Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Galamukani!  |  May 2013

 KUCHEZA NDI | RACQUEL HALL

Mzimayi Wachiyuda Anafufuzanso Mozama Zimene Ankakhulupirira

Mzimayi Wachiyuda Anafufuzanso Mozama Zimene Ankakhulupirira

Mayi ake a Racquel Hall ndi Myuda ndipo kwawo ndi ku Israel pomwe bambo ake ndi a ku Austria koma anayamba Chiyuda. Agogo ake akuchikazi anali m’gulu lomenyera ufulu wa Ayuda ndipo anasamukira ku Israel mu 1948. Chaka chimenechi ndi chimene dziko la Israel linayamba kudzilamulira lokha. Mtolankhani wa Galamukani! anafunsa Racquel chimene chinamupangitsa kuti aganizirenso za chikhulupiriro chake cha Chiyuda.

Tiuzeni za moyo wanu.

Ndinabadwira ku United States m’chaka cha 1979. Ndili ndi zaka zitatu, ukwati wa mayi ndi bambo anga unatha. Chifukwa cha zimenezi ndinaleredwa ndi mayi anga okha ndipo anandiphunzitsa chikhalidwe cha Chiyuda. Ndinkapitanso kusukulu ya Chiyuda. Ndili ndi zaka 7, tinasamukira ku Israel ndipo tinakhalako kwa chaka chimodzi. Ndinayamba sukulu ina ya konko yomwe amaitcha kibbutz. Kenako tisanamukira ku Mexico.

Ngakhale kuti kudera limene tinkakhala kunalibe masunagoge, ndinkayesetsabe kutsatira chikhalidwe cha Chiyuda. Tsiku la Sabata likakwana, ndinkayatsa makandulo, kuwerenga buku la Chiyuda lotchedwa Torah komanso kupemphera pogwiritsa ntchito buku lamapemphero. Ndikakhala kusukulu, ndinkakonda kuuza anzanga kuti zipembedzo zonse zinachokera m’chipembedzo chathu. Ndinali ndisanawerengepo Chipangano Chatsopano chomwe chimanena zimene Yesu Khristu ankaphunzitsa komanso utumiki wake. Ndipo mayi anga ankandiletsa kuti ndisadzayerekeze kuwerenga Chipangano Chatsopano chifukwa chidzandisokoneza.

Ndiye n’chiyani chinakuchititsani kuwerenga Chipangano Chatsopano?

Nditakwanitsa zaka 17, ndinasamukiranso ku United States kuti ndikamalize maphunziro anga. Ndili kumeneko, mnzanga wina yemwe anali Mkhristu anandiuza kuti sindingakhale wosangalala nditapanda kudziwa za Yesu.

Atandiuza zimenezi ndinamuyankha kuti: “Anthu amene amakhulupirira Yesu ndi osocheretsedwa.”

Anandifunsa kuti: “Kodi iweyo unawerengapo Chipangano Chatsopano?”

Ndinamuyankha kuti: “Ayi.”

Kenako anandiuza kuti: “Ndiye ungaweruze bwanji kuti anthu amene amakhulupirira Yesu ndi osocheretsedwa  pomwe iweyo sudziwa chilichonse chokhudza Yesu?”

Zimene ananenazo zinandipweteka kwambiri chifukwa pamoyo wanga ndimaona kuti munthu amene amafulumira kuweruza anzake iye asakudziwapo chilichonse pa nkhaniyo ndi wopusa. Mwamanyazi ndinatenga Baibulo lake n’kukayamba kuwerenga Chipangano Chatsopano.

Kodi zimene munawerengazo zinakukhudzani bwanji?

Ndinadabwa kwambiri kudziwa kuti amene analemba Chipangano Chatsopano anali Ayuda. Komanso pamene ndinkawerenga, ndinkaona kuti Yesu anali Myuda wachifundo, wodzichepetsa komanso wofunitsitsa kuthandiza anthu osati kuwadyera masuku pamutu. Moti ndinapita ku laibulale kukabwereka mabuku ofotokoza za Yesu. Komabe mabuku onsewo sanandipatse umboni woti Yesu anali Mesiya. Mabuku ena ankafotokoza kuti Yesu ndi Mulungu, zomwe zinkandisokoneza kwambiri. Ndinkadzifunsa kuti ngati Yesu ali Mulungu, ndiye popemphera ankapemphera kwa ndani? Komanso Yesu anafa, pomwe Baibulo limati: “Inu [Mulungu] simufa.” *

Munatani kuti mupeze mayankho a mafunso amenewo?

Ndinkafunitsitsa kudziwa choonadi chifukwa ndinkadziwa kuti choonadi sichidzitsutsa. Ndinapemphera kwa Mulungu mochokera pansi pamtima kwinaku ndikugwetsa misozi. Aka kanali koyamba pamoyo wanga kuti ndipemphere popanda kugwiritsa ntchito buku lamapemphero. Nditangomaliza kupemphera, ndinamva kugogoda pachitseko. Nditatsegula ndinaona kuti anali anthu awiri a Mboni za Yehova. Iwo anandipatsa buku lothandiza pophunzira Baibulo. Nditawerenga bukuli komanso kuphunzira ndi a Mboniwa, ndinazindikira kuti zimene ankakhulupirira zinali zochokera m’Baibulo. Mwachitsanzo, a Mboni za Yehova amakhulupirira kuti Yesu sali mbali ya Utatu koma ndi “Mwana wa Mulungu” * komanso “woyamba wa chilengedwe cha Mulungu.” *

Kenako ndinabwereranso ku Mexico, komwe ndinapitiriza kuphunzira ndi Mboni za Yehova za maulosi osiyanasiyana onena za Mesiya. Ndinadabwa kuona kuti pali maulosi ambiri onena za Mesiya. Koma ndinkakayikirabe. Ndinkadzifunsa kuti: ‘Kodi ndi Yesu yekha amene anachita zinthu mogwirizana ndi maulosi amenewa? Kodi sizingatheke kuti Yesu ankachita zinthu mochenjera kuti azioneke ngati maulosiwo akukwaniritsidwa pa iye?’

N’chiyani chinakupangitsani kukhulupiriradi kuti Yesu ndi Mesiya?

A Mboni za Yehova anandionetsa maulosi osiyanasiyana omwe munthu sangathe kuwakwaniritsa ngakhale atachita zinthu mochenjera. Mwachitsanzo, kutatsala zaka 700 kuti Mesiya abadwe, mneneri Mika analoseleratu kuti Mesiya adzabadwira ku Betelehemu wa ku Yudeya. * Kodi pali munthu amene angasankhe yekha kumene akabadwire? Yesaya ananeneratunso kuti Mesiya adzaphedwa ngati chigawenga koma adzaikidwa m’manda ndi anthu olemera. * Yesu yekha ndi amene anakwaniritsa maulosi onsewa.

Umboni winanso ndi mzera umene Yesu anabadwira. Baibulo linaloseleratu kuti Mesiya adzakhala mbadwa ya Mfumu Davide. * Ayuda akale ankasunga mipukutu ya mibadwo ya makolo. Zikanakhala kuti Yesu sanabadwire mumzera wa Davide, adani ake akanatsutsa zoti Yesu ndi Mesiya. Koma sananene chilichonse chifukwa aliyense ankadziwa kuti Yesu ndi mbadwa ya Davide. Ndipo nthawi ina, khamu la anthu linkamukuwira Yesu kuti “Mwana wa Davide.” *

M’chaka cha 70 C.E., patatha zaka 37 Yesu atamwalira, asilikali achiroma anawononga mzinda wa Yerusalemu ndipo mipukutu ija inawonongedwa ndipo ina inasowa. Choncho kuti anthu adziwedi kuti Yesu ndi Mesiya yemwe anabadwira mumzera wa Davide, anayenera kuonekera chisanafike chaka cha 70 C.E.

Zimenezi zinakukhudzani bwanji?

Pa Deuteronomo 18:18, 19 pali ulosi wonena kuti Mulungu adzapatsa Aisiraeli mneneri ngati Mose. Pa ulosiwu Mulungu ananena kuti: “Amene sadzamvera mawu anga amene iye adzalankhule m’dzina langa, adzayankha mlandu kwa ine.” Nditafufuza mozama m’Baibulo lonse ndinapeza kuti mneneri ameneyu anali Yesu wa ku Nazareti.