Masiku ano mafilimu ndi mapulogalamu a pa TV ambiri amasonyeza anthu akuchita zamatsenga, ufiti komanso anthu ouka kumanda akudzayamwa magazi a anthu.

Kodi mukuganiza bwanji? Kodi pali vuto lililonse ngati munthu amaonera mafilimu ndi mapulogalamu otero?

Galamukani! iyi ikufotokoza zimene zimachititsa kuti anthu ambiri azichita chidwi ndi nkhani zamatsenga. Ikufotokozanso kuopsa kochita zimenezi.