Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

Arctic

Pulofesa wina wa payunivesite ya Cambridge, ku Britain, dzina lake Peter Wadhams, ananena kuti: “Zaka 30 zapitazo, madzi ambiri m’dera la Arctic ankakhalabe oundana m’nyengo yotentha poyerekeza ndi masiku ano.” Mu 2012, sitima zapamadzi pafupifupi 50 zinatha kudutsa bwinobwino m’malo amene poyamba sizinkatha kudutsa chifukwa cha madzi oundana. Zimenezi zachitika chifukwa cha kusintha kwa nyengo.

Dziko Lonse

Akatswiri ofufuza apeza kuti mkaka wa m’mawere wa azimayi amene angobereka kumene, umakhala ndi mitundu yosiyanasiyana ya mabakiteliya yoposa 700. Akatswiriwa sankaganiza kuti mabakiteliyawa angakhale ambiri chonchi. Iwo akufufuza kuti adziwe mmene mabakiteliyawa amathandizira kugaya chakudya komanso kuteteza thupi la mwana wongobadwa kumeneyo.

Britain

Pa kafukufuku wina amene asayansi a ku Britain anapanga anapeza kuti, madalayivala amene akudwala chimfine amalephera kuganiza mwachangu poyendetsa galimoto poyerekezera ndi amene akuyendetsa galimoto ataledzera.

Democratic Republic of Congo

Ku Africa, anthu akupha njovu zambiri chaka chilichonse pofuna minyanga yake ndipo anthu akuti zimenezi sizinachitikepo kwina kulikonse. Pa nthawi ina, anthu anachita kukwera helikopita n’kuwombera njovu zambiri pamutu nthawi imodzi.

Australia

Asayansi apeza kuti zinthu zambiri zachilengedwe zopezeka m’madzi pamalo otchedwa Great Barrier Reef zakhala zikufa m’zaka 27 zapitazi. Iwo akuona kuti zimenezi zachitika chifukwa cha kuwomba kwa mphepo ya mkuntho, kubwera kwa nsomba zotchedwa starfish komanso kuwonongeka kwa miyala ya pamalowa chifukwa cha kutentha kwa madzi.