Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Galamukani!  |  November 2014

Ngalande za Madzi za ku Roma Ankazimanga Mwaukadaulo

Ngalande za Madzi za ku Roma Ankazimanga Mwaukadaulo

NGALANDE za madzi za ku Roma zili m’gulu la zinthu zakale zimene zinkamangidwa mwaukadaulo. Sextus Julius Frontinus, yemwe anali bwanamkubwa komanso mkulu woona za madzi ku Roma, analemba kuti: “Ngalande zathu ndi zazikuluzikulu komanso n’zomangidwa mwaluso ndipo sizingafanane ndi zinthu zopanda ntchito zomwe anthu a ku Greece amanyadira kuti anazimanga mwaluso.” *

N’chifukwa Chiyani Ngalandezi Zinali Zofunika?

Kale mizinda yambiri inkamangidwa pafupi ndi madzi. Ndipo ndi mmene zinalilinso ndi mzinda wa Roma. Poyamba anthu a mumzindawu ankagwiritsa ntchito madzi ochokera mu mtsinje wa Tiber komanso m’mitsinje ndi m’zitsime zimene zinali pafupi ndi mzindawu. Koma kuyambira m’zaka za m’ma 300 B.C.E., anthu a ku Roma anayamba kuchuluka ndipo zimenezi zinapangitsa kuti madzi aziperewera.

Anthu ambiri a mumzindawu analibe mipopi m’nyumba zawo. Chifukwa cha zimenezi, mumzindawu anamangamo mabafa ambiri oti anthu azisambamo. Mabafawa ankakhala aulere koma ena anali olipiritsa. Bafa laulere loyamba kumangidwa analitsegulira mu 19 B.C.E., ndipo madzi ake ankachokera m’ngalande yotchedwa Aqua Virgo. Munthu wina dzina lake Marcus Agrippa, yemwe anali mnzake wapamtima wa Caesar Augustus, anapereka ndalama zambiri zoti zigwiritsidwe ntchito pokulitsa komanso kuyeretsa m’ngalande za madzi za mumzindawu.

Mabafawa ankawagwiritsanso ntchito ngati malo ochezera. M’mabafa ena akuluakulu ankadzalamo maluwa komanso munkakhala laibulale. Madzi a m’mabafawa, omwe ankapatutsidwa kuchokera m’ngalande zikuluzikulu zija, ankayenda nthawi zonse. Akachoka m’mabafamu ankadutsa m’zimbudzi zomwe anazilumikiza kumabafawa ndipo ankakokolola zoipa zonse.

Mmene Ankamangira Komanso Kukonza Ngalandezi

Mbali yaikulu ya ngalandezi, inkakhala pansi pa nthaka ndipo ndi mbali yochepa chabe yomwe inkaonekera kunja. Zimenezi zinkathandiza kuti ngalandezi zisakokoloke ndi madzi. Zinkathandizanso kuti zisathe malo komanso kuti zisamasokoneze kwambiri anthu. Mwachitsanzo, ngalande yotchedwa Aqua Marcia, yomwe inamalizidwa  mu 140 B.C.E., inali yaitali makilomita 92, koma ndi makilomita 11 okha omwe ankaonekera kunja.

Akafuna kumanga ngalande, ankafunika kudziwa kuti madzi a m’ngalandeyo azidzachokera mumtsinje uti. Ankafunikanso kudziwa kumene madzi a mumtsinjewo amalowera. Komanso ankalawa madziwo kuti adziwe ngati ali abwino. Chinanso ankaona ngati anthu akuderalo, omwe anamwapo madziwo, ali ndi thanzi labwino kapena ayi. Akafufuza zonsezi n’kuona kuti angathe kumanga ngalande pamalopo, ankaganizira kukula ndi kutalika kwake komanso pamene idzadutse. Nthawi zambiri akapolo ndi amene ankakumba ngalandezi. Pankatenga nthawi yaitali komanso ndalama zambiri kuti amalize kumanga ngalande imodzi, makamaka ngati pakufunika zipilala zoichirikizira.

Komanso kuti ngalandezi zikhalepo kwa nthawi yaitali, zinkafunika kumakonzedwa komanso kutetezedwa. Pa nthawi ina akuluakulu a mzinda wa Roma analemba ntchito anthu okwana 700 kuti akonze ngalandezi. Akamalemba mapulani a momwe amangire ngalandezi, ankaganiziranso mmene azidzazikonzera zikawonongeka. Mwachitsanzo, ankabowola mabowo m’malo omwe ngalandezi zinadutsa pansi pa nthaka n’cholinga choti zikawonongeka, munthu azitha kulowa n’kukakonza. Ngalande ikawonongeka kwambiri, ankapatutsa madzi n’cholinga choti athe kukonza powonongekapo.

Ngalande za M’tauni

Pofika zaka za m’ma 200 C.E., mumzinda wa Roma munali ngalande zikuluzikulu zokwana 11. Ngalande yoyamba inali yotchedwa Aqua Appia ndipo inamangidwa mu 312 B.C.E. Ngalandeyi inali yaitali makilomita 16 ndipo pafupifupi yonse, inali pansi pa nthaka. Ngalande ina inali yotchedwa Aqua Claudia. Ngalandeyi inali yaitali makilomita 69 ndipo mbali yake ina idakalipo mpaka pano. Mbali ina yokwana makilomita 10 ya ngalandeyi inali ndi zipilala. Zina mwa zipilalazi zinali zazitali mamita 27.

Kodi ngalandezi zinkakhala ndi madzi ochuluka bwanji? Ambiri zedi. Mwachitsanzo, ngalande yotchedwa Aqua Marcia ija, tsiku lililonse inkapititsa madzi mumzinda wa Roma okwana malita 190 miliyoni. Madziwa ankalowa m’mathanki ndipo kenako ankagawikana n’kupita m’mathanki enanso ang’onoang’ono komanso m’malo ena omwe ankakagwiritsidwa ntchito. Anthu ena amanena kuti ngalande za ku Roma zinkakhala zikuluzikulu moti zinali zotheka munthu aliyense wa mumzindawu kugwiritsa ntchito madzi oposa dilamu imodzi patsiku.

Buku lina linanena kuti patapita nthawi, chiwerengero cha anthu a mumzinda wa Roma chinawonjezeka. Koma “mumzindawu munkakhalabe madzi okwanira chifukwa munamangidwanso ngalande zina.” (Roman Aqueducts & Water Supply) Masiku ano anthu akapita ku Asia Minor, France, Spain ndi ku North Africa, amagoma akaona mmene ngalandezi zinkamangidwira.

^ ndime 2 Anthu a ku Roma sanali oyamba kumanga ngalande za madzi. Anthu a ku Siriya, Iguputo, India komanso Perisiya ankamanga ngalande za madzi, Aroma asanayambe kumanga ngalande zoterezi.