KODI muli wachinyamata munali ndi zolinga ziti? Mwina munkafuna kukhala pa banja, kukhala ndi luso linalake kapena kugwira ntchito inayake. Koma nthawi zina zinthu siziyenda mmene tinkaganizira. Mavuto ena angasokoneze kwambiri moyo wathu. Izi n’zimene zinachitikira anthu atatu amene akuoneka m’munsimu.

  • Woyamba ndi mayi wina wa ku Germany dzina lake Anja. Iye anapezeka ndi khansa ali ndi zaka 21 ndipo panopa amangokhala pakhomo.

  • Wachiwiri ndi mayi wina wa ku United States dzina lake Delina. Iye amadwaladwala komanso amasamalira azichimwene ake atatu olumala. Wachitatu ndi bambo wina wa ku Canada dzina lake Gregory. Iye amavutika kwambiri ndi nkhawa.

  • Koma onsewa amadziwa zochita ndi mavuto awo. Kodi iwo amatani?

Mwambi wina wa m’Baibulo umati: “Ukafooka pa tsiku la masautso, mphamvu zako zidzakhala zochepa.” (Miyambo 24:10) Choncho nkhani yagona pa mmene timaonera mavuto athu. Anthu ena akakumana ndi mavuto amangogwa ulesi. Koma anthu amene amaona mavuto awo moyenera savutika kudziwa zochita.

Tiyeni tione zimene Anja, Delina ndi Gregory amachita.