ANTHUFE tikhoza kukumana ndi vuto lalikulu pa nthawi imene sitikuyembekezera. Ndipo zimenezi zikhoza kuchitikira aliyense, ngakhale munthu wolemera.

BAIBULO LIMANENA KUTI:

“Anthu othamanga kwambiri sapambana pampikisano, amphamvu sapambana pankhondo, anzeru sapeza chakudya, omvetsa zinthu nawonso sapeza chuma, ndipo ngakhale odziwa zinthu sakondedwa, chifukwa nthawi yatsoka ndi zinthu zosayembekezereka zimagwera onsewo.”—Mlaliki 9:11.

Popeza aliyense akhoza kukumana ndi vuto lalikulu, funso ndi lakuti: Kodi inuyo zimenezi zitakuchitikirani mungatani? Mwachitsanzo, kodi mungatani:

  • Katundu wanu yense atawonongeka pa ngozi zamwadzidzidzi monga kusefukira kwa madzi?

  • Atakupezani ndi matenda aakulu?

  • Munthu wa m’banja lanu atamwalira?

A Mboni za Yehova, omwe amafalitsa magaziniyi, amakhulupirira kuti Baibulo lingakuthandizeni kudziwa zoyenera kuchita zoterezi zikachitika. Baibulo lingakuthandizeninso kudziwa zimene mungachite kuti mukhale ndi chiyembekezo. (Aroma 15:4) Zitsanzo zotsatirazi zikusonyeza umboni wa zimenezi.