Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

GALAMUKANI! August 2014 | Kodi Mungatani Kuti Mugwirizanenso Ngati Mwayambana?

Anthu ambiri amafuna atamakhala mwamtendere ndi anthu oyandikana nawo, koma pamakhala zinthu zambiri zimene zimalepheretsa zimenezi. Kodi mungatani kuti mukayambana muzikambirana mwamtendere?

NKHANI YAPACHIKUTO

Kodi Mungatani Kuti Mugwirizanenso Ngati Mwayambana?

Malangizo a m’Baibulo anathandiza anthu ena kuti ayambe kugwirizana.

Zochitika Padzikoli

Nkhani zake: kugwiritsa ntchito matabuleti m’malo mwa mabuku m’sukulu ndi m’mayunivesite, mafuta amene ankawaganizira kuti si oipa kwenikweni omwe achititsa kuti chiwerengero cha anthu omwalira chiwonjezeke komanso anthu a tchalitchi chinachake amene sanawerengepo Baibulo.

MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA

Kodi Mungatani Kuti Musamangopatsa Mwana Wanu Chilichonse Chimene Akufuna?

Mungatani ngati mwakaniza mwana wanu zinazake, iye n’kuyamba kuvuta kapena kuchonderera pofuna kudziwa ngati mwatsimikizadi?

“Onetsetsani Mbalame”

Kodi Yesu ankaphunzitsa mfundo yotani pamene ananena zimenezi?

TIONE ZAKALE

William Whiston

“Anachotsedwa ntchito ndipo anzake anayamba kumusala.” N’chiyani chinachititsa zimenezi?

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Maloto Ochokera kwa Mulungu

Kodi Mulungu amalankhula ndi anthu kudzera m’maloto masiku ano?

KODI ZINANGOCHITIKA ZOKHA?

Mapiko a Gulugufe Ndi Odabwitsa Zedi

Agulugufe ena ali ndi mapiko akuda amene amawathandiza kuti azimva kutentha. Koma palinso chinthu china chimene chimawathandiza

Zina zimene zili pawebusaiti

Kodi Ndithetse Chibwenzichi?—Gawo 1

Mukalowa m’banja, mukuyenera kukhala ndi mnzanuyo kwa moyo wanu wonse. Ndiye ngati mukuona kuti munthu amene muli naye pachibwenzi sangakhale woyenera kumanga naye banja, musangokhala osachitapo chilichonse.

Khadi la M’Baibulo la Farao

Kodi Farao wa ku Iguputo anapulumuka pamene asilikali ake anawonongedwa pa Nyanja Yofiira?