Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Galamukani!  |  May 2013

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

United States

Lipoti lina linasonyeza kuti m’zaka 10 zapitazi, apolisi a ku malo okwerera ndege a ku United States, apeza zinthu pafupifupi 50 miliyoni zomwe anthu saloledwa kukwera nazo m’ndege. M’chaka cha 2011 chokha, apolisiwa apeza mfuti zokwana 1,200 m’zikwama za anthu okakwera ndege. Ambiri mwa anthuwa atafunsidwa chifukwa chimene atengera mfuti, anayankha kuti anangoiwala zoti atenga mfuti m’chikwama mwawo.

Brazil

Akuluakulu a zamaphunziro apeza njira yothandiza makolo kuti azidziwa ngati mwana wawo wathawa, wachedwa kapena kujomba kusukulu popanda chifukwa. Iwo akumaika kachipangizo kenakake pa yunifomu ya mwana aliyense wa sukulu. Mwanayo akafika kusukulu, kachipangizoko kamatumiza uthenga kwa makolo ake ndipo akachedwa kusukulu ndi mphindi 20, kachipangizoko kamatumizanso uthenga wowadziwitsa makolowo.

Norway

Dziko la Norway lasiya kuona tchalitchi cha Lutheran ngati tchalitchi champhamvu kwambiri m’dzikolo. Zimenezi zachitika chifukwa chakuti nduna zaboma zinasankha kuti tchalitchi chisamakhale ndi mphamvu kwambiri pankhani ya zochitika za boma.

Czech Republic

Kafukufuku amene anachitika ku Czech anasonyeza kuti, anthu awiri pa atatu alionse ogwira ntchito amaona kuti ayenera kuyankha foni, imelo kapena meseji yokhudza ntchito ngakhale ataweruka. Anthu anayi pa 10 alionse ananena kuti amaona kuti akapanda kuyankha msangamsanga ndiye kuti achita mwano.

India

Ngakhale kuti dziko la India lakhala likupanga zakudya zambiri m’zaka 20 zapitazi komanso kusunga matani okwana 71 miliyoni a mpunga ndi tirigu, anthu ambiri m’dzikolo akuvutikabe ndi njala. Anthu amangodya pafupifupi hafu ya zakudyazi. Zikuoneka kuti zakudya zambiri zimangotayidwa kapena zimagulitsidwa mwachinyengo.