Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Galamukani!  |  December 2014

Kanyama Kakang’ono ka Maso Aakulu

Kanyama Kakang’ono ka Maso Aakulu

PALI kanyama kenakake ka ubweya wosalala komwe kamaoneka ngati changa ndipo kamapezeka ku Asia. Anthu ambiri amaona kuti kanyamaka ndi kokongola kwambiri koma ena amati kamaoneka modabwitsa. Kanyama kameneka ndi ka masentimita 12.5 basi ndipo kamalemera magalamu 114 okha. Komatu kali ndi miyendo yaitali ndi maso aakulu kwambiri osagwirizana ndi msinkhu wake.

Tiyeni tikambirane za kanyama ka mtundu umenewu komwe kamapezeka ku Philippines. Maso, makutu, manja, mapazi komanso miyendo ya kanyamaka ndi zazikulu kwambiri poyerekeza ndi thupi lake. Kalinso ndi mchira wautali. Komatu mmene kamachitira zinthu, zimachita kusonyezeratu kuti kanalengedwa mwaluso kwambiri.

MAKUTU: Kanyama kameneka kali ndi makutu opyapyala, omwe kamatha kuwapinda kapena kuwatambasula ndipo kamatha kumva ngakhale kaphokoso kapansipansi. Chifukwa choti kamamva kwambiri, kamatha kupeza chakudya chake mosavuta. Kamathanso kuzindikira zilombo monga amphaka am’tchire, zikakhala pafupi, n’kuthawa. Kanyamaka kamakonda kugwira tizilombo monga nkhululu, chiswe, zikumbu, mbalame ndi achule, ndipo kukada kamatha kumva mosavuta phokoso la tizilombo timeneti.

MANJA: Kanyamaka kali ndi manja omwe amatha kugwira mwamphamvu nthambi za mitengo. Kumapeto kwa zala zake kuli tinthu timene timapangitsa kuti kakagwira nthambi kasamaterereke. Kamathanso kugona tulo panthambi ya mtengo nthawi yaitali, osagwa. Zimenezi zimatheka chifukwa choti pansi pa mchira wake pali timabampu tomwe timachititsa kuti kamatirire panthambiyo.

 MASO: Palibenso nyama ya m’gulu loyamwitsa yomwe imakhala ndi maso aakulu osagwirizana ndi thupi lake ngati mmene zilili ndi kanyama kameneka. Ndipotu diso lililonse la kanyamaka limakhala lalikulu kuposa ubongo wake. Kanyamaka sikatha kuyendetsa maso ake moti nthawi zonse kamayang’ana kutsogolo. Komabe sikuti kamavutika kuona zinthu zomwe zili m’mbali, chifukwa kali ndi khosi lofewa kwambiri moti kamatha kutembenukira mbali zonse mosavuta.

MIYENDO: Miyendo yaitali ya kanyamaka imakathandiza kuti kazitha kudumpha n’kukagwera pamtunda wa mamita 6. Izi n’zodabwitsa kwambiri poti paja kanyamaka n’kakafupi kwambiri. Kakafuna kugwira tizilombo, kamadumpha katatambasula zala zake ndipo nthawi zambiri sikaphonya. Chodabwitsa n’choti kamatha kuchita zimenezi ngakhale usiku.

Kanyamaka kamafa anthu akakagwira kuti azikaweta. Mwina zimenezi zimachitika chifukwa choti kamakonda kudya tizilombo togwira kokha komanso sikasangalala anthu akamakaweta. Komabe anthu a ku Philippines amakonda kwambiri kanyama kameneka. Pafupifupi chiwalo chilichonse cha kanyamaka n’chochititsa chidwi.