Kodi kusinkhasinkha n’kutani?

“Ndidzasinkhasinkha za ntchito zanu zonse, ndipo ndiziganizira zochita zanu.”Salimo 77:12.

ZIMENE ANTHU AMANENA

Kusinkhasinkha kumachitika m’njira zosiyanasiyana, ndipo zimene anthu ambiri amachita posinkhasinkha zinachokera ku zipembedzo za ku Asia zakale. Pa nkhani ya kusinkhasinkhayi, wolemba mbiri wina anati: “Kuti munthu asinkhesinkhe amafunika kuchotsa chilichonse m’maganizo mwake, n’kungotsala nkhani imene akufuna aisinkhesinkhe yokhayo.” Mawu akewa akusonyeza kuti iye amakhulupirira kuti kuchotsa chilichonse m’maganizo posinkhasinkha kumathandiza munthu kukhala ndi mtendere wamumtima, kuona zinthu moyenera komanso kumvetsa bwino zinthu zauzimu.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Baibulo limanena kuti kusinkhasinkha n’kofunika kwambiri. (1 Timoteyo 4:15) Koma kusinkhasinkha kumene Baibulo limalimbikitsa sikutanthauza kuti munthu ayenera kuchotsa chilichonse m’maganizo mwake n’kungotsala ndi nkhani imene akufuna kusinkhasinkhayo. Sikutanthauzanso kumangotchula mobwerezabwereza mawu enaake. Kusinkhasinkha kumene Baibulo limalimbikitsa kumatanthauza kukhala ndi cholinga chofuna kumvetsa nkhani kapena mfundo inayake yofunika, monga makhalidwe a Mulungu, mfundo zake komanso zimene iye analenga. Popemphera kwa Mulungu, munthu wina wokhulupirika ananena kuti: “Ndasinkhasinkha zochita zanu zonse, ndipo ndakhala ndikuganizira ntchito ya manja anu ndi mtima wonse.” (Salimo 143:5) Iye ananenanso kuti: “Ndikakumbukira inu ndili pabedi langa, pa nthawi za ulonda wa usiku ndimasinkhasinkha za inu.”—Salimo 63:6.

 Kodi kusinkhasinkha kungakuthandizeni bwanji?

“Mtima wa munthu wolungama umayamba waganiza usanayankhe.”Miyambo 15:28.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Kusinkhasinkha koyenera kumatithandiza kuti tikhale ndi makhalidwe abwino komanso kuti tikhale odziletsa. Zimenezi zimatithandiza kuti tizilankhula mwanzeru komanso kuti tizichita zinthu zoyenera. (Miyambo 16:23) Choncho kusinkhasinkha kotereku kumathandiza kuti munthu azikhala wosangalala komanso kuti zinthu zizimuyendera bwino. Ponena za munthu amene nthawi zonse amasinkhasinkha za Mulungu, lemba la Salimo 1:3 limati: “Munthu ameneyo adzakhala ngati mtengo wobzalidwa m’mphepete mwa mitsinje ya madzi, umene umabala zipatso m’nyengo yake, umenenso masamba ake safota, ndipo zochita zake zonse zidzamuyendera bwino.”

Kusinkhasinkha kumathandizanso kuti munthu azimvetsa zinthu komanso kuti azizikumbukira. Mwachitsanzo, tikaphunzira zokhudza zinthu zina zimene Mulungu analenga, kapena nkhani inayake ya m’Baibulo, timadziwa mfundo zambiri zochititsa chidwi. Koma tikasinkhasinkha zokhudza mfundo zimenezo, timaona kugwirizana kwa mfundozo komanso mmene zikugwirizanirana ndi zomwe tikudziwa kale. Kalipentala amatha kugwiritsa ntchito zinthu zosiyanasiyana n’kupanga chinthu chokongola. Nafenso pogwiritsa ntchito zinthu zosiyanasiyana zomwe taphunzira, timatha kumvetsa bwino mfundo inayake.

Kodi m’pofunika kuti tizisankha zinthu zoti tisinkhesinkhe?

“Mtima ndi wonyenga kwambiri kuposa china chilichonse ndipo ungathe kuchita china chilichonse choipa. Ndani angaudziwe?”Yeremiya 17:9.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

“Mumtima mwa munthu, mumatuluka maganizo oipa. Mumatuluka zadama, zakuba, zaumbanda, zachigololo, kusirira kwa nsanje, kuchita zoipa, chinyengo, khalidwe lotayirira, diso la kaduka, . . . ndiponso kuchita zinthu mosaganizira ena.” (Maliko 7:21, 22) Mofanana ndi mmene timachitira ndi moto, kuti timayenera kuugwiritsa ntchito mosamala, tiyeneranso kusamala ndi zimene timasinkhasinkha. Apo phuluzi, tingayambe kuganiza zolakwika, ndipo zimenezo zingachititse kuti tipange zinthu zoipa.—Yakobo 1:14, 15.

N’chifukwa chake Baibulo limalimbikitsa kuti tizisinkhasinkha pa ‘zinthu zoona, zofunika kwambiri, zolungama, zoyera, zachikondi, zoyamikirika, khalidwe labwino komanso zotamandika.’ (Afilipi 4:8, 9) Mumtima mwathu mukakhala zinthu ngati zimenezi, timakhala ndi makhalidwe abwino, timalankhula zinthu zabwino komanso timakhala bwino ndi anzathu.—Akolose 4:6.