Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 ZITHUNZI ZAKALE

Koresi Wamkulu

Koresi Wamkulu

Usiku wa pa October 5/6, mu 539 B.C.E., panachitika zinthu zimene zinkaoneka kuti n’zosatheka mumzinda wa Babulo, womwe unali likulu la ufumu wa Babulo. Usiku umenewu, mzindawu unagonjetsedwa ndi asilikali a Amedi ndi Aperisiya. Mfumu ya Perisiya, dzina lake Koresi yemwenso ankadziwika kuti Koresi Wamkulu, ndi amene anatsogolera asilikaliwa. Kuti Koresi agonjetse mzindawu anachita zinthu mochenjera komanso mwanzeru.

KODI KORESI ANAGONJETSA BWANJI MZINDA WA BABULO?

Buku lina linanena kuti: “Pamene Koresi ankafuna kugonjetsa Babulo, mzindawu unali wotchuka komanso wolimba kwambiri pa mizinda yonse ya ku Middle East mwinanso kuposa mizinda yonse yapadziko lapansi.” (Ancient World Leaders—Cyrus the Great) Mzindawu unali wovuta kuugonjetsa chifukwa mtsinje wa Firate unkadutsa pakati pa mzindawu komanso unali ndi ngalande zozungulira mzinda wonsewo zomwe zinkadzaza ndi madzi nthawi zonse. Mzindawu unalinso ndi mpanda wolimba komanso waukulu kwambiri.

Asilikali a Koresi anapatutsa mtsinje wa Firate chakumpoto kwa mzinda wa Babulo. Zimenezi zinachititsa kuti madziwo aphwe. Kenako asilikaliwo anawoloka mtsinjewo kukafika pa zipata zolowera mumzindawo, zomwe zinali zosatseka, n’kuugonjetsa. Olemba mbiri achigiriki, Herodotus ndi Xenophon analemba kuti anthu a ku Babulo ankaona kuti ndi otetezeka moti usiku umene mzindawo unagonjetsedwa mfumu pamodzi ndi anthu ena ambiri anali pa phwando. (Onani bokosi lakuti  “Dzanja Lalemba Khoma.”) Ndipotu zimene Koresi anachita pogonjetsa mzindawu zinakwaniritsa maulosi ena a m’Baibulo.

Baibulo linalosereratu kuti Koresi adzagonjetsa mzinda wa Babulo

 MAULOSI OCHITITSA CHIDWI

Maulosi okhudza kugonjetsedwa kwa Babulo amene Yesaya analemba ndi ochititsa chidwi kwambiri chifukwa analembedwa zaka 200 zimenezi zisanachitike. Pa nthawiyi n’kuti patatsala zaka pafupifupi 150 kuti Koresi abadwe. Taonani ena a maulosiwa:

  • Kudzabadwa munthu wina dzina lake Koresi amene adzagonjetsa mzinda wa Babulo komanso kumasula Ayuda ku ukapolo.—Yesaya 44:28; 45:1.

  • Mtsinje wa Firate udzaphwa zimene zidzachititsa kuti asilikali a Koresi awoloke.—Yesaya 44:27.

  • Zipata za mzindawo zidzakhala zotsegula.—Yesaya 45:1.

  • Asilikali a ku Babulo adzasiya kumenya nkhondo.—Yeremiya 51:30; Yesaya 13:1, 7.

ANAPULUMUTSIDWA MODABWITSA KWAMBIRI

Chakumayambiriro kwa chaka cha 607 B.C.E., asilikali a Babulo anawononga mzinda wa Yerusalemu ndipo Ayuda amene anapulumuka anawatengera ku ukapolo. Kodi Ayuda anakhala akapolo kwa nthawi yaitali bwanji? Mulungu ananeneratu kuti: “Zaka 70 zimenezo zikadzakwanira, ndidzabwezera mfumu ya Babulo ndi mtundu umenewo . . . ndipo dziko lawolo lidzakhala mabwinja mpaka kalekale.”—Yeremiya 25:12.

Monga taonera kale, Koresi anagonjetsa mzinda wa Babulo mu 539 B.C.E., kenako anamasula Ayuda omwe anali akapolo ku Babulo. Ayudawo anakafika kwawo mu 537 B.C.E. Pa nthawiyi panali patadutsa zaka 70 kuchokera pamene anagwidwa ukapolo. (Ezara 1:1-4) Zitatero, mzinda wa Babulo unakhala “bwinja” ndipo zimenezinso zinakwaniritsa ulosi wina wa m’Baibulo.

N’CHIFUKWA CHIYANI KUDZIWA ZIMENEZI KULI KOFUNIKA?

Taganizirani izi: Baibulo linalosera kuti (1) Ayuda adzakhala ku ukapolo zaka 70, (2) Koresi adzagonjetsa Babulo komanso linaneneratu mmene adzaugonjetsere ndi (3) kuti mzinda wa Babulo udzakhala bwinja. Munthu sakanatha kulosera zimenezi. Choncho n’zoona kuti: “Ulosi sunayambe wanenedwapo mwa kufuna kwa munthu, koma anthu analankhula mawu ochokera kwa Mulungu.” (2 Petulo 1:21) Chimenechi ndi chifukwa chomveka choti tiziwerengera Baibulo.

^ ndime 36 Mawuwa amanena za kulemera kwa ndalama. Kuti mudziwe zambiri werengani mutu 7 m’buku lakuti Samalani Ulosi wa Danieli! lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.