PULOFESA Yan-Der Hsuuw wapayunivesite ina ya ku Taiwan, ndi mkulu woona za kafukufuku wa mmene ana osabadwa amakulira m’mimba mwa mayi awo. Poyamba ankakhulupirira kuti zamoyo zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina. Koma atakhala katswiri pa ntchito yakeyi anasintha maganizo. Iye anafotokozera mtolankhani wa Galamukani! zifukwa zake.

Tiuzeni mwachidule za mbiri yanu.

Ndinabadwa mu 1966 ndipo ndinakulira ku Taiwan. Makolo anga ankatsatira zikhulupiriro za chipembedzo cha Chitao komanso Chibuda. Tinkalambira makolo akale ndi zifaniziro koma sitinkakhulupirira kuti kuli Mlengi.

N’chifukwa chiyani munasankha kuphunzira zokhudza zinthu zamoyo?

Ndili mwana, ndinkakonda kusamalira ziweto ndipo ndinkafuna nditaphunzira mmene ndingathandizire nyama komanso anthu amene akuvutika ndi matenda. Choncho ndinayamba kuphunzira za vetenale ndipo kenako ndinaphunzira zokhudza mmene ana osabadwa amakulira. Ndinkaganiza kuti zimenezi zindithandiza kumvetsa mmene moyo unayambira.

Poyamba munkakhulupirira kuti zamoyo zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina. Mungatiuze chifukwa chake?

Mapulofesa ankatiphunzitsa kuti zamoyo zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina ndipo ankanena kuti pali umboni wa zimenezi. Choncho ndinayamba kuzikhulupirira.

Ndiyeno n’chiyani chinakupangitsani kuti muyambe kuwerenga Baibulo?

Panali zinthu ziwiri. Choyamba ndinkaona kuti, pa milungu yambirimbiri imene anthu amalambira payenera kukhala Mulungu mmodzi wamkulu kuposa inayo. Ndiye ndinkafuna kumudziwa. Chachiwiri, ndinkadziwa kuti pali anthu ambiri amene amakhulupirira Baibulo. Choncho ndinkafuna kudziwa zambiri zimene Baibulo limaphunzitsa.

Mu 1992, ndinayamba kuphunzira payunivesite ina yachikatolika ya ku Belgium. Ndiyeno ndinapita kutchalitchi cha Katolika n’kufunsa wansembe wina kuti andithandize kumvetsa Baibulo koma sanandithandize.

Ndiye n’chiyani chinakuthandizani kuti muyambe kumvetsa bwino Baibulo?

Patatha zaka ziwiri, ndinakumana ndi mayi ena a Mboni za Yehova dzina lawo a Ruth ndipo anali a ku Poland. Pa nthawiyi n’kuti ndidakali ku Belgium ndikuchita kafukufuku wokhudza zinthu zamoyo. A Ruth anaphunzira Chitchainizi n’cholinga choti azithandiza ophunzira apayunivesite amene ankafuna kuphunzira za Mulungu. Nditakumana nawo ndinasangalala kwambiri chifukwa ndinali nditapemphera kuti munthu wina andithandize kumvetsa Baibulo.

A Ruth anandiuza umboni wa m’Malemba wosonyeza kuti ngakhale kuti Baibulo si buku la sayansi, silitsutsana ndi sayansi. Mwachitsanzo, lemba la Salimo 139:16 limati: “Maso anu anandiona pamene ndinali mluza, ndipo ziwalo zanga zonse zinalembedwa m’buku lanu. M’bukumo munalembamo za masiku amene zinapangidwa koma panalibe ngakhale chiwalo chimodzi chimene chinali chitapangidwa.” Davide anafotokoza mawuwa mwandakatulo, pamene ankapemphera kwa Mulungu. Ndipotu zimene ananenazi ndi zoona. Ndikutero chifukwa chakuti mayi akangokhala woyembekezera, malangizo okhudza ziwalo za mwanayo amakhala alipo kale ngakhale kuti ziwalozo zimakhala zisanapangidwe. Nditazindikira kuti Baibulo ndi lolondola ndinayamba kukhulupirira kuti ndi Mawu a Mulungu. Ndinayambanso kuona kuti pali Mulungu mmodzi yekha woona ndipo dzina lake ndi Yehova. 1

 N’chiyani chinachititsa kuti muyambe kukhulupirira zoti Mulungu ndi amene analenga zamoyo?

Asayansi akamapanga kafukufuku amafuna kudziwa zoona pa nkhani inayake, osati kungopeza mfundo zosonyeza kuti zimene ena anapeza kale ndi zoona. Choncho zimene ndinapeza pa kafukufuku wokhudza mmene mwana wosabadwa amakulira, zinachititsa kuti ndiyambe kukhulupirira kuti zamoyo zinachita kulengedwa. Mwachitsanzo, anthu amene amapanga zinthu kumafakitale amaonetsetsa kuti zinthuzo zikuikidwa m’malo ake, m’njira yoyenera ndiponso pa nthawi yake. Ndi mmene zimakhaliranso mwana akamakula m’mimba mwa mayi ake, koma kungoti zimachitika modabwitsa kwambiri kuposa mmene zimachitikira m’mafakitale.

Komatu zonse zimayamba ndi selo limodzi, si choncho?

Eee. Kenako seloli limagawanika n’kupanga maselo awiri ndipo maselo amenewo amapitirizabe kugawanika. Ndipo chiwerengero cha maselowa chimawonjezeka kawiri pakadutsa maola 12 kapena 24 alionse. Zimenezi zikangoyambika, maselowo amagawanika m’njira yoti ayambe kupanga ziwalo zosiyanasiyana. 2 Kuti mwana apangike pamafunika mitundu pafupifupi 200 ya maselo. Ena mwa maselo amenewa ndi maselo a magazi, a mafupa komanso a mitsempha.

Zimene ndinapeza zokhudza mmene mwana wosabadwa amakulira, zinachititsa kuti ndiyambe kukhulupirira kuti zamoyo zinachita kulengedwa

Maselowa amagawanika n’kupanga maselo oyenera pamalo oyenera ndiponso pa nthawi yoyenera. Kenako amadzapanga miyendo, manja komanso ziwalo zina. Choncho malangizo onse okhudza mmene mwana adzakhalire amakhala kuti analembedweratu mu DNA. Izitu n’zogometsa kwambiri ndipo palibe katswiri amene angakwanitse kuchita zimenezi. Ndikaganizira zonsezi ndimaona kuti Mulungu ndi ndiye analenga zamoyo.

N’chifukwa chiyani munasankha kuti mukhale wa Mboni za Yehova?

M’mawu amodzi ndingati, chikondi. Yesu Khristu anati: “Onse adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga, ngati mukukondana.” (Yohane 13:35) Munthu akakhala ndi chikondi choterechi sakhala watsankho. Akhristu amakondana mosaganizira za dziko limene munthu amachokera, chikhalidwe chake kapena mtundu wake. Nditayamba kusonkhana ndi a Mboni ndinaona kuti amakondana kwambiri.

^ 2. Pulofesa Yan-Der Hsuuw anasiya kugwira ntchito zina zokhudzana ndi mmene ana osabadwa amakulira ataona kuti zikusemphana ndi zimene akuphunzira m’Baibulo.