Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Galamukani!  |  January 2013

 KUCHEZA NDI | PAOLA CHIOZZI

Wasayansi Akufotokoza za Chikhulupiriro Chake

Wasayansi Akufotokoza za Chikhulupiriro Chake

Kwa zaka zoposa 20, Dr.  Paola Chiozzi, wakhala akugwira ntchito pa yunivesite ya Ferrara ku Italy, yofufuza mmene maselo a m’thupi amagwirira ntchito. Mtolankhani wa Galamukani! anacheza naye nkhani za sayansi komanso zimene dokotalayu amakhulupirira.

Tiuzeni za moyo wanu.

Bambo anga ankagwira ntchito yokonza nsapato pomwe mayi anga ankagwira ntchito pafamu. Koma ineyo ndinkafuna ndidzakhale wasayansi. Ndinkachita chidwi kwambiri ndi maluwa okongola, mbalame komanso tizilombo touluka. Ndinkaona kuti sikuti zimenezi zinangokhalapo zokha koma kuti pali winawake wanzeru kwambiri amene anazilenga.

Ndiye kuti kuyambira kale mwakhala mukukhulupirira kuti kuli Mulungu?

Ayi, chifukwa kuyambira ndili mwana ndinkakayikira zoti kuli Mulungu. Bambo anga atamwalira ndi matenda a mtima ndinayamba kudzifunsa kuti: ‘N’chifukwa chiyani Mlengi yemwe analenga zinthu zokongola zonsezi amalola kuti anthu azivutika komanso kufa?’

Kodi sayansi inakuthandizani kupeza yankho la funso limenelo?

Ndinganene kuti ayi, chifukwa nditayamba kugwira ntchito imeneyi ndinayamba kuphunzira zambiri zokhudza maselo a m’thupi, omwe anapangidwa kuti pakapita nthawi azifa kuti ena atsopano alowe m’malo mwake. Zimene maselo amachita ndi zofunika kwambiri pa thanzi lathu komabe asayansi angoyamba posachedwapa kuchita chidwi ndi mmene maselo amachitira zimenezi.

Kodi n’chifukwa chiyani zili zofunika kuti maselo a m’thupi mwathu azifa?

Thupi la munthu linapangidwa ndi maselo ambirimbiri. Pakapita nthawi maselo amenewa amafa ndipo amalowedwa m’malo ndi atsopano. Mtundu uliwonse wa selo uli ndi nthawi yake imene umafa. Mwachitsanzo maselo ena amafa pakapita milungu yochepa ndipo ena amafa pakapita zaka zingapo. Payenera kukhala dongosolo linalake lapadera kwambiri kuti maselo amene afa azilowedwa m’malo ndi atsopano.

 Chingachitike n’chiyani ngati zimenezi sizinachitike?

Asayansi ena anapeza kuti ngati maselo sakufa, munthu akhoza kudwala nyamakazi ya m’mafupa kapena khansa. Komanso ngati maselo afa nthawi imene amayenera kufa isanafike, munthu akhoza kudwala matenda ofa ziwalo otchedwa Parkinson kapena matenda a muubongo otchedwa Alzheimer. Kafukufuku amene ndikupanga wandithandiza kupeza njira zochizira matenda amenewa.

Kodi kafukufuku wanuyu wakuthandizani bwanji?

Kunena zoona nditayamba kufufuza za maselo ndinadabwa kwambiri chifukwa zimene maselo amachita zimasonyeza kuti amene anatilenga amafuna kuti tizikhala athanzi. Komabe ndinkadzifunsa kuti, ‘Nangano n’chifukwa chiyani timadwala komanso kufa?’ Ndinayesetsa kufufuza koma sindinapeze yankho la funso limeneli.

Ndiye kuti simunkakayikira kuti pali winawake amene anakonza zoti maselo a m’thupi mwa munthu azifa eti?

