Pa ziganizo zili kumanjazi,

NDI CHITI CHOMWE MUKUONA KUTI NDI CHOLONDOLA?

  1. ZAMOYO ZINACHITA KUSINTHA KUCHOKERA KU ZINTHU ZINA

  2. ZAMOYO ZINACHITA KULENGEDWA

ANTHU ena angaganize kuti asayansi anganene kuti chiganizo cholondola ndi choyambacho, pomwe anthu amene amakhulupirira kuti kuli Mulungu angati cholondola ndi chachiwiricho.

Komatu si asayansi onse omwe amakhulupirira kuti zamoyo zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina.

Mfundo ndi yakuti pali anthu ambiri ophunzira kuphatikizapo a sayansi ambiri omwe amakayikira zoti zamoyo zinachita kusitha kuchokera ku zinthu zina.

Wasayansi wina dzina lake Gerard, yemwe anaphunzira zoti zinthu zamoyo zinasintha kuchokera ku zinthu zina, anati: “Polemba mayeso, ndinkalemba zoti zamoyo zinachokera ku zinthu zina. Koma sikuti ndinkazikhulupirira. Ndinkangolemba zimenezi n’cholinga choti ndikhoze.”

Koma kodi n’chifukwa chiyani asayansi ena zimawavuta kukhulupirira kuti zamoyo zinachokera ku zinthu zina? Kuti tiyankhe funsoli, choyamba tiyeni tikambirane mafunso amene amazunguza mutu akatswiri akachita kafukufuku pa nkhaniyi. Mafunso ake ndi awa: (1) Kodi moyo unayamba bwanji? (2) Kodi mitundu yosiyanasiyana ya zamoyo inachokera kuti?