zimene munali nazo zikatheka, mumamva bwino mumtima.

Christopher ananena kuti: “Ndimakonda kudziikira zolinga zoti ndizikwaniritse. Zimenezi zimandithandiza kuti ndisamasowe chochita. Ndipo ukakwaniritsa cholinga chako umamva bwino kwambiri. Mumtima umangoti, ‘Ndimafuna zija zatheka.’”

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Woyang’ana mphepo sadzabzala mbewu, ndipo woyang’ana mitambo sadzakolola.”​—Mlaliki 11:4.

ZIMENE MUNGACHITE

Mungagwiritse ntchito njira zili m’munsizi kuti mukwaniritse zolinga zanu.

Zolinga: Lembani zolinga zomwe mukufuna kuzikwaniritsa. Kenako sankhani zolinga zomwe mukufuna kuzikwaniritsa koyambirira, kachiwiri, kachitatu mpaka zonse zitatheka.

Konzani pulani. Pa cholinga chilichonse, chitani izi:

  • Lembani nthawi imene mukufuna kudzakwaniritsa cholingacho.

  • Lembani njira zomwe mungatsatire kuti mukwaniritse cholinga chanu.

  • Konzekerani mavuto omwe mungadzakumane nawo komanso zomwe mungadzachite.

Yambani mwamsanga. Musadikire kuti zonse zikhale m’malo kuti muyambepo. Mwina mungadzifunse kuti, ‘Kodi ndi chinthu chiti chomwe ndingayambirire kuchita?’ Mukapeza poyambira, yambanipo. Muzilemba mmene zonse zikuyendera komanso njira zimene mwatsatira.

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Zolinga za munthu wakhama zimam’pindulira.”​—Miyambo 21:5.