Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

GALAMUKANI! February 2015 | Kodi Baibulo Ndi Lothandizabe Masiku Ano?

Werengani magaziniyi kuti mudziwe mfundo 4 zomwe zimasonyeza kuti Baibulo ndi lothandizabe masiku ano ngati momwe zinalili pa nthawi yomwe linkalembedwa.

NKHANI YAPACHIKUTO

Kodi Mfundo za M’Baibulo N’zothandizabe Masiku Ano?

Pamene Hilton ankachoka panyumba, makolo ake ankaganiza kuti sangasinthe. Koma mmene ankabwera patatha zaka 12 anali atasintha kwambiri moti makolo ake sanamuzindikire. N’chiyani chinamuthandiza kuti asinthe?

NKHANI YAPACHIKUTO

Mfundo Zake N’zothandiza Nthawi Zonse—Kuchita Zinthu Mwachilungamo

Raquel akanalola kuchita zachinyengo bwenzi akupeza ndalama, koma anaona kuti zimenezi zimubweretsera mavuto komanso ziwononga ubwenzi wake ndi Yehova.

NKHANI YAPACHIKUTO

Mfundo Zake N’zothandiza Nthawi Zonse—Kusakwiya Msanga

N’chiyani chinathandiza Cassius kuti aziugwira mtima?

NKHANI YAPACHIKUTO

Mfundo Zake N’zothandiza Nthawi Zonse—Kukhulupirika M’banja

Mayi wina anaphunzira kufunika kokhala wokhulupirika m’banja, banja lake litatsala pang’ono kutha. Kodi anatani kuti banja lake lisathe?

NKHANI YAPACHIKUTO

Mfundo Zake N’zothandiza Nthawi Zonse—Chikondi

Chikondi chimene chimatchulidwa m’Baibulo kawirikawiri, si chikondi cha pakati pa mwamuna ndi mkazi.

ZOCHITIKA PADZIKOLI

Nkhani Zaumoyo

Werengani nkhani za posachedwapa zimene zikusonyeza kuti maulosi a m’Baibulo onena za matenda ndi olondola.

Nzeru Zomwe Zimateteza

Kodi mawu a pa Miyambo 13:8 akuti: “Moyo wa munthu udzawomboledwa ndi chuma chake, koma munthu wosauka sadzudzulidwa,” amatanthauza chiyani?

MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA

Kodi Mungayankhe Bwanji Mwana Wanu Atakufunsani za Imfa?

Werengani nkhaniyi kuti mudziwe zinthu 4 zimene mungachite pothandiza mwana wanu kudziwa zokhudza imfa komanso mmene mungamuthandizire kupirira wachibale akamwalira.

KUCHEZA NDI ANTHU

N’chifukwa Chiyani Wansembe Anasiya Chipembedzo Chake?

Werengani nkhaniyi kuti mumve zimene Antonio Della Gatta anachita kuti adziwe Mulungu komanso azichita zimene amafuna.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Mesiya

Kodi mukudziwa kuti Baibulo linalosera kuti Mesiya adzafa asanamalize ntchito yake?

KODI ZINANGOCHITIKA ZOKHA?

Mapiko a Mbalame Opindikira M’mwamba

Potengera mapiko a mbalame, akatswiri apanga ndege zabwino kwambiri. Zimenezi zinathandiza kupulumutsa malita okwana 7,600 miliyoni a mafuta padziko lonse m’chaka chimodzi chokha.

Zina zimene zili pawebusaiti

Kupatsa N’kwabwino

Pali zambiri zimene mungachite kuti muthandize ena. Kodi mukuganiza kuti mungachite chiyani?