Ngakhale kuti sayansi yapita patsogolo, matenda akupitirizabe kusowetsa anthu mtendere. Komabe ambiri mwa matendawa ndi opeweka.

Padziko Lonse

Bungwe loona zaumoyo padziko lonse linanena kuti pomadzafika chaka cha 2035, anthu 24 miliyoni adzapezeka ndi matenda a khansa. Chiwerengerochi n’chokwera ndi 70 peresenti tikayerekezera ndi anthu amene akupezeka ndi khansa panopo, omwe ndi oposa 14 miliyoni. Akuganiza kuti hafu ya anthuwa adzadwala matendawa chifukwa cha kumwa mowa mwauchidakwa, kusachita masewera olimbitsa thupi, kunenepa kwambiri, kusuta fodya komanso chifukwa cha kuwala koopsa kochokera ku zipangizo zamakono ndiponso dzuwa.

Britain

Boma la Britain linachita kafukufuku wokhudza matenda omwe munthu amadwala chifukwa chodya nyama ya ng’ombe yodwala misala. Kafukufukuyu anasonyeza kuti matendawa amafalitsidwa ngati munthu walandira magazi a munthu yemwe akudwala matendawa. Phungu wina wa nyumba ya malamulo, dzina lake Andrew Miller, ananena kuti: “N’zodetsa nkhawa kwambiri kuti matendawa alibe mankhwala ndipo akhoza kufalikira mosavuta kwa anthu ambiri. Zikuoneka kuti munthu akhoza kuwatenganso ngati ataikidwa chiwalo, monga impso, cha munthu yemwe akudwala matendawa.”

Norway

Kafukufuku wina, yemwe anachitika kwa zaka 11 pakati pa anthu pafupifupi 63,000, anasonyeza kuti nthawi zambiri matenda a nkhawa ndi amene amachititsa kuti munthu adwale matenda a mtima. Bungwe lina loona za matendawa ku Europe, linanena zimene munthu wina yemwe analemba zokhudza kafukufukuyu ananena. Anati matenda a nkhawa amachititsa kuti munthu azikhala wokhumudwa zomwe zingapangitse kuti adwale matenda a mtima. Nthawi zambiri munthu wotereyu zimamuvuta kutsatira malangizo othandiza amene madokotala amuuza.

United States

Asayansi akufufuza kuopsa kwa zotsalira za ndudu zomwe zimangotayidwa paliponse m’nyumba, m’mahotela komanso m’magalimoto. Zinthu zimenezi zikakhalitsa komanso zikachuluka, zimayambitsa mavuto osiyanasiyana.