Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo

 MUTU 55

Mngelo wa Yehova anateteza Hezekiya

Mngelo wa Yehova anateteza Hezekiya

Senakeribu yemwe anali mfumu ya Asuri anagonjetsa ufumu wa Isiraeli wa mafuko 10. Ndiyeno ankafunanso kugonjetsa ufumu wa Yuda wa mafuko awiri. Iye anayamba kugonjetsa mizinda ya Yuda. Mzinda umene ankaufunitsitsa unali wa Yerusalemu. Koma Senakeribu sankadziwa kuti Yehova ankateteza mzindawu.

Hezekiya, yemwe anali mfumu ya Yuda, anapatsa Senakeribu ndalama zambiri kuti asalande mzinda wa Yerusalemu. Senakeribu analandira ndalamazo, komabe anatumiza gulu la asilikali ake ku Yerusalemu. Anthu a mumzindawo atamva kuti asilikaliwo atsala pang’ono kufika, anachita mantha kwambiri. Koma Hezekiya anawauza kuti: ‘Musaope. N’zoona kuti Asuri ndi amphamvu, komabe Yehova atithandiza.’

Senakeribu anatumiza Rabisake kuti apite ku Yerusalemu kukalankhula ndi Ayuda. Rabisake anaima panja pa mzindawu n’kukuwa kuti: ‘Inutu Hezekiya asakupusitseni. Yehova sangakuthandizeni. Palibe mulungu amene angatilepheretse kukugonjetsani!’

Hezekiya anapempha Yehova kuti awathandize kudziwa zoyenera kuchita. Yehova anayankha kuti: ‘Musaope zimene Rabisake akunenazo. Senakeribu sangagonjetse Yerusalemu.’ Kenako Hezekiya analandira makalata ochokera kwa Senakeribu. M’makalatawo munali mawu akuti: ‘Tangonenani kuti mwagonja. Yehovatu sakupulumutsani.’ Zitatero Hezekiya anapemphera kuti: ‘Chonde Yehova tipulumutseni kuti aliyense adziwe zoti inu ndinu Mulungu woona.’ Yehova anamuuza kuti: ‘Mfumu ya Asuri sifika ku Yerusalemu. Ineyo nditeteza mzinda wangawu.’

Senakeribu ankaona kuti agonjetsa Yerusalemu basi. Koma usiku wina, Yehova anatumiza mngelo kumalo amene asilikali a Asuri ankagona. Mngeloyo anapha asilikali 185,000. Asilikali onse amphamvu a Senakeribu anathera pomwepo. Zitatero Senakeribu anadziwa kuti wagonja ndipo  anangouyamba ulendo wobwerera kwawo. Apa ndiye kuti Yehova anakwaniritsa lonjezo lake loti adzateteza Hezekiya komanso mzinda wa Yerusalemu. Kodi iweyo ukanakhala ku Yerusalemu, ukanadalira Yehova?

“Mngelo wa Yehova amamanga msasa mozungulira onse oopa Mulungu, ndipo amawapulumutsa.”​—Salimo 34:7