Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Galamukani!  |  December 2014

 KUCHEZA NDI | STEPHEN TAYLOR

Katswiri wa Zachuma Akufotokoza za Chikhulupiriro Chake

Katswiri wa Zachuma Akufotokoza za Chikhulupiriro Chake

Pulofesa Stephen Taylor ndi mphunzitsi komanso wochita kafukufuku pa yunivesite ina mumzinda wa Sydney ku Australia. Iye amafufuza nkhani zokhudza chuma komanso zimene zingathandize kuti chiziyenda bwino. Mtolankhani wa Galamukani! anacheza naye kuti adziwe mmene ntchito yakeyi imakhudzira zimene amakhulupirira.

Tiuzeni za mbiri yanu.

Banja lathu linali lokonda kupemphera ndipo makolo anga anali olimbikira ntchito komanso ankayesetsa kuchita zinthu mwachilungamo. Makolo angawa ankandilimbikitsa kuti ndidzapite patali ndi sukulu, choncho nditamaliza sekondale ndinayamba kuphunzira zamalonda payunivesite inayake ya ku Wales. Koma ndinazindikira kuti ndimakonda kufufuza zinthu, choncho ndinaganiza zoyamba kuchita kafukufuku pa zinthu zosiyanasiyana.

Ndiye munayamba kuchita kafukufuku wokhudza chiyani?

Ndinkafuna kumvetsa mmene misika yogulitsa masheya imayendera. Anthu amagula ndi kugulitsa masheya m’makampani ndipo makampaniwo amagwiritsa ntchito ndalamazo poyendetsera bizinesi zawo. Ndimafufuza zinthu zomwe zimapangitsa kuti mitengo ya masheya ikwere kapena itsike.

Kodi mungatipatse chitsanzo cha zimenezi?

Makampani amafunika kupereka lipoti la phindu lomwe apeza. Anthu amene ali ndi masheya m’kampaniyo amaona malipotiwa akafuna kudziwa mmene kampaniyo ikuyendera. Koma palibe njira zabwino zomwe zinakhazikitsidwa zoti azigwiritsa ntchito popereka malipotiwa. Anthu ena amaona kuti zimenezi zimapangitsa makampani kupezerapo mwayi wochita zachinyengo pobisa phindu lenileni lomwe apeza. Ndiye kodi eni masheya angadziwe bwanji zonse zokhudza kampaniyo? Nanga ndi zinthu ziti zomwe akuluakulu a boma ayenera kudziwa kuti azionetsetsa kuti misika ya masheya ikuyenda bwino? Ine ndi anzanga tikufufuza mayankho a mafunso amenewa.

Kodi poyamba munali mpingo wanji?

Ndili mwana, ndinkapita ndi makolo anga ku tchalitchi cha Presbyterian, koma ndili mnyamata  ndinasiya kupita kutchalitchi. Ndinkakhulupirira zoti kuli Mlengi komanso zoti Baibulo ndi Mawu a Mulungu. Koma ndinkaona kuti chipembedzo sichithandiza munthu kuthetsa mavuto ake. Ndinkaonanso kuti matchalitchi ali ngati malo ochezera basi. Ndili ku Europe, ndinapita m’matchalitchi akuluakulu angapo koma ndinadabwa kuti matchalitchiwa ali ndi ndalama zambiri pomwe anthu ambiri m’dzikoli ali pa umphawi wadzaoneni. Ndinaona kuti zimenezi si zabwino ndipo ndinayamba kukayikira zochita za matchalitchi.

N’chiyani chinachititsa kuti musinthe maganizo?

Mkazi wanga, Jennifer, anayamba kuphunzira Baibulo ndi a Mboni za Yehova ndipo ankapita kumisonkhano yawo. Tsiku lina ndinaganiza zopita nawo kuti ndikaone zimene amaphunzitsa. Ndinazindikira kuti sindinkadziwa Baibulo ngakhale pang’ono ndipo zimenezi zinandidabwitsa kwabasi. Choncho ndinayamba kuphunzira Baibulo ndi a Mboni za Yehova.

