Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Galamukani!  |  February 2015

 NKHANI YA PACHIKUTO | KODI MFUNDO ZA M’BAIBULO N’ZOTHANDIZABE MASIKU ANO?

Mfundo Zake N’zothandiza Nthawi Zonse—Kusakwiya Msanga

Mfundo Zake N’zothandiza Nthawi Zonse—Kusakwiya Msanga

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Wopusa amatulutsa mkwiyo wake wonse, koma wanzeru amakhala wodekha mpaka pamapeto.”Miyambo 29:11.

“Ndimaona kuti ndinapulumuka lokumbakumba”

UBWINO WOSAKWIYA MSANGA: Titati titchule ubwino wosakwiya msanga, dzuwa likhoza kulowa. Koma ubwino wina ndi woti, munthu wosakwiya msanga amakhala ndi thanzi labwino. Baibulo limati: “Mtima wodekha ndiwo moyo wa munthu.” Limanenanso kuti: “Mtima wosangalala ndiwo mankhwala ochiritsa.” (Miyambo 14:30; 17:22) Akatswiri ambiri anapeza kuti anthu amene amakwiya pafupipafupi amakhala pa ngozi yoti angathe kudwala matenda osiyanasiyana, makamaka matenda a mtima. Komatu kusakwiya msanga sikumangothandiza munthu kukhala ndi thanzi labwino. Kumathandizanso kuti azikhala bwino ndi anthu.

Mwachitsanzo Cassius, yemwe ali ndi zaka za m’ma 30 anati: “Poyamba ndinali munthu wovuta ndipo sindinkachedwa kupsa mtima. Sindinkati ndamenyana liti ndi anthu. Komabe pansi pa mtima ndinkadziona kuti ndine munthu wachabechabe. Koma nditayamba kutsatira mfundo za m’Baibulo ndinasintha kwambiri ndipo ndinayamba kuugwira mtima. Ndinkayesetsanso kukhala wodzichepetsa komanso wokhululuka. Ndikanapanda kusintha, mwina bwenzi pano ndili kundende kapena bwenzi nditafa. Kunena zoona ndimaona kuti ndinapulumuka lokumbakumba.”

Cassius anayamba kukhululuka komanso kuugwira mtima, ena akamuputa

Onaninso

UTHENGA WABWINO WOCHOKERA KWA MULUNGU

Kodi Timapindula Bwanji ndi Mfundo za M’Baibulo?

Yesu anafotokoza chifukwa chake timafunikira malangizo komanso anatchula mfundo ziwiri za m’Baibulo zomwe ndi zofunika kwambiri pa moyo wathu.

GALAMUKANI!

Makhalidwe Abwino Angakuthandizeni Kuti Muzisangalala

Anthu ambiri amayendera mfundo yoti: ‘Palibe vuto ndi kuchita chilichonse chomwe mtima wako ukufuna, bola ngati iweyo ukuona kuti n’choyenera.’ Koma kodi ndi nzeru kutsatira mfundo imeneyi? Werengani nkhaniyi kuti muone makhalidwe ena a m’Baibulo amene angakuthandizeni.