Padziko lonse, ku Asia n’kumene kuli anthu ambiri. Mwachitsanzo, ku China ndi ku India kokha, kuli anthu pafupifupi hafu ya chiwerengero cha anthu padziko lonse. Kodi mayiko a ku Asia amakumana ndi mavuto otani pa nkhani ya maphunziro ndi kuteteza nzika zawo?

Makolo Ayenera Kuphunzitsa Ana awo Zokhudza Kugonana

Akatswiri oona za malamulo ku China ananena kuti ana amene saphunzitsidwa ndi makolo awo zokhudza kugonana adakali aang’ono, nthawi zambiri ndi amene amachitidwa chipongwe ndi anthu ogona ana. Mwachitsanzo, pa zaka 4 zapitazi, oweruza milandu a ku China, analandira milandu 8,000 yokhudza ana amene anagwiriridwa. Pulofesa wa pa yunivesite ina ku Beijing ananena kuti, “Anthu achipongwewa amaona kuti ana ndiye osavuta kuwanyengerera komanso kuwachita chipongwe. Choncho, makolo ayenera kuphunzitsa ana awo nkhani za kugonana adakali aang’ono, kuti awateteze kwa anthu oterewa.”

ZIMENE BAIBULO LIMANENA: Makolo anzeru amaphunzitsa ana awo mmene angadzitetezere kwa ‘anthu onena zinthu zopotoka.’—Miyambo 2:1, 10-12.

Ana Omwe Amafa Pambuyo pa Mphepo Yamkuntho

Kafukufuku wina anasonyeza kuti chiwerengero cha ana aakazi omwe amafa ku Philippines pambuyo pa mphepo yamkuntho, chimakhala chokwera kuwirikiza ka 15 chiwerengero cha anthu omwe anafa ndi mphepo yamkunthoyo. Mwa zina, zimenezi zimachitika chifukwa choti pambuyo pa mphepo yamkuntho, ntchito zimasowa komanso ndalama zimathera kumanga nyumba zomwe zawonongeka. Chifukwa chinanso n’choti boma silimasamalira kwenikweni ana aakazi pa nkhani ya chakudya ndi mankhwala.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA: ‘Muzigawira chakudya chanu anthu anjala, ndiponso muziitanira m’nyumba zanu anthu osautsika ndi osowa pokhala. Ndimafuna kuti mukaona munthu wosavala muzimuveka.’—Yesaya 58:7.

Achikulire Ambiri a ku South Korea Amadzipha

M’chaka cha 2011, munthu mmodzi pa anthu 4 alionse amene anadzipha ku South Korea, anali wachikulire. Achikulire ake ndi azaka 65 kapena kuposa. Kafukufuku wina anasonyeza kuti zimenezi zimachitika chifukwa chakuti masiku ano achikulire sakusamalidwanso bwino ngati kale komanso chifukwa cha mavuto a zachuma. Pafupifupi hafu ya anthu achikulire a ku South Korea ndi osauka. Ndi anthu ochepa ku South Korea amene amaganiza kuti ana ali ndi udindo wosamalira makolo awo achikulire.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA: “Uzilemekeza bambo ako ndi mayi ako.”—Aefeso 6:2.