Ndinachita chidwi kwambiri ndi njira imene a Mboni amagwiritsa ntchito pophunzitsa anthu Baibulo. Amafunsa funso, kupereka mfundo ndi umboni wokhudza nkhaniyo ndipo kenako mumatha kupeza yankho lolondola kuchokera pa mfundozo. Njirayi ndi imenenso ine ndimatsatira pa ntchito yanga. Choncho, mu 1999 ndinabatizidwa n’kukhala wa Mboni za Yehova. Apa n’kuti patatha zaka zingapo mkazi wanga atabatizidwa kale.

Kodi zomwe mukudziwa pa nkhani zachuma zakuthandizani kuti muzikhulupirira kwambiri Baibulo?

Ee. Mwachitsanzo m’Chilamulo chimene Mulungu anapatsa Aisiraeli akale, munali mfundo zokhudza nkhani zachuma, zomwe mpaka pano akatswiri a zachuma amalimbana nazo. Mwachitsanzo, panali lamulo loti Aisiraeli azisiya zokolola zawo zina kuti osauka azikunkha. Lamulo limeneli ndi lofanana ndi nkhani ya kukhoma msonkho komanso ya inshulansi. Panalinso lamulo loti Aisiraeli azibwereka ndalama Aisiraeli anzawo osauka popanda kulandira chiwongoladzanja. Izi zikufanana ndi mfundo yoti aliyense azikhala ndi mwayi wotenga ngongole. Lamulo lina linkauza Aisiraeli kuti pakatha zaka 50, azibweza malo kubanja lomwe linawagulitsa malowo chifukwa ndi cholowa cha banjalo. Mfundo imeneyi ndi yogwirizana ndi lamulo la masiku ano loteteza kuti munthu asalandidwe katundu. (Levitiko 19:9, 10; 25:10, 35-37; Deuteronomo 24:19-21) Malamulo amenewa ankathandiza anthu m’njira zitatu. (1) Ankawathandiza kuti asamasoweretu pogwira, (2) ankawathandiza kuti asakhale aumphawi mpaka kalekale, komanso (3) ankathandiza kuti pasamakhale kusiyana kwambiri pakati pa osauka ndi olemera. N’zochititsa chidwi kuti panatenga zaka zoposa 3,000, kuti akatswiri atulukire mfundo zangati zimenezi pa nkhani zachuma.

Baibulo limalimbikitsanso anthu kukhala ndi makhalidwe omwe ndi othandiza pa nkhani zachuma. Mwachitsanzo limaphunzitsa kuti anthu ayenera kukhala ndi makhalidwe monga kupanda chinyengo, kukhulupirika, chifundo komanso kuwolowa manja. (Deuteronomo 15:7-11; 25:15; Salimo 15) N’zochititsa chidwi kuti chifukwa cha mavuto azachuma, mabungwe ena komanso masukulu ophunzitsa kayendetsedwe ka bizinesi, anakhazikitsa mfundo zolimbikitsa anthu kuchita zabwino. Mabungwe ndi masukuluwa akulimbikitsa akuluakulu awo kuti azitsatira mfundozi. Koma ineyo ndimaona kuti mfundo za m’Baibulo zimaposa mfundo zonse zomwe anthu amakhazikitsa.

Kodi kukhala wa Mboni za Yehova kwakuthandizani bwanji?

Kuphunzira Baibulo kunali ngati kusunga chuma choti chidzandithandize m’tsogolo

Mkazi wanga amandiuza kuti ndimachita zinthu bwino kuposa kale. Poyamba ndinkaganiza kuti ndiyenera kuchita zinthu osalakwitsa chilichonse ndipo ndinali munthu wokhwimitsa zinthu. Mwina zimenezi n’zimene zinkachititsa kuti ndizichita bwino pa ntchito yanga. Koma mfundo za m’Baibulo zandithandiza kuti ndiziona zinthu moyenera. Ndikuona kuti panopa ndine munthu wosangalala ndipo banja langanso ndi losangalala. Timasangalalanso kuuza ena mfundo za m’Baibulo, zomwe ndi zothandiza kwambiri. Ndikuona kuti kuphunzira Baibulo kunali ngati kusunga chuma choti chidzandithandize m’tsogolo.