Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo

Kalata Yochokera ku Bungwe Lolamulira

Kalata Yochokera ku Bungwe Lolamulira

Okondedwa Abale ndi Alongo Athu:

Popeza timalambira Yehova, timakonda kwambiri Baibulo chifukwa ndi Mawu ake. Timadziwa kuti nkhani zake n’zolondola komanso mfundo zake ndi zothandiza. Tikudziwanso kuti Yehova watipatsa Baibulo chifukwa chakuti amatikonda. (Salimo 119:105; Luka 1:3; 1 Yohane 4:19) Timafunitsitsanso kuthandiza ena kuti adziwe mfundo za choonadi zimene zili m’Mawu a Mulungu. Choncho ndife osangalala kutulutsa bukuli la mutu wakuti, Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo. Ndiyeno tikufuna tingofotokoza pang’ono za bukuli.

Bukuli kwenikweni talilemba kuti lithandize ana. Koma ngakhale zili choncho, ndi lothandizanso kwa akuluakulu amene akufuna kulidziwa bwino Baibulo. Popeza Baibulo ndi buku la aliyense, kuphunzira nkhani za m’bukuli kungatithandize kuti tizikhala osangalala.

Bukuli likufotokoza nkhani za m’Baibulo kuyambira pamene anthu analengedwa. Tayesetsa kufotokoza nkhanizi m’njira yosavuta kumva komanso motsatira nthawi imene zinthuzo zinachitika.

Koma sikuti bukuli likungofotokoza nkhani za m’Baibulo. Talemba nkhanizi komanso kukonza zithunzi zake m’njira yoti munthu akamawerenga azikhala ngati akuona zimene zinkachitika komanso kumva mmene anthuwo ankamvera.

Bukuli litithandiza kuona kuti Baibulo limafotokoza za anthu amene anamvera Yehova ndi amene sanamumvere. Ndipo litithandiza kuona zimene tingaphunzire kwa anthuwo. (Aroma 15:4; 1 Akorinto 10:6) Bukuli lili ndi zigawo 14. Kumayambiriro kwa  chigawo chilichonse kuli mawu ofotokoza zimene tingaphunzire m’chigawocho.

Ngati ndinu makolo mungawerenge ndi ana anu mutu uliwonse n’kukambirana zithunzi zake. Kenako mungawerengenso limodzi mavesi a m’Baibulo amene pachokera nkhaniyo. Mukatero, mungathandize anawo kuona kugwirizana pakati pa zimene mwawerenga m’Baibulo ndi zimene mwaphunzira m’nkhaniyo. Njira imeneyi ingathandizenso ngati mukukambirana ndi munthu wamkulu amene akufuna kulidziwa bwino Baibulo.

Sitikukayikira kuti bukuli lithandiza ana ndi akulu omwe kuti aphunzire mfundo za m’Mawu a Mulungu n’kumazigwiritsa ntchito pa moyo wawo. Izi zingathandize kuti nawonso akhale m’banja la Mulungu n’kumamulambira.

Ndife abale anu,

Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova