Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Galamukani!  |  May 2014

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

Kum’mwera Chakum’mawa kwa Asia

Mogwirizana ndi zimene bungwe lina loona za nyama zakutchire linanena, pa zaka za pakati pa 1997 ndi 2011, akatswiri ofufuza zinthu anatulukira mitundu yatsopano ya zomera ndi ya nyama yambirimbiri. Nyama zimene anapezazo zikuphatikizapo mtundu winawake wa njoka ya mphiri (Trimeresurus rubeus). Zinthuzi anazipeza m’chigawo cha Greater Mekong. Chigawochi chapangidwa ndi mayiko monga Cambodia, Laos, Myanmar, Thailand, Vietnam ndi dera la Yunnan ku China. Pa zinthu zatsopano zomwe anazitulukira m’chaka cha 2011 chokha, pali mitundu ya zomera 82, mitundu ya nyama zokwawa 21, mitundu ya nsomba 13, mitundu ya nyama za m’gulu la achule 5 komanso mitundu 5 ya nyama zoyamwitsa.

Ulaya

Nyuzipepala ya Moscow Times inanena kuti khalidwe loba anthu lavuta kwambiri “ku Ulaya.” Anthu amagulitsidwa kuti azikawagwiritsa ntchito yochita zachiwerewere, kuwakakamiza kugwira ntchito zakalavulagaga komanso kuti “azikawadula ziwalo n’kumagulitsa, ngakhale kuti malondawa ndi osavomerezeka.” Oba anthu amapezerapo mwayi wochita zimenezi chifukwa cha umphawi, ulova komanso chifukwa cha khalidwe lochitira nkhanza akazi.

New Zealand

Zotsatira za kafukufuku wina zinasonyeza kuti ana ndiponso achinyamata amene amatha nthawi yaitali akuonera TV, “akakula sakonda kucheza ndi anthu.” Zimene apezazi zikugwirizana ndi zomwe anthu ena amanena kuti ana sayenera “kuonera TV kwa maola oposa awiri pa tsiku, ndipo ayenera kuonera mapulogalamu abwino okhaokha.”

Alaska

Pafupifupi “midzi yonse ya ku Alaska” ili m’mbali mwa mitsinje ndipo anthu ambiri a m’midziyi amakumana ndi vuto la kusefukira kwa madzi komanso kukokoloka kwa nthaka. Malipoti akusonyeza kuti pa nthawi ina m’derali kumatentha kwambiri ndipo izi zimachititsa kuti madzi asamaundane. Zimenezi zikuchititsa kuti anthu a m’midziyi azivutika ndi mphepo yamkuntho.

Padziko Lonse

Mkulu wa bungwe lina loona za mphamvu ya magetsi, dzina lake Maria van der Hoeven, ananena kuti, ngakhale kuti mayiko akuwononga ndalama kupanga zipangizo zapamwamba zogwiritsa ntchito mphepo komanso mphamvu ya dzuwa popanga magetsi, “zipangizozi zikumatulutsabe mpweya wowononga chilengedwe ngati mmene zinkakhalira zaka 20 zapitazo.”