KODI MUNADZIFUNSAPO KUTI:

  • Ndingatani kuti banja langa lizisangalala?

  • Ndingatani kuti ndipeze anzanga abwino komanso kuti ena azindiona kuti ndine munthu wabwino?

  • Kodi anthu amene anamwalira adzakhalanso ndi moyo?

  • Kodi mavuto amene timakumana nawowa adzathadi?

  • Kodi anthu sadzaliwonongeratu dziko lapansili?

  • Kodi zipembedzo zonse zimathandiza anthu kudziwa Mulungu woona?

KUTI MUPEZE MAYANKHO A MAFUNSOWA KOMANSO ENA

Pitani pawebusaiti yathu ya jw.org yomwe ikupezeka m’zinenero zoposa 900. Pamalowa mukhoza kupeza mfundo zothandiza kwambiri pa nkhani zosiyanasiyana.

Mungapezeponso mavidiyo a anthu osiyanasiyana omwe anayamba kusangalala ataphunzira Baibulo ndipo sakunong’oneza bondo. Ena mwa anthuwa ankagwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo ndipo ena anali akaidi. Enanso ndi ophunzira kwambiri kuphatikizaponso akatswiri a zasayansi.

Pa jw.org/ny mukhoza kuwerenga kapena kupanga dawunilodi Mabaibulo komanso mabuku ndi magazini osiyanasiyana, kwaulere. Nkhani zina zomwe mungazipeze pawebusaiti ndi izi: