KODI mchenga umachokera kuti? Mchenga umapangidwa m’njira zosiyanasiyana. Koma pali njira ina yochititsa chidwi kwambiri imene tikambirane m’nkhaniyi.

Pali nsomba zinazake zomwe zimapanga mchenga. Nsombazi zimakhala m’nyanja zikuluzikulu ndipo zimadya zomera zina za pansi pa nyanja zomwe zikafa zimauma ngati miyala. Nsombazi zikadya zinthu zimenezi, zimagaya zakudyazo ndipo zosafunika m’thupi zimatuluka ngati mchenga. Nsombazi zimakwanitsa kudya zomerazi chifukwa zili ndi nsagwada komanso mano olimba kwambiri. Mitundu ina ya nsombazi imatha kukhala ndi moyo zaka 20, mano ake adakali olimba.

M’malo ena, mchenga umene nsombazi zimapanga umakhala wambiri kuposa umene umapangidwa m’njira zina. Akatswiri ena amati nsomba imodzi imatha kupanga makilogalamu pafupifupi 100 a mchenga pa chaka.

Mtundu wina wa nsomba zopanga mchenga

Nsombazi zimagwiranso ntchito yofunika kwambiri. Zikamadya zomera zakufa zomwe zimakhala ndi ndere, zimathandiza kuti malowo akhale oyera. Koma pamalo pamene palibe nsombazi komanso zinthu zina zomwe zimadya zomera, zomera za pamalowo sizikula bwino chifukwa pamakhala ndere ndi ziyangoyango. Buku lina linanena kuti: “Anthu ena amanena kuti zikanakhala kuti palibe nsombazi, bwenzi zomera za m’nyanjazi zitatha.”—Reef Life.

Usiku nsombazi zimagona mokwanira ndipo izi ndi zimene zimathandiza kuti nsombazi zizitha kupanga mchenga komanso kuyeretsa pamalo omwe pamakhala zomera za m’madzi. Komabe usiku ndi nthawi yoopsa chifukwa kumakhala nsomba zina zikuluzikulu zomwe zimafuna kugwira nsombazi. Choncho pofuna kudziteteza, nsombazi zimagona pansi pa miyala. Komabe nthawi zina zimagwidwa ndi nsomba zikuluzikuluzo.

Kuti zisagwidwe, nsombazi zimadzikuta ndi zinthu zinazake zonunkha. Zinthuzi ndi zangati mamina ndipo zimakhala zoonekera mkati. Asayansi amati zinthu zimenezi zimatetezanso nsombazi kuti zisagwidwe ndi nsomba zikuluzikulu.

Nsombazi zimaoneka patali komanso ndi zokongola kwambiri pa zinthu zonse zomwe zimakhala m’zomera za m’nyanja. Nsombazi zikakhala zazing’ono, zimakhala ndi mitundu yosiyanasiyana komanso yokongola kwambiri, koma zikamakula zimasintha. Komanso nsomba za mtunduwu zomwe zimakhala m’madera omwe anthu sazigwira kwambiri, zimazolowerana ndi anthu ndipo sizithawa. Choncho n’zosavuta kufufuza ndi kuphunzira zambiri zokhudza nsombazi.

Akatswiri ambiri ofufuza zinthu za m’nyanja amasangalala kwabasi akamaona komanso kumvetsera nsombazi zikudya zomera za m’nyanja. Zimene nsombazi zimachita, zimathandiza kuti malo amene zimakhala akhale osangalatsa kwa zinthu zina za m’madzi komanso kwa anthufe.