Kamtsikana kena kataona utsi ukutuluka m’fakitale inayake n’kumaoneka ngati mitambo kankaganiza kuti ntchito ya fakitaleyo ndi kupanga mitambo. Kusamvetsa kwa kamtsikanako kungakhale koseketsa. Komatu kusamvetsa zinthu zofunika kwambiri kungatibweretsere mavuto aakulu. Mwachitsanzo, tikhoza kudwala kwambiri ngati sitinamvetse bwino malangizo a mankhwala amene tapatsidwa.

Koma chinthu choopsa kwambiri ndi kusamvetsa Mawu a Mulungu. Mwachitsanzo, anthu ena atalephera kumvetsa zimene Yesu ankaphunzitsa sanafunenso kuphunzira chilichonse kuchokera kwa iye. (Yohane 6:48-68) Apatu anataya mwayi waukulu kwambiri.

Kodi mumawerenga Baibulo kuti lizikuthandizani pa moyo wanu? Ngati ndi choncho, mukuchita bwino kwambiri. Koma kodi pangakhale zinthu zina zimene simuzimvetsa? Pali anthu ambiri amene samvetsa mfundo zina za m’Baibulo. Tiyeni tione mfundo zitatu za m’Baibulo zomwe ambiri sazimvetsa.

  • Anthu ena samvetsa lamulo la m’Baibulo lakuti, ‘tiziopa Mulungu woona.’ Iwo amaganiza kuti lamuloli limatanthauza kuti tizichita mantha kwambiri ndi Mulungu. (Mlaliki 12:13) Koma si zimene Mulungu amafuna. Iye anati: “Usachite mantha, pakuti ndili nawe. Usayang’ane uku ndi uku mwamantha, pakuti ine ndine Mulungu wako. Ndikulimbitsa. Ndithu ndikuthandiza.” (Yesaya 41:10) Choncho kuopa Mulungu sikutanthauza kuchita naye mantha koma kumulemekeza kwambiri.

  • Kodi dziko lapansi lidzawonongedwa ndi moto?

    Anthu ena samvetsa mawu a m’Baibulo akuti: “Chilichonse chili ndi nthawi yake . . . Pali nthawi yobadwa ndi nthawi ya kufa.” Iwo amaganiza kuti Mulungu anasankhiratu nthawi imene munthu aliyense adzafe. (Mlaliki 3:1, 2) Koma lembali likungofotokoza zimene zimachitika pa moyo wa munthu ndipo limasonyeza kuti aliyense amafa. Baibulo limasonyezanso kuti zimene timachita pa moyo wathu zingachititse kuti tikhale ndi moyo wautali kapena ayi. Mwachitsanzo, limati: “Kuopa Yehova kudzawonjezera masiku.” (Miyambo 10:27; Salimo 90:10; Yesaya 55:3) Mawuwa ndi oona chifukwa munthu akamalemekeza Mawu a Mulungu amapewa zinthu zomwe zingawononge moyo wake, monga kuledzera kapena chiwerewere.—1 Akorinto 6:9, 10.

  • Anthu ena akamawerenga m’Baibulo kuti kumwamba ndiponso dziko lapansi Mulungu ‘wazisungira moto,’ amaganiza kuti Mulunguyo adzawononga dziko lenilenili. (2 Petulo 3:7) Koma iye analonjeza kuti sadzalola kuti dziko lapansili liwonongedwe. Mulungu ‘anakhazikitsa dziko lapansi pamaziko olimba ndipo silidzagwedezeka mpaka kalekale.’ (Salimo 104:5; Yesaya 45:18) Choncho sikuti adzawononga dziko lenilenili koma adzawononga anthu onse oipa komanso zinthu zonse zomwe zimachititsa mavuto. Zidzakhala ngati wazitentha ndi moto chifukwa sizidzakhalaponso. Komanso kumwamba kwenikweni kungaphatikizepo kuthambo ndiponso kumene Mulungu amakhala. Ndipotu zimenezi sizingawonongedwe.

N’CHIFUKWA CHIYANI NTHAWI ZINA ANTHU SALIMVETSA BAIBULO?

Monga mwaonera kale, nthawi zambiri anthu samvetsa zimene amawerenga m’Baibulo. Koma kodi n’chifukwa chiyani Mulungu amalola zimenezi? Anthu ena angadzifunse kuti: ‘N’chifukwa chiyani Mulungu yemwe ndi wanzeru kwambiri komanso amadziwa zonse, sanatipatse buku lomveka bwino loti aliyense angathe kulimvetsa mosavuta?’ Tiyeni tione zifukwa zitatu zimene zimachititsa kuti anthu ena asamalimvetse Baibulo.

