Israel, Jordan ndi Palestine

Zikuoneka kuti Nyanja Yakufa ikuphwa moti chaka chilichonse ikumatsika pafupifupi ndi mita imodzi. Anthu ena akuona kuti izi zikapitirira, pofika chaka cha 2050 nyanjayi idzakhala itaumiratu. Akuluakulu a boma akufufuza njira yothetsera vutoli. Njira ina imene akuiganizira ndi yochotsa mchere m’madzi ena a m’Nyanja Yofiira n’cholinga choti anthu azigwiritsa ntchito madziwa. Mchere umene angachotsewo akuganiza zokauika m’Nyanja Yakufa pofuna kuti anthu asamagwiritse ntchito madzi a m’nyanjayi. Komabe anthu ena akuganiza kuti zimenezi zingawononge zinthu zamoyo za m’Nyanja Yakufa.

Germany

Zotsatira za kafukufuku yemwe kampani ina ya inshulansi inachita, zinasonyeza kuti pa Khirisimasi anthu ambiri amagonekedwa m’chipatala chifukwa chodwala matenda a mtima, kuposa nthawi ina iliyonse. Kampaniyi inati izi zimachitika chifukwa choti pa nthawiyi, anthu ambiri amakhala ndi nkhawa chifukwa cha nkhani zokhudza mphatso za Khirisimasi komanso zimene ayenera kuchitira achibale ndi anzawo.

Britain

Poyamba akatswiri asayansi a ku Britain ankaganiza kuti nkhono inayake ya m’madzi ya ku Iceland, yomwe inaphedwa mu 2006, inakhala ndi moyo zaka 405. Koma tsopano akatswiriwa apeza kuti nkhonoyi inakhala ndi moyo zaka 507. Izi zikusonyeza kuti nkhonoyi ndi imene yakhala ndi moyo wautali kuposa nyama iliyonse. * Nkhonoyi inafa anthu ochita kafukufuku ataiika m’firiji pamene ankapita nayo ku labotale yawo.

Latin America ndi Dera la Caribbean

Pa msonkhano womwe unachitika mumzinda wa Havana m’dziko la Cuba kumayambiriro kwa chaka cha 2014, mayiko 33 a ku America ndi dera la Caribbean anagwirizana zoti mayiko awo azidziwika kuti ndi “Dera la Mtendere.” Mayikowa anagwirizana kuti azithetsa mikangano pakati pawo popanda kumenyana. Pa msonkhanowu panali Ban Ki-moon, yemwe ndi mlembi wamkulu wa bungwe la United Nations.

^ ndime 7 Ponena kuti nkhonoyi ndi yomwe yakhala ndi moyo wautali kuposa nyama iliyonse, sitikuphatikizapo zamoyo za m’madzi, monga zotchedwa coral, zomwe zimakhala zaka masauzande ambiri.