United states

Pofuna kuchepetsa ngozi, apolisi ena akumagwiritsa ntchito zipangizo zamakono akafuna kugwira magalimoto a zigawenga komanso a madalaivala ophwanya malamulo a pamsewu. Njira ina imene akuyesa ndi yoti akumaika chipangizo chinachake kutsogolo kwa magalimoto a apolisi. Akaona galimoto imene akufuna kuigwira, amasindikiza kabatani kamene kamachititsa kuti kanthu kenakake katuluke mwamphamvu n’kukamata pagalimoto yothamangitsidwayo. Zikatere, apolisiwo amatha kuona galimotoyo kulikonse kumene ikupita ndipo angathe kuigwira popanda kuithamangitsa pa liwiro loopsa.

India

Kafukufuku wina anasonyeza kuti ku India, pa ola lililonse mzimayi amaphedwa chifukwa cha mikangano yokhudza malowolo amene banja la mkazi limapereka ku banja la mwamuna. Ngakhale kuti boma limaletsa kulandira kapena kupereka malowolo, m’chaka cha 2012 azimayi oposa 8,200 anaphedwa chifukwa choti mwamuna wawo kapena achibale ake ankaona kuti malowolo amene anapatsidwa anali osakwanira.

Switzerland

Anthu ena ofufuza za mbalame anamangirira tizipangizo tinatake ku mbalame zitatu zotchedwa alpine swift zomwe anazipeza pamalo amene zimaswera. Tizipangizoti tinawathandiza kudziwa kuti mbalamezi zinauluka kupita ku Africa ndipo zinauluka kwa masiku oposa 200 osaima paliponse. Poyamba anthu ankakhulupirira kuti nyama za m’madzi zokha ndi zimene zimayenda mtunda wautali chonchi osapumira.

Horn of Africa

Kuyambira mu April 2005 mpaka December 2012, zigawenga zapanyanja zinalanda sitima zapamadzi zokwana 179 m’dera la Horn of Africa. Pa kafukufuku amene a banki yaikulu ya padziko lonse anachita, anapeza kuti zigawengazi zinapatsidwa ndalama zokwana madola 413 miliyoni a ku America kuti zibweze sitimazo.