  1. Baibulo linalembedwa m’njira yoti anthu odzichepetsa okha komanso ofunadi kuphunzira azilimvetsa. Yesu anauza Atate wake kuti: “Atate ndikukutamandani pamaso pa onse, inu Ambuye  wakumwamba ndi dziko lapansi, chifukwa zinthu izi mwazibisa kwa anzeru ndi ozama m’maphunziro, koma mwaziulula kwa tiana.” (Luka 10:21) Baibulo linalembedwa m’njira yoti anthu amene ali ndi maganizo oyenera okha azilimvetsa. Anthu onyada, mwina chifukwa chodziona kuti ndi anzeru komanso ophunzira kwambiri, amavutika kulimvetsa. Koma anthu amene amakhala ndi maganizo ofanana ndi a “tiana,” tomwe timakhala todzichepetsa komanso tofunitsitsa kuphunzira, Mulungu amawathandiza kumvetsa bwino uthenga wa m’Baibulo. Izi zikusonyeza kuti Mulungu analemba Baibulo mwaluso kwambiri.

  2. Anthu amene amapempha Mulungu kuti awathandize ndi amene angamvetse Baibulo. Yesu anasonyeza kuti anthu angafunikire kuthandizidwa kuti amvetse zimene iye ankaphunzitsa. Koma kodi angathandizidwe bwanji? Yesu anati: “Mthandizi, amene ndi mzimu woyera, amene Atate wanga adzatumiza m’dzina langa, adzakuphunzitsani zinthu zonse.” (Yohane 14:26) Choncho Mulungu amagwiritsa ntchito mzimu woyera kuti athandize anthu kumvetsa zimene akuwerenga m’Baibulo. Koma Mulungu sapereka mzimu wake kwa anthu amene samudalira ndipo n’chifukwa chake anthuwo sangamvetse zimene akuwerenga. Mzimu woyera umalimbikitsanso Akhristu amene amadziwa zambiri kuti azithandiza anthu amene amafunitsitsa kumvetsa mfundo za m’Baibulo.—Machitidwe 8:26-35.

  3. Nkhani zina za m’Baibulo zili ndi nthawi yake yoyenera imene anthu angazimvetse. Mwachitsanzo, mneneri Danieli anauzidwa kuti alembe uthenga wokhudza nthawi ya mapeto. Mngelo wina anamuuza kuti: “Danieli, sunga mawuwa mwachinsinsi ndipo utseke ndi kumata bukuli kufikira nthawi yamapeto.” Anthu ambiri ankawerenga buku la Danieli koma sankalimvetsa. Ndipotu nayenso Danieli sankamvetsa zinthu zina ngakhale kuti analemba yekha. Iye ananena modzichepetsa kuti: “Ndinamva zimene ananenazo, koma sindinadziwe tanthauzo lake.” Koma patapita nthawi, anthu anayamba kumvetsa ulosi wa Danieli pa nthawi imene Mulungu anaona kuti ndi yoyenera. Mngeloyo anafotokozanso kuti: “Pita Danieli, pakuti mawuwa asungidwa mwachinsinsi ndipo atsekedwa ndi kumatidwa kufikira nthawi yamapeto.” Koma kodi ndi anthu ati amene akanamvetsa mawuwa? Mngeloyo ananena kuti: “Palibe munthu woipa aliyense amene adzamvetsetse mawu amenewa, koma anthu ozindikira adzawamvetsetsa.” (Danieli 12:4, 8-10) Choncho taona kuti Mulungu amathandiza anthu kuti amvetse nkhani zina za m’Baibulo pa nthawi imene iyeyo waona kuti ndi yoyenera.

Nthawi zina nawonso a Mboni za Yehova samvetsa bwino nkhani zina za m’Baibulo. Koma nthawi ikakwana yoti Mulungu awathandize kumvetsa nkhanizo, iwo amakhala okonzeka kusintha. A Mboniwa amaona kuti akutsanzira atumwi a Khristu, omwe ankasintha maganizo awo modzichepetsa Yesu akawathandiza.—Machitidwe 1:6, 7.

Kusamvetsa zinthu kwa kamtsikana kamene tinakatchula kaja si nkhani yaikulu. Koma kusamvetsa bwino zimene Baibulo limaphunzitsa ndi nkhani yaikulu kwambiri. Tikutero chifukwa chakuti uthenga wake ndi wofunika kwambiri. Choncho si bwino kumaona kuti mungamvetse panokha zimene mukuwerenga m’Baibulo. Mungachite bwino kufufuza anthu omwe angakuthandizeni kumvetsa zimene mukuwerenga. Pezani anthu amene ndi odzichepetsa, amene amadalira mzimu woyera wa Mulungu ndiponso amene amakhulupirira kuti tikukhala m’nthawi imene Mulungu akufuna kuti tizimvetsa bwino uthenga wa m’Baibulo. Mukhoza kulankhula ndi a Mboni za Yehova kapena kuwerenga nkhani zothandiza kuphunzira Baibulo zomwe zili pawebusaiti ya jw.org. Baibulo limalonjeza kuti: “Ukaitana kumvetsa zinthu . . . udzamudziwadi Mulungu.”—Miyambo 2:3-5.