Inde. Zimene maselowa amachita n’zovuta kumvetsa koma zimatithandiza kudziwa kuti amene analenga selo ndi wanzeru zakuya. Ndimakhulupirira kuti amene analenga selo ndi Mulungu. Kuti ndidziwe mmene maselo amagwirira ntchito, ndimagwiritsa ntchito maikulosikopu yamphamvu kwambiri. Nthawi zina selo limatha kufa n’kulowedwa m’malo ndi latsopano mu kanthawi kochepa kwambiri. Maselo anakonzedwa kuti azitha kufa okha. Zimenezi zimachitika m’njira yochititsa chidwi kwambiri.

Popeza kuti maselo amafa n’kulowedwa m’malo ndi ena atsopano, ndiye kuti n’zotheka kukhala ndi moyo wosatha

Munali ndi mafunso okhudza Mulungu komanso chifukwa chimene anthu amavutikira, munapeza bwanji mayankho a mafunso amenewa?

Mu 1991, anyamata awiri a Mboni za Yehova anafika kumene ndinkakhala ndipo ndinawafunsa kuti andiuze chifukwa chake anthufe timafa. Anyamatawo anandiwerengera lemba la Aroma 5:12, lomwe limati: ‘Uchimo unalowa m’dziko kudzera mwa munthu mmodzi, ndi imfa kudzera mwa uchimo.’ Lembali limasonyeza kuti zikanakhala kuti Adamu sanachimwe ndiye kuti sakanafa. Nthawi yomweyo ndinazindikira kuti zimenezi zikugwirizana ndi zimene ndinapeza pofufuza mmene maselo amagwirira ntchito. Ineyo ndimaona kuti Mulungu sanatilenge kuti tizifa. Popeza kuti maselo amafa n’kulowedwa m’malo ndi ena atsopano, ndiye kuti n’zotheka kukhala ndi moyo wosatha.

Nangano n’chiyani chinakuthandizani kukhulupirira kuti Baibulo ndi Mawu a Mulungu?

Ndinawerenga lemba la Salimo 139:16 lomwe limati: “Maso anu anandiona pamene ndinali mluza, ndipo ziwalo zanga zonse zinalembedwa m’buku lanu.” Pa ntchito yanga ndinaphunzira kuti zonse zokhudza thupi la munthu zinalembedwadi m’maselo. Ndinkadzifunsa kuti ‘Zinatheka bwanji kuti wamasalimo ameneyu adziwe zimenezi?’ Nditapitiriza kuphunzira Baibulo ndinayamba kuona kuti linalembedwadi ndi Mulungu.

Kodi alipo amene anakuthandizani kuti mulimvetse bwino Baibulo?

Inde. Munthu wina wa Mboni za Yehova anayamba kuphunzira nane Baibulo. Zimenezi zinandithandiza kudziwa chifukwa chake Mulungu amalola kuti anthu azivutika. Ndinadziwanso zimene Baibulo limanena pa nkhani ya cholinga cha Mulungu. Baibulo limanena kuti Mulungu “adzameza imfa kwamuyaya.” (Yesaya 25:8) Mlengi wathu sizidzamuvuta kuchititsa kuti maselo a m’thupi mwathu ayambe kugwira ntchito mwangwiro n’cholinga choti tikhale ndi moyo kwamuyaya.

Kodi mwathandiza bwanji ena pogwiritsa ntchito zimene munaphunzira m’Baibulo?

Ndinakhala wa Mboni za Yehova mu 1995, ndipo kuyambira nthawi imeneyo ndakhala ndikuuza anthu ena zimene ndimaphunzira m’Baibulo. Mwachitsanzo mnzanga wina, yemwe kutchalitchi kwawo amaphunzitsa kuti Mulungu sakhululukira anthu amene achita kudzipha, anakhumudwa kwambiri mchimwene wake atadzipha. Koma ndinamuonetsa lonjezo la m’Baibulo lakuti akufa adzauka. (Yohane 5:28, 29) Anasangalala kwambiri kudziwa kuti Mlengi wathu amatikonda. Ndimaona kuti ndikamauza anthu choonadi cha m’Baibulo ndimakhala wosangalala kwambiri kuposa mmene ndimachitira ndikamagwira ntchito yanga.