Kodi Mulungu ali ndi thupi lotani?

“Mulungu ndiye Mzimu.” —Yohane 4:24.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Baibulo limati Mulungu ndi mzimu. (2 Akorinto 3:17) Chifukwa cha zimenezi iye ndi wapamwamba kuposa ifeyo. Lemba la 1 Timoteyo 1:17 limati: “[Mulungu ndi] Mfumu yamuyaya imene siifa, yosaoneka.” Baibulo limanenanso kuti: “Palibe amene anaonapo Mulungu.”—1 Yohane 4:12.

Mlengi wathu ndi wapamwamba kwambiri moti sitingathe kuganizira n’komwe kuti amaoneka bwanji. Lemba la Yesaya 40:18 limati: “Kodi anthu inu Mulungu mungamuyerekezere ndi ndani, ndipo kodi mungapange chiyani choti mumufanizire nacho?” Ngakhale kumwamba komwe ndi kochititsa mantha sitingakuyerekere n’komwe ndi mphamvu za Mlengi.—Yesaya 40:22, 26.

Komabe angelo amatha kuona Mulungu komanso kulankhulana naye pamasom’pamaso. Kodi zimenezi zimatheka bwanji? Zimatheka chifukwa choti angelo nawonso ndi mizimu ndipo amakhala kumwamba. (1 Mafumu 22:21; Aheberi 1:7) Yesu Khristu ananena za angelowa kuti: “Amaona nkhope ya Atate wanga wakumwamba nthawi zonse.”—Mateyu 18:10.

Kodi Mulungu amapezeka paliponse?

“Muzipemphera motere: ‘Atate wathu wakumwamba, dzina lanu liyeretsedwe.’”—Mateyu 6:9.

 ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Baibulo silinena kuti Mulungu amapezeka paliponse ngati mphamvu inayake yosaoneka. Koma monga mmene mawu a Yesu a pa Mateyu 6:9 ndi pa Mateyu 18:10 amasonyezera, Mulungu ndi munthu ndipo ali ngati Tate. Iye amakhala kumwamba, komwe ndi ‘kumalo ake okhala okhazikika.’—1 Mafumu 8:43.

Yesu atatsala pang’ono kuphedwa ananena kuti: “Ndikuchoka m’dziko kupita kwa Atate.” (Yohane 16:28) Khristu ataphedwa, anauka n’kukhala mzimu ndipo anapita “kumwamba kwenikweniko . . . kuti aonekere pamaso pa Mulungu.”Aheberi 9:24.

N’chifukwa chiyani kudziwa zimenezi kuli kothandiza? Chifukwa choyamba n’chakuti, kumudziwa bwino Mulungu kungatithandize kuti tikhale naye paubwenzi. (Yakobo 4:8) Chachiwiri n’chakuti, kumudziwa bwino Mulungu kumatithandiza kuti tisamalambire milungu yonyenga monga mafano amene anthu ena amalambira. Lemba la 1 Yohane 5:21 limati: “Inu ana okondedwa, pewani mafano.”

Kodi anthu analengedwa bwanji m’chifaniziro cha Mulungu?

“Mulungu analenga munthu m’chifaniziro chake, m’chifaniziro cha Mulungu anam’lenga iye. Anawalenga mwamuna ndi mkazi.”—Genesis 1:27.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Anthufe timatha kusonyeza makhalidwe amene Mulungu ali nawo monga chikondi, chilungamo ndi nzeru. N’chifukwa chake Baibulo limanena kuti: “Muzitsanzira Mulungu, monga ana ake okondedwa, ndipo yendanibe m’chikondi.” —Aefeso 5:1, 2.

Mulungu anatilenganso kuti tizitha kusankha tokha zochita ndipo chifukwa cha zimenezi timatha kusankha zinthu zabwino komanso kusonyeza chikondi kwa anthu ena. (1 Akorinto 13:4-7) Komanso tili ndi luso lopanga zinthu zosiyanasiyana, timasangalala ndi zinthu zokongola komanso timachita chidwi ndi zinthu za m’chilengedwe. Kuwonjezera pamenepa, anthufe mwachibadwa timafuna kudziwa za Mlengi wathu komanso zimene amafuna kuti tizichita.—Mateyu 5:3.

Mmene Baibulo lingakuthandizireni. Tikadziwa zambiri zokhudza Mulungu n’kumayesetsa kumutsanzira, timayamba kuchita zimene iye amafuna. Zimenezi zimatithandiza kuti tizikhala osangalala, tizikhala ndi mtendere wamumtima komanso kuti tizikhala okhutira ndi zimene timachita pa moyo wathu. (Yesaya 48:17, 18) Mulungu amadziwa kuti anthu amakopeka ndi makhalidwe ake ndipo anthu oona mtima amafuna kuyamba kumulambira, zomwe zingawathandize kuti adzapeze moyo wosatha.—Yohane 6:44; 17